Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nilimbitseni Mtima

Nilimbitseni Mtima

(2 Mafumu 6:16)

Daunilodi:

  1. 1. Navutika mtima—

    Nasoŵa cocita.

    Olo zinthu zinivute;

    Mumanithandiza.

    Moyo ungavute,

    Koma nimadziŵa:

    Ndimwe wokhulupilika;

    Mudzaniteteza.

    (KOLASI)

    Yehova, nithandizeni

    Kuti niziona.

    Tilidi ambili kuposa

    Olimbana nafe.

    Conde, n’thandizeni;

    Kuti nipilile.

    Nilimbitseni mtima,

    Simungalephele.

  2. 2. Ndine cabe munthu.

    Nimacita mantha.

    Ndimwe pothaŵila panga;

    Simumalephela.

    Munipatse mphamvu,

    Kuti nisayope.

    Ine nidzapililabe—

    Kufikila imfa.

    (KOLASI)

    Yehova, nithandizeni

    Kuti niziona.

    Tilidi ambili kuposa

    Olimbana nafe.

    Conde, n’thandizeni;

    Kuti nipilile.

    Nilimbitseni mtima,

    Simungalephele.

    (KOLASI)

    Yehova, nithandizeni

    Kuti niziona.

    Tilidi ambili kuposa

    Olimbana nafe.

    Conde, n’thandizeni;

    Kuti nipilile.

    Nilimbitseni mtima,

    Simungalephele.

    Nilimbitseni mtima,

    Simungalephele.