Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nakupatsani Mphatso Yabwino Koposa

Nakupatsani Mphatso Yabwino Koposa

Daunilodi:

  1. 1. Munatipatsa

    Mwana mwamuna wabwino.

    Tam’phunzitsa

    Tam’kulitsa tikondwela tikaona,

    Zosankha zake zabwino.

    (KOLASI)

    Timamukonda koma timadziŵa citetezo cazoona,

    Cili m’manja anu M’lungu,

    Ndipo sicizatha.

    Zaka zam’tsogolo mtima udzakhazikika,

    Tipeleka kuli imwe tipeleka,

    Mwana wathu.

  2. 2. Munatipatsa

    Mwana wamkazi wabwino mumisozi,

    Mucimwemwe, tam’kulitsa ndipo akhala

    Mkazi timanyadila

    (KOLASI)

    Timamukonda koma timadziŵa citetezo cazoona,

    Cili m’manja anu M’lungu,

    Ndipo sicizatha.

    Zaka zam’tsogolo mtima udzakhazikika

    Tipeleka kuli imwe tipeleka,

    Mwana wathu.