Ndasangalala Kuti Sindinagonje
Pangani Dawunilodi:
1. Pamakhala mayesero
Ena tsiku ndi tsiku—tsiku ndii tsiku.
Sindingadziwiretudi,
Koma mulimonsemo, ndingapeze njira.
Ndikalimba ndidzapirira.
Ndizikonzekereratu—
Zochita ndi zonena
Chiyeso chikafika.
Pena kwa ine n’zovuta.
Ndizipemphera kwa M’lungu.
(KOLASI)
Nipempha n’sagonje
Ndipirire chiyeso.
Ndipempha n’sagonje
Ndikhulupirikebe.
2. Ndikozanso kukopeka
N’kucheza ndi oipa—zingachitike.
Pena ndingaone ena
Akuchita zoipa—zinthu zoipa.
Kutengekanso maganizo
Ndi anthu osayenera.
M’pomwe ndimakumbuka
Ndisachite zoipa.
Ndidzakhulupirikabe
Palibe choti ndiope.
(KOLASI)
Ndasangalalatu,
Kuti sindinagonje.
Ndasangalalatu,
Ndakhulupirika.