Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amatithandiza Nthawi Zonse

Yehova Amatithandiza Nthawi Zonse

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Ndinkachitadi mantha,

    Ndinali wosatetezeka.

    Ndinkatsutsidwa kwambiri.

    Koma ndalimba mtima.

    Iye wati ndim’dalire,

    Ndithu anditeteza.

    Amandikondadi.

    (KOLASI)

    Wan’thandiza

    Kulimba n’tafooka,

    Kulimba n’tatha nzeru,

    Kulimba m’mayesero,

    Kupirira ndithu,

    Kulimba m’mavuto,

    Kum’dalira nthawi zonse.

    Yehova ’mandithandiza.

    Wan’dziwitsa

    Njira zake

    Zomwe n’zolungama.

    An’thandiza,

    Kuti ndimvetse

    N’kudziperekabe.

  2. 2. Sulitu wekha.

    Ngakhale unachoka,

    Ali nawe.

    Akuthandiza

    Kuti upirirebe ndithu

    N’kukupatsa nzeru.

    (KOLASI)

    Akuthandiza

    Kulimba ukafo’ka,

    Kulimba zikavuta,

    Kulimba m’mayesero,

    Kupirira ndithu,

    Kulimba m’mavuto,

    Kum’dalira nthawi zonse.

    Yehova ’matithandiza​—

    M’zonse, m’zonse.

    Yehova ’matithandiza.

    Tadziwatu ndithu

    Njira zake

    Zomwe n’zolungama.

    Yehova ’matithandiza

    Athandiza,

    Kuti timvetse

    N’kudziperekabe.

    (KOLASI)

    Ndinatha

    Kulimba n’tafooka,

    Kulimba n’tatha nzeru,

    Kulimba m’mayesero,

    Kupirira ndithu,

    Kulimba m’mavuto,

    Kum’dalira nthawi zonse.

    Yehova ’matithandiza​—

    M’zonse, m’zonse.

    Yehova ’matithandiza​—

    M’zonse, m’zonse

    Yehova ’matithandiza.