Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Yehova Ali Na Ise Nthawi Zonse

Yehova Ali Na Ise Nthawi Zonse

Daunilodi:

  1. 1. Ninalidi na mantha

    Opanda malo othaŵila

    N’nalibe onithandiza,

    Ninavutitsidwadi.

    M’lungu ananiteteza,

    Ananipatsa mphamvu

    Iye anikonda.

    (KOLASI)

    Ananilimbitsa

    Nonipatsa mphamvu

    Pa Nthawi ya mavuto,

    Na pa nthawi yolila.

    Mphamvu yopilila

    Kuti nisayope

    Mphamvu kuti nim’dalile

    Yehova ali na ine.

    Nthawi zonse

    Kulikonse

    Amanithandiza.

    Nthawi zonse

    Anikumbutsa

    Kuti anikonda.

  2. 2. Sitili tekha

    Olo zinthu zivute

    Ali na’se

    Tidzapambana

    Ngati tilibe mphamvu

    Adzatilimbikitsa.

    (KOLASI)

    Adzatilimbitsa

    Notipatsa mphamvu

    Pa nthawi ya mavuto

    Na pa nthawi yolila.

    Mphamvu yopilila

    Kuti tisayope.

    Mphamvu kuti tim’dalile.

    Yehova ali na ise

    Nthawi zonse.

    Yehova ali na ise.

    Ayenda na ise

    Kulikonse

    Adzatithandiza.

    Yehova ali na ine

    Nthawi zonse

    Atikumbutsa

    Kuti atikonda.

    (KOLASI)

    Ananilimbitsa

    Nonipatsa mphamvu

    Pa nthawi ya mavuto

    Na pa nthawi yolila.

    Mphamvu yopilila

    Kuti nisayope

    Mphamvu kuti tim’dalile.

    Yehova ali na ise

    Nthawi zonse

    Yehova ali na ise.

    Nthawi zonse

    Yehova ali na ise.