Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Dziko Latsopano Likubwelalo

Dziko Latsopano Likubwelalo

Daunilodi:

  1. 1. Mu maganizo yelekeza.

    Patsogolo ana akuseŵela

    Na kusekelela.

    Mu dziko mulibe zotiyofya.

    Amene asamalila dziko

    Ni anthu omvela atate wathu

    Ndipo kwa nthawi zonse,

    Kuli mtendele wosaneneka.

    Mwana wa M’lungu

    Adzatilamulila

    M’dziko latsopano.

    (KOLASI)

    Ciyembekezo ici

    N’cimene Cimatilimbitsa

    Citithandiza kuganizila

    Zinthu zam’tsogolo,

    M’dziko likubwela.

  2. 2. Ganizilani za malowa

    M’mbali mwa mapili na m’mbali mwa nyanja

    Ni malo abwino.

    Musanangene m’nyumba mwanu

    Muona okondedwa

    Na misozi m’maso mwanu

    Wangoukitsidwa

    Mwa cikondi mwam’kumbatila.

    Ngakhale imfa

    Siidzakhalako

    M’dziko likubwela.

    (KOLASI)

    Ciyembekezo ici

    N’cimene Cimatilimbitsa.

    Citithandiza kuganizila

    Zinthu zam’tsogolo,

    M’dziko likubwela.

    (BILIJI)

    Mawu onse a M’lungu

    Adzakwanilitsidwa ndithu

    Yehova afuna kuti

    Akhutilitse Cilengedwe conse..

    (KOLASI)

    Ciyembekezo ici

    N’cimene Cimatilimbitsa

    Citithandiza kuganizila

    Zinthu zam’tsogolo,

    M’dziko likubwela.

    M’dziko likubwela.

    M’dziko likubwela.

    M’dziko likubwela..