Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Khululuka na Mtima Wonse

Khululuka na Mtima Wonse

Daunilodi:

  1. 1. Ninasunga cinthu kukhosi

    Koma cinisautsa mtima.

    Cinivuta kuiŵala.

    Nifunika nikhululuke

    Koma sindine ninalakwitsa,

    Ndipo cimaniŵaŵa ngako.

    (MWANA WA KOLASI)

    Koma nipemphele

    Kwa Yehova.

    Adziŵadi zonse zinacitika,

    Ndipo adzanithandiza

    Kukhululuka.

    (KOLASI)

    Siningakwanitse nekha

    Conde, M’lungu n’thandizeni

    Nikhululukedi.

    Nipatseni mphamvu

    Nikhululuke na mtima wonse

    M’lungu nipempha thandizo

    Nikhululuke na mtima wonse.

  2. 2. Niyesetsa kuiŵalako

    Pena zibwela mumtima,

    Nifuna kuiŵala zonse.

    Nimadziŵa, kukhululuka

    Koona nikuiŵala zonse;

    Kusasunga ca ku khosi.

    (MWANA WA KOLASI)

    Koma nipemphele

    Kwa Yehova.

    Adziŵadi zonse zinacitika,

    Ndipo adzanithandiza

    Kukhululuka.

    (KOLASI)

    Siningakwanitse nekha

    Conde, M’lungu n’thandizeni

    Nikhululukedi.

    Nipatseni mphamvu

    Nikhululuke na mtima wonse

    M’lungu nipempha thandizo

    Nikhululuke na mtima wonse.

    Mtima wonse.

    N‘khululuke.

    N’khululuke.