Sitisiya
Pangani Dawunilodi:
1. Nditamva cho’nadi koyamba
Za Yehova ndi za paradaiso,
N’nayamba kuzikonda kwambiri.
M’dzikoli zosokoneza n’zambiri.
(KUKONZEKERA KOLASI)
Sindingasiye,
N’zichita zoyenera.
(KOLASI)
Ndikulimbitsa chikhulupiriro.
Sindidzabwerera m’mbuyo.
Mawu ake anditsogolere.
Ndikupempha ndipirire.
Ndikhale wolimba, sindisiya.
2. Tikhozatu kusankha mwanzeru
Polimbitsa chikhulupiriro.
Dzikoli likufuna tisinthe
Ndikumachita zomwe tikufuna.
(KUKONZEKERA KOLASI)
Posachedwatu,
Dziko likupita.
(KOLASI)
Tikulimbitsa chikhulupiriro.
Sitidzabwerera m’mbuyo.
Mawu ake atitsogolere.
Tikupempha tipirire.
Tikhale olimba, sitisiya.
(KOLASI)
Tikulimbitsa chikhulupiriro.
Sitidzabwerera m’mbuyo.
Mawu ake atitsogolere.
Tikupempha tipirire.
Tikhale olimba, sitisiya.
Sitisiya.
Sitisiya.