Chimwemwe Chosatha
Pangani Dawunilodi:
1. M’mwamba mwadzaza nyenyezi
Zikuwalatu.
Masananso Kukongola
M’matikondadi.
M’nalenga nyanja ndi mtunda,
Ndi zonse timaonazi
Munamva bwino.
(KOLASI)
Tonse tikusangalala,
N’za chipulumutso chathu,
Ndi dziko latsopano.
Kukondedwa ndi ’nu M’lungu
Ndi mwayidi wapadera.
Ndinutu m’matipatsa
Chimwemwe chosatha.
2. Tili n’zonse zofunika
Zosangalatsa
Munatilenga mwaluso,
Timamva bwino.
Munatipatsatu mtima,
Wofuna kukhala moyo
Mpakatu kale.
(KOLASI)
Tonse tikusangalala,
N’za chipulumutso chathu,
Ndi dziko latsopano.
Kukondedwa ndi ’nu M’lungu
Ndi mwayidi wapadera.
Ndinutu m’matipatsa
Chimwemwe chosatha.
(VESI LOKOMETSERA)
Popandatu Yesu
Chimwemwe panalibe.
Iyetu anatifera
Ndiye chimwemwe n’chosatha.
(KOLASI)
Tonse tikusangalala,
N’za chipulumutso chathu,
Ndi dziko latsopano.
Kukondedwa ndi ’nu M’lungu
Ndi mwayidi wapadera.
Ndinutu m’matipatsa
Chimwemwe chosatha.
(KOLASI)
Tonse tikusangalala,
N’za chipulumutso chathu,
Ndi dziko latsopano.
Kukondedwa ndi ’nu M’lungu
Ndi mwayidi wapadera.
Ndinutu m’matipatsa
Chimwemwe chosatha.
(Onaninso Sal. 37:4; 1 Akor. 15:28.)