Muziteteza Maganizo Anu

Muziteteza Maganizo Anu

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Ndimafuna n’zimumvera,

    Komatu ndimavutika—

    Ndikumaona ngati

    Ndikuchita zochepa.

    Usiku ndimapemphera,

    Paja ndi zomwe munandiuza.

    N’kayamba kuda nkhawa,

    Yehova paja munati

    (KOLASI)

    Ndiziteteza mtima wangawu,

    N’ganizire zabwinodi.

    N’saganizire zofo’ketsa.

    Ndidzapezatu mtendere ndithu.

  2. 2. Ndimafuna n’zimumvera,

    Koma ndimatopa ndi nkhawa.

    Pena ndimamva ngati

    M’lungu sangandikonde.

    Kukacha ndikatuluka

    Ndimauza ena za tsogolo.

    Nkhawa zanga n’kuchepa.

    Yehova muman’teteza.

    (KOLASI)

    Ndiziteteza mtima wangawu,

    N’ganizire zabwinodi.

    N’saganizire zofo’ketsa.

    Ndidzapezatu mtendere ndithu.

    Mtenderedi.

    (VESI LOKOMETSERA)

    Ndizichotsa maganizo

    Omwetu ndi ofo’ketsa.

    N’sade nkhawa, n’sakaikire

    M’lungu zikomo, pon’thandiza kuti

    N’samade nkhawa.

    (KOLASI)

    Ndiziteteza mtima wangawu,

    N’ganizire zabwinodi.

    N’saganizire zofo’ketsa.

    Ndidzapezatu mtendere ndithu.