Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndi Maso a Chikhulupiriro

Ndi Maso a Chikhulupiriro

(Salimo 27:13)

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Ndioperenji mkango?

    Ndioperenji anthu?

    Yehovatu alipo

    Ndiopenso chani!

    M’lungu andipulumutsa.

    (KOLASI)

    Ndi masotu a chikhulupiriro

    Sindidzaopa chilichonsecho.

    Yehovatu alipo

    Sindichita mantha,

    Amakhala nane pafupi

    An’thandiza.

  2. 2. Atumiki akale

    Anakhulupirika.

    Chikhulupiriro

    Chinawathandiza.

    M’lungu adzawaukitsa.

    (KOLASI)

    Ndi masotu a chikhulupiriro

    Sindidzaopa chilichonsecho.

    Yehovatu alipo

    Sindichita mantha,

    Amakhala nane pafupi

    An’thandiza.

    (VESI LOKOMETSERA)

    Ndi Yehova, zonse ndi zotheka

    Ndili n’chikhulupiriro.

    Chikhulupiriro chathandiza kuti

    Ndipirire pa mavuto.

  3. 3. M’lungu wandilonjeza

    Tsogolo labwino.

    Ndipirirebe

    Poti posachedwa

    Yehova athetsa mavuto.

    (KOLASI)

    Ndi masotu a chikhulupiriro

    Sindidzaopa chilichonsecho.

    Yehovatu alipo

    Sindichita mantha,

    Amakhala nane pafupi

    An’thandiza.

    An’thandiza.

(Onaninso Aheb. 11:1-40.)