Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Gwiritsani Ntchito Mphamvu Zanu Potumikira Yehova

Gwiritsani Ntchito Mphamvu Zanu Potumikira Yehova

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Ulitu mwana, zinkaphwekako

    Kuchitatu zoyenera.

    Unkakondanso kulalikira,

    N’kupemphera nthawi zonse.

    (KUKONZEKERA KOLASI)

    Koma pomwe ukukula zinthu zingasinthe.

    Ungakanike kugogoda m’makomo mu ‘tumiki.

    Koma pomwe watalika chonde usasiye

    Kutumikira Yehova,

    Adzakudalitsa.

    (KOLASI)

    M’nyumba ya Yehova uli ndi malo,

    Akuthandiza.

    Ungamupatse Yehova zambiritu.

    M’lungu amaona,

    Amakukonda.

  2. 2. Pano wakula, zinthu zasinthadi,

    Mayesero ayambanso.

    Nkhawa nazo zachulukadi

    Pemphera, M’lungu amamva.

    (KUKONZEKERA KOLASI)

    Pomwetu wakula uzichita zimene

    Umaphunzira, udzasangalala ndithu.

    Pomwe ukufuna kuti usankhe zochita,

    Usaiwale Yehova,

    Adzakudalitsa.

    (KOLASI)

    M’nyumba ya Yehova uli ndi malo,

    Akuthandiza.

    Ungamupatse Yehova zambiritu.

    M’lungu amaona,

    Amakukonda.

    (VESI LOKOMETSERA)

    M’tumikire ndi mphamvu zako.

    N’zabwinodi, sungadzadandaule.

    (KOLASI)

    M’nyumba ya Yehova uli ndi malo,

    Akuthandiza.

    Ungamupatse Yehova zambiritu.

    M’lungu amaona,

    Amakukonda.

    (VESI LOKOMETSERA)

    M’tumikire ndi mphamvu zako.

    N’zabwinodi, sungadzadandaule.

    M’tumikire ndi mphamvu zako.

    N’zabwinodi, sungadzadandaule.