Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Uziphunzirapo Kanthu Ukalakwitsa

Uziphunzirapo Kanthu Ukalakwitsa

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Pa anthu ochimwafe

    Palibe amene,

    Anganenetu,

    Kuti sanalakwitseko.

    Lero walakwitsa,

    Chonde usafooke,

    Uphunzirepo kanthu.

    Mulungutu angakuthandize.

    (KOLASI)

    Ukagwa, udzuke.

    Ukhoza kusintha.

    Ukagwa, dzukatu.

    Uphunzireponso.

    Upemphe thandizo,

    Kwa Mulungu,

    Wamoyo.

    Tsimikiza mtima.

    Iye akulimbitsa.

    Ukagwa, udzuke.

  2. 2. Tsiku lina lafika,

    Ukudzi’mbabe mlandu.

    Kale silibwerera,

    Sungalisinthenso.

    Usataye mtima.

    Udalire Yehova.

    Mawu ake ngamphamvu,

    Akudzutsa, amakukondabe.

    (KOLASI)

    Ukagwa, udzuke.

    Ukhoza kusintha.

    Ukagwa, dzukatu.

    Uphunzireponso.

    Upemphe thandizo,

    Kwa Mulungu,

    Wamoyo.

    Tsimikiza mtima.

    Iye akulimbitsa.

    (VESI LOKOMETSERA)

    ’Mulungutu ndi wamkulu,

    Kuposa mitima yathu.’

    Iye akutsogolera.

    Um’dalire.

    Akudzutsa.

    (KOLASI)

    Ukagwa, udzuke.

    Ukhoza kusintha.

    Ukagwa, dzukatu.

    Uphunzireponso.

    Upemphe thandizo,

    Kwa Mulungu,

    Wamoyo.

    Tsimikiza mtima.

    Iye akulimbitsa.

    Ukagwa, udzuke.

    Ukagwa, dzukatu.