Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Ukagwa, Phunzilapo

Ukagwa, Phunzilapo

Daunilodi:

  1. 1. Palibe anganene

    Kuti salakwatu.

    Tonse pa dziko

    Timacimwa, timalakwa.

    Nawenso walakwa,

    Koma citapo kanthu.

    Tengelapo phunzilo,

    Ndipo mvela mawu a Yehova.

    (KOLASI)

    Ukagwa, nyamuka,

    Iwe phunzilapo.

    Nyamuka, pilila,

    Usataye mtima.

    Yehova afuna

    Kuti akuthandize.

    Ndipo dziŵa kuti

    Udzakhala wolimba

    Ukaphunzilapo.

  2. 2. Madzi akatayika,

    Indetu sawoleka.

    Sungasinthe zimene

    Zinapita kale.

    Conco osaopa,

    Pemphela kwa Yehova.

    Ŵelenga mawu ake

    Kuti akuonetse zocita.

    (KOLASI)

    Ukagwa, nyamuka,

    Iwe phunzilapo.

    Nyamuka, pilila,

    Usataye mtima.

    Yehova afuna

    Kuti akuthandize.

    Ndipo dziŵa kuti

    Udzakhala wolimba.

    (BILIJI)

    Lola mawu a Yehova

    Azikukumbutsa ndithu

    Kuti cikondi cake n’cacikuludi.

    Usafo’ke.

    (KOLASI)

    Ukagwa, nyamuka,

    Iwe phunzilapo.

    Nyamuka, pilila,

    Usataye mtima.

    Yehova afuna

    Kuti akuthandize.

    Ndipo dziŵa kuti

    Udzakhala wolimba

    Ukaphunzilapo.

    Ukaphunzilapo.