Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nidziŵa Yehova Ali Nane

Nidziŵa Yehova Ali Nane

Daunilodi:

  1. 1. Nauka m’mamaŵa kukonzekela.

    Napemphela kwa M’lungu, nanyamuka.

    Olo aniletsa kulalikila,

    N’dzamvela M’lungu; sin’dzaleka.

    (KOLASI)

    Sin’dzacita mantha, Yehova M’lungu ali nane.

    Amanipatsa mtendele woculuka.

    Amanipatsa mtendele woculuka.

  2. 2. Uja mwamuna ‘mene ninapeza

    Analidi na nkhawa zambili.

    Conco nifuna nikamuonenso.

    Adzakondwela kudziŵa co’nadi.

    (KOLASI)

    Sin’dzacita mantha, Yehova M’lungu ali nane.

    Amanipatsa mtendele woculuka.

    Amanipatsa mtendele woculuka.

    (BILIJI)

    Inde, monga moto mumtima mwanga

    Mawuwa nidzalankhulabe.

    Nidzalengeza dzina lake;

    Sinidzaleka mpaka kumapeto.

    Nidziŵa kuti sinili nekha,

    Nidzalimbabe mpaka imfa.

    N’dzamudalila Yehova M’lungu;

    Walonjeza moyo wosatha.

  3. 3. Usiku pogona nipemphela,

    Kuyamika Atate Yehova.

    Zonigwela maŵa sinidziŵa.

    Nidalila M’lungu, siniopa.

    (KOLASI)

    Sin’dzacita mantha, Yehova M’lungu ali nane.

    Amanipatsa mtendele woculuka.

    Amanipatsa mtendele woculuka.