Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Timakobidi Tiwiri”

“Timakobidi Tiwiri”

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Tochepa

    N’tomwe ali nato.

    Enatu

    Akupereka zambiri zedi

    Ndipo iye

    Akudzimva wachabe.

    Kodi M’lungu wake

    Angalandire tochepa?

    (KOLASI)

    Kaya n’tochepa,

    Tiperekebe

    Ndipo M’lungu alandira.

    Iye ndi wamkulu

    Kuposa anthufe,

    Kuposa mitima yathu.

    Timpatse.

  2. 2. Kalekale

    Zinkamuyenderadi.

    Ankapereka

    Zochulukanso, anali ndi mphamvu.

    Pano zochepa

    N’zomwe angakwanitse

    Koma kwa Yehova

    Zochepazo ndi zochuluka.

    (KOLASI)

    Kaya n’tochepa,

    Tiperekebe

    Ndipo M’lungu alandira.

    Iye ndi wamkulu

    Kuposa anthufe,

    Kuposa mitima yathu.

    Timpatse.

    (VESI LOKOMETSERA)

    Amamvetsatu tikapereka

    Zochepa kapena zochuluka.

    Sadzatiiwala.

    (KOLASI)

    Kaya n’tochepa,

    Tiperekebe

    Ndipo M’lungu alandira.

    Iye ndi wamkulu

    Kuposa anthufe,

    Kuposa mitima yathu.

    Tim’patse.

    Tim’patse zomwe tingathe.