“Sadzachedwa” (Nyimbo ya Msonkhano wa 2023)
Pangani Dawunilodi:
1. Dziko lopanda nkhawa zonsezi
Ndi lomwe tonse tikulakalaka.
Padziko lonse zinthu zaipa
Tikudziwatu muthetsa zonsezi.
(KOLASI)
Molezadi mtima tikudikirira
Dzikotu latsopano.
Mapeto afika posachedwa pompa.
Mawu anu akuti, ‘sadzachedwadi.’
2. Mulungu wathu mudzaitana
Omwe anafa, ndipo adzadzuka.
Zidzakhalatu zosangalatsa!
Tithandizeni kulezabe mtima.
(KOLASI)
Molezadi mtima tikudikirira
Dzikotu latsopano.
Mapeto afika posachedwa pompa.
Mawu anu akuti, ‘sadzachedwadi.’
3. Mumafufuza mitima yathu
N’kutitonthoza ndi chiyembekezo.
Tichite khama polalikira.
Tikhale maso nthawi yafupika.
(KOLASI)
Molezadi mtima tikudikirira
Dzikotu latsopano.
Mapeto afika posachedwa pompa.
Mawu anu akuti, ‘sadzachedwadi.’
Tiyembekezerebe.
(Onaninso Akol. 1:11.)