Capamodzi Tidzamuimbila Mokondwa Yehova
Daunilodi
1. Anthu akulila,
ambili asocela
Pali nkhondo; kumenyana,
Mayankho sapezeka
Anthu amanama
mwa kulonjeza bodza
Koma Yehova akulonjeza
Kutipatsa mtendele.
(KOLASI)
Tidzapeza
mtendele
Capamodzi
tidzamuimbila
Yehova mokondwa
2. Malonjezo onse
adzakwanilitsidwa
Yehova M’lungu amatikonda
Tidzaona mtendele,
Siticita mantha
amatitonthoza
Ndipo tidziŵa tidzapeza
Mtendele wosatha.
(KOLASI)
Tidzapeza
mtendele
Capamodzi
tidzamuimbila
Yehova mokondwa.
(BILIJI)
M’dziko latsopano
Tidzamasulidwa
Sikudzakhala imfa cisoni
Anthu adzamvela
Yehova Mulungu.
(KOLASI)
Tidzapeza
mtendele
Capamodzi
tidzamuimbila
Tidzapeza
mtendele
Capamodzi
tidzamuimbila
Yehova mokondwa
Ku’muyaya wonse!