Tidzamuimbira

Tidzamuimbira
  1. 1. Anthu akulira,

    Akusowa pogwira.

    Nkhondo, njala, sizikutha.

    Mafunso ndi ambiri.

    Nkhawa zikukula,

    Angathandize n’ndani?

    Yehova yekha adzatipatsa

    Dziko labwino zedi.

    (KOLASI)

    Atipatsa

    Mtendere.

    Madalitso

    Padzikotu lonse.

    Tidzamuimbira.

  2. 2. Sinkhambakamwatu.

    Kaya zivute bwanji

    Yehova M’lungu azitipatsa

    Mtendere ngati mtsinje.

    Sitizida nkhawa,

    Tizisangalala.

    Podziwa kuti posachedwa

    Mavutowa atha.

    (KOLASI)

    Atipatsa

    Mtendere.

    Madalitso

    Padzikotu lonse.

    Tidzamuimbira.

    (VESI LOKOMETSERA)

    Mu’fumu wa M’lungu

    Mavuto adzatha.

    Mtendere konse, imfa kulibe,

    Anthu adzaimba

    Mwachisangalalo.

    (KOLASI)

    Atipatsa

    Mtendere.

    Madalitso

    Padzikotu lonse.

    Atipatsa

    Mtendere.

    Madalitso

    Padzikotu lonse.

    Tidzamuimbira.

    M’dziko latsopano.