Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pang’onong’ono N’kanafa

Pang’onong’ono N’kanafa

Pang’onong’ono N’kanafa

“Nthaŵi zina ndimalota nditakhalanso ndi miyendo iŵiri. . . . Zaka zapitazo, ndidakali kamwana, ndinapita kukaseŵera ndi anzanga pafupi ndi nyumba yathu. Mwadzidzidzi ndinangomva kuti ‘PHOO!’. . . Mwendo wanga wonse wamanja unadukiratu.”—Song Kosal, wazaka 12, wa ku Cambodia.

TSIKU lililonse, pafupifupi anthu 70 amalumala kapena kufa chifukwa cha maboma okwirira. Ambiri amene amavutika ndi mabombawa si asilikali. Koma ndi anthu wamba—anthu oŵeta ng’ombe, akazi otunga madzi, ndi ana akamaseŵera. Mwachitsanzo Rukia, wa zaka zisanu ndi zitatu amene ali pachithunzi cha pachikutopo, anavulazidwa ndi bomba lokwirira limene linapha achimwene ake atatu ndi azakhali ake.

Bomba lokwirira lingathe kukhala ndi mphamvu kwa zaka 50 atalikwirira. Motero, “lili chida chokhacho chimene chimapha anthu ochuluka kwambiri nkhondo itatha kusiyana ndi pamene idakali m’kati,” ikutero magazini yotchedwa The Defense Monitor. Palibe amene akudziŵa kuti pali mabomba okwirira angati padziko lonse. Si kwachilendo kumva ena akuti alipo pafupifupi 60 miliyoni. N’zoona kuti mabomba ambiri okwiriridwa akufukulidwa. Komabe, posachedwa pompa, mu 1997, bungwe la United Nations linati “bomba limodzi lililonse likachotsedwa, enanso 20 amakwiriridwa. Mu 1994 mabomba pafupifupi 100,000 anawafukula koma enanso 2 miliyoni anakwiriridwa.”

Kodi n’chifukwa chiyani akuluakulu ambiri ankhondo amasiku ano amasankha mabomba okwirira? Kodi mabomba ameneŵa amakhudza bwanji chuma ndiponso umoyo wa anthu? Kodi anthu amene amapulumuka amavutika motani? Kodi pali nthaŵi iliyonse imene dziko lathuli lidzakhale lopanda mabomba okwirira?

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

© ICRC/David Higgs

Copyright Nic Dunlop/Panos Pictures