Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Aids mu Afirika—Kodi Pali Chiyembekezo Chotani M’zaka Chikwi Zatsopano?

Aids mu Afirika—Kodi Pali Chiyembekezo Chotani M’zaka Chikwi Zatsopano?

Aids mu Afirika—Kodi Pali Chiyembekezo Chotani M’zaka Chikwi Zatsopano?

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU ZAMBIA

MU SEPTEMBER wapitayo nthumwi zochokera ku madera osiyanasiyana a mu Afirika zinafika ku Lusaka, Zambia, kukachita msonkhano wa 11th International Conference on AIDS and STDs in Africa (Msonkhano wa Mayiko Onse Wokambirana za AIDS ndi Matenda Opatsirana Kudzera m’Chiwerewere mu Afirika). Chimodzi mwa zolinga za msonkhanowo chinali kulimbikitsa mgwirizano wa zigawo zonse pa kuyankha funso lakuti, Kodi tingalimbane motani ndi kufala kwa matenda a AIDS mu Afirika?

Pulofesa Nkandu Luo, yemwe panthaŵiyo anali nduna ya zaumoyo ku Zambia, ananena kuti nthendayi “yafika poipa kwambiri” mu Afirika ndiponso m’madera ena amene akutukuka kumene, ndipo anawonjezera kuti nthendayi “ikulepheretsa ngakhalenso kubwezera m’mbuyo ntchito zachitukuko zofunika kwambiri m’zaumoyo ngakhalenso m’ntchito zachikhalidwe ndi zachuma.”

M’nkhani yosiyirana yonena za kuteteza magazi, okamba anavomereza kuti AIDS yafalitsidwa kudzera m’kuika magazi. Dokotala wina, yemwe ndi nthumwi ya World Health Organization’s Blood Safety Unit (Nthambi ya Bungwe la Zaumoyo Padziko Lonse Yoona za Kuteteza Magazi), anati pamene kuli kwakuti kuchita chiwerewere ndi munthu amene ali ndi kachilombo koyambitsa matendaŵa sikufalitsa kachilombo ka HIV nthaŵi zonse, munthu wothiridwa magazi omwe ali ndi kachilombo koyambitsa matenda a AIDS amagwidwa ndi nthendayi, nthaŵi zonse akangotero! Pachifukwa chabwino chimenechi, dokotala ameneyu ananena kuti m’zochitika zoterozo, “kuika munthu magazi kotetezeka kwambiri ndiko kusamuika n’komwe.”

Nthumwi za kumsonkhanowo zinanenetsa kuti kukwera mtengo kwambiri kwa chithandizo cha mankhwala a matendaŵa kukupangitsa kukhala kovuta kapenanso kulepheretseratu anthu amene ali ndi AIDS kupeza chithandizo chamankhwala. Mwachitsanzo, pa avareji, munthu wokhala mu mzinda wa ku Uganda amapeza ndalama zosaposera madola 200 pamwezi. Koma chithandizo chamankhwala akupha mavairasi chingakwane madola 1,000 pamwezi!

Msonkhano umenewo wa ku Lusaka unasonyeza kuti chiyambi cha zaka chikwi zatsopano sichingapeze njira zosavuta zothetsera kufalikira kwa matenda a AIDS. Koma ngakhale kuti zinthu zili choncho, anthu amene akuphunzira Baibulo amadziŵa kuti ndithudi njira yothetsera matenda onse ndi ya Mlengi, Yehova Mulungu, amene akulonjeza kuti m’dziko lake latsopano, “wokhalamo sadzanena: Ine ndidwala.”—Yesaya 33:24.

[Mapu/Zithunzi patsamba 31]

Pulofesa Nkandu Luo

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzi ndi chilolezo cha E. Mwanaleza, Times of Zambia