Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi “Kupemphera Pawekha” Kungathetse Vutoli?

Kodi “Kupemphera Pawekha” Kungathetse Vutoli?

Kodi “Kupemphera Pawekha” Kungathetse Vutoli?

POMWE ANTHU AKUCHOKA m’magulu achipembedzo, sizodabwitsa kuti anthu ambiri akuyamba chipembedzo chopemphera paokha. Komabe, mafunso ndi akuti, Kodi kuchita zimenezi kungathetse njala yauzimu? Kodi “kupemphera pawekha” kungathetse vutoli?

Kuti tiyankhe mafunso ameneŵa, tiyeni tione kaye ngati kupemphera pawekha kungakhale kothandiza tikakupenda bwinobwino ndi ‘mphamvu zathu za kulingalira,’ yomwe ndi ina mwa mphatso zazikulu kwambiri zimene tili nazo.—Aroma 12:1, NW.

Munthu woganiza bwino amakana zimene zimatsutsana. Komabe, ku Sweden pofufuza chipembedzo chopemphera pawekha, anapeza kuti nthaŵi zambiri anthu “amaphatikiza mothamanga malingaliro osiyanasiyana (ndi osagwirizana) achilengedwe ndiponso cholinga cha moyo pa zimene amaganiza.”

Mwachitsanzo, anthu aŵiri okha pa anthu 100 alionse amene ankati ndi “Akristu paokha” anatchula Yesu, kunenanso kuti anakhalakodi. Komanso anali kutchulatchula chiphunzitso chakuti munthu akamwalira amakabadwanso kwinakwake. Ndiyeno, kodi zikugwirizana kunena kuti mumatsatira Yesu Kristu koma mukukana kutsatira khalidwe lake ndi ziphunzitso zake n’kumatsatira ziphunzitso zosiyana kwambiri ndi za Kristu? *

Mphamvu zathu za kulingalira zimatithandizanso kupeŵa zinthu zosamvetsetseka ndi zosatsatirika. Ngakhale zili choncho anthu ena atafunsidwa ngati amakhulupirira “Mulungu kapena mphamvu yake,” ambiri anayankha kuti, zikhoza kutheka kuti zilikodi zinthu “Zinazake” zangati zimenezo. Wina anati: “Ndimakhulupirira kuti pali mphamvu ina yake yosaoneka koma sindinganene kuti mphamvuyo ndi ya Mulungu.” Amene amakhulupirira Mulungu ankaona kuti “sawathandiza kwenikweni pa moyo wawo.” Motero lipotili linati chipembedzo chongopemphera panokha chili ndi “malingaliro ambiri osamvetsetseka,” ndipo linamaliza mwa kupereka yankho limene anthu ankakonda kunena lakuti: “Ndimakhulupirira chinachake, koma sindidziŵa kuti n’chiyani.”

Kufufuza chipembedzo chongopemphera paokha kumene kunachitika ku Canada kunasonyeza zomwezi. Magazini ya Alberta Report inati: “Anthu masiku ano amakhulupirira kwambiri zinthu zosiyanasiyana zosamvetsetseka. Ndiponso tingathe kuona kuti anthu akamatsatira zinthu zimene amakhulupirira paokhazi siziwathandiza. Alibe malamulo enieni a khalidwe labwino. Choncho zilibe phindu.” Magaziniyi inanena za “mulungu wosweka” chifukwa amene amakhulupirira zimenezi “amatenga zidutswa zosiyanasiyana za zikhulupiriro zodziŵika bwino.” Kodi mukuganiza kuti ndi nzeru kuganiza kuti zikhulupiriro za chipembedzo ngakhale chiyembekezo cha m’tsogolo zidalire pa mfundo zosamvetsetseka, zokayikitsa ndi zosakhutiritsa, ndiponso zosiyanasiyana zoterozo?

Timafunika Kuyanjana ndi Ena

Okhulupirira a chipembedzo amasangalala kwambiri ndi kuyanjana, ubale ndi kugwirizana. (Machitidwe 2:42, 46) Koma popeza chipembedzo chopemphera pawekha n’cha inu nokha basi, kodi chingachite bwanji zimenezi?

Kodi chipembedzo chopemphera pawekha chimene “aliyense amakhala ngati ali ndi tchalitchi chake” sichimangowonjezera magawano a chipembedzo pakati pa anthu? Magazini ya Alberta Report, inati: “Tsopano chipembedzo ndi nkhani ya zimene munthu akuganiza . . . , ndipo motero takhala m’dziko la zikhulupiriro osati mazana ochepa koma mamiliyoni angapo.” N’chifukwa chake chipembedzo chopemphera pawekha, akuti ndi chosokoneza mwauzimu.

Bwanji Khalidwe la Munthu?

Bishopu wa ku Sweden, Martin Lönnebo, atafunsidwa ndi atolankhani a nyuzipepala ya Svenska Dagbladet ananena kuti “chipembedzo chopemphera pawekha sichingatithandize nthaŵi yathu ino, ndipo mfundo zake zokhudza makhalidwe sizingathe kudzafika m’mbadwo wam’tsogolo.” Mungathe kutsimikizira zimenezi poona maganizo amene makolo ambiri a ku Sweden amakhala nawo polera ana. Nyuzipepala ya Svenska Dagbladet inalongosola mwachidule za maganizo ameneŵa, ponena kuti: “Khulupirirani zimene mukufuna. Ndipo musakakamize ana anu kuti asankhe chikhulupiriro chinachake. Koma alekeni adzasankhe akadzakula.”

Nyuzipepalayi inavomereza kuti kuwauza ana makhalidwe achipembedzo tingati n’kuwasokoneza maganizo. Komano inamaliza ndi mawu akuti: “Kuphunzitsa ana makhalidwe achipembedzo n’kothandiza ndipo ingakhale njira yokha . . . yowathandizira kudzasankha okha chipembedzo.” Ndithudi, mavuto amene achinyamata akukumana nawo masiku ano akusonyeza kuti chipembedzo chopemphera pawekha chalephera kugwirizanitsa mabanja pogwiritsa ntchito mfundo zosapita m’mbali za makhalidwe abwino zimene angaphunzitsenso mbadwo wotsatira.

Choncho, zikuoneka kuti chipembedzo chopemphera pawekha sichingatipatse mayankho odalirika a mafunso amene timakhala nawo pamoyo, ngakhalenso kugwirizanitsa anthu kapena kuwapatsa chitsogozo cha makhalidwe abwino chimene amafunikira. Nkhani imene taitchula poyamba ija ya mu nyuzipepala ya Svenska Dagbladet inanena izi pankhani ya chipembedzo chopemphera pawekha: “Ngati ‘chikhulupiriro’ chili ndi zonse zimene munthu amakonda, ndiye kuti n’chopanda tanthauzo. Ndipo ufulu wopanda malire, si ufulu weniweni.”

Ndithudi, m’mbali zambiri chipembedzo chopemphera pawekha sichikhutiritsa anthu mwauzimu. Inde, kodi munthu wanzeru angaganize kuti angakhutire mwauzimu mwa kungosankha zikhulupiriro m’miyambo yosiyanasiyana, ngati kuti akusankha zakudya zimene amakonda patebulo limene aliyense angatenge yekha zakudya zimene akufuna? Zikuonekanso kuti magulu achipembedzo alephera kukhutiritsa anthu m’njira imeneyi. Kodi nanga ndiye tigwire mtengo wanji?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Yesu sanaphunzitse kuti akufa amakabadwanso kwinakwake. Koma anaphunzitsa kuti akufa sadziŵa kanthu; tinganene kuti ali mtulo, akudikira kudzaukitsidwa.—Yohane 5:28, 29; 11:11-14.

[Chithunzi pamasamba 24, 25]

Kodi tiyenera kuona chipembedzo monga tebulo pamene paikidwa zakudya zosiyanasiyana, pomwe tingasankhe zikhulupiriro zimene zatisangalatsa?