Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Njira Yabwino Yokukhutiritsani Mwauzimu

Njira Yabwino Yokukhutiritsani Mwauzimu

Njira Yabwino Yokukhutiritsani Mwauzimu

N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU amafunika kupembedza? Ena anganene kuti anthu amafuna nkhani zauzimu kuti atetezeke m’dziko lopanda chitetezoli. Koma si zokhazo ayi. Nkhani ina m’magazini ya American Sociological Review inati: “Anthu safuna kupembedza chifukwa cha nkhani ya chitetezo yokha. Anthu nthaŵi zonse akhala akufunafuna mayankho a mafunso monga akuti: Kodi moyo unachokera kuti? Kodi m’tsogolo muli zotani? Kodi tinabadwiranji?”

Ndithudi, simungatsutse kuti ameneŵa ndi mafunso ofunika kwambiri. Ndiye kodi sakufunikanso mayankho odalirika? Mafunso ameneŵa ndi ofunika kwambiri motero sitingawayankhe mongosankhapo zikhulupiriro zotisangalatsa m’miyambo yosiyanasiyana ya chipembedzo. Tifunika kugwiritsa ntchito njira yabwino kuti tipeze mayankho odalirika a mafunso ofunika kwambiri ameneŵa.

Kodi pali njira ina yabwino? Ferrar Fenton, wotembenuza Baibulo, ananena mawu ochititsa chidwi kwambiri ponena za buku limeneli. Analitcha kuti ndi njira yokhayo “imene Anthu Angadziŵire za Chilengedwe Chonse Ndiponso za Iwo Eni.” Inde Baibulo limayankha mafunso okhudza zakale, zamasiku ano, ndi zam’tsogolo. Limatiuza za kumene tinachokera, cholinga cha moyo, momwe tingakhalire achimwemwe, ndiponso zimene zili m’tsogolo. Sipanakhaleko buku lina limene lasintha zochita za anthu kapena limene lakumana ndi mikwingwirima yoopsa ngati Baibulo. Nangano n’chifukwa chiyani anthu ambiri amanyalanyaza buku lapadera limeneli akamafufuza mayankho a mafunso okhudza moyo?

Anthu ambiri sanayambe akhala pansi n’kuona kuti Baibulo ndi matchalitchi amene akudziŵa, n’zosiyana kwambiri. Aona anthu otchedwa Akristu akuphana m’dzina la Mulungu. Ambiri adandaula monga momwe nyuzipepala ya The Guardian inanenera, kuti “masiku ano ansembe akukonda kwambiri kusonkhetsa ndalama kuposa kuyendera anthu awo ndi kumawathandiza mwauzimu.” Mwina amaganiza kuti Baibulo limavomereza kapena limalekerera khalidwe limeneli. Zoona zake n’zakuti, Baibulo limalangiza Akristu ‘kukondana wina ndi mnzake,’ ndipo limauza anthu amene amalalikira kuti, “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.” (Yohane 13:34; Mateyu 10:8) Choncho kodi n’kwanzeru kudana ndi Baibulo chifukwa cha zochita za anthu amene amangoti amalilemekeza koma salitsatira n’komwe?

Anthu ambiri amakhulupirira kuti Baibulo limatsutsana ndi sayansi, n’lodzitsutsa, ndiponso n’lakale. Koma kuliŵerenga mosamalitsa kumasonyeza kuti zimenezi si zoona. N’zoona kuti Baibulo si buku lophunzitsa sayansi. Koma likamafotokoza nkhani za sayansi monga ndondomeko ya kulengedwa kwa zamoyo pa dziko lapansi, mpangidwe wa dziko lapansi, kapena zoyenera kuchita pamatenda opatsirana limanena zoona zokhazokha. Komanso, limanena zinthu zaka mazana ambiri asayansi asanazitulukire. Ndipo ngakhale kuti Baibulo lili ndi mabuku 66 amene analembedwa kwa zaka 1, 600, onse amagwirizana. Komanso, Baibulo limasonyeza mmene anthu alilidi pankhani ya kuganiza ndi makhalidwe awo, zimene zimalichititsa kuti lizikhalabe lothandiza kwambiri ngakhale masiku ano.

Buku lapadera limeneli limanena chinthu chofunika kwambiri pankhani yolambira Mulungu. Limati anthu sayenera kulambira momwe akufunira, koma momwe Mulungu amafunira. (Yohane 5:30; Yakobo 4:13-15; 2 Petro 1:21) Koma ndi anthu ochepa chabe amene amavomereza ndi kutsatira mfundo imeneyi. Kuyambira kalekale anthu akhala akuyambitsa zipembedzo zoti zigwirizane ndi zofuna zawo. Anthu akamasema milungu yawo ya mitengo ndi kumailambira amakhala akutero. Magulu achipembedzo akamaphunzitsa ziphunzitso zawozawo amakhala akuteronso. Ndipo kodi si zimenenso anthu amene ali m’chipembedzo chopemphera pawokha amachita kuti chigwirizane ndi zofuna zawo?

Ganiziraninso izi. Bwanji osachita zimene woweruza wamkulu m’bwalo lamilandu lapamwamba ku United States anachita? Iye mosakondera anaona maumboni osonyeza ngati Baibulo n’loona kapena n’lonama, monga momwe amachitira akamaŵeruza milandu m’khoti. Kodi anapeza zotani? Ananena kuti: “Ndaona kuti Baibulo si buku lochokera kwa anthu ayi, koma linachokera kwa Mulungu.”

Kodi inunso mungafufuze motani mogwirizana ndi zimenezi? Mongokuthandizani maganizo tinganene kuti yambani n’kuphunzira Baibulolo mwandondomeko yabwino, pofufuza mayankho a mafunso amene ali kumayambiriro kwa nkhani ino. Pali anthu a Mboni za Yehova pafupifupi 6 miliyoni, m’mayiko 235, amene anachita kale phunziro limeneli. Amagwiritsa ntchito nthaŵi yawo kuuza ena zimene aphunzira. Phunziro la Baibulo lapanyumba limene amachititsa kwaulere lathandiza anthu ambiri zedi kupeza chikhulupiriro chenicheni osati cha kanthaŵi chabe kapena chongoti popeza ineyo ndachikonda. Chikristu choona, chosadetsedwa chimene chili m’Baibulo, si chipembedzo wamba. Chimanena zoona zake za Mulungu ndi zofuna zake. Nanga chodzivutitsira ndi zinthu zosadziŵika bwinozo chikhale chiyani?—Yohane 17:17.

[Zithunzi patsamba 26]

Njira yabwino kuti mukhale wokhutira mwauzimu ndiyo kuphunzira za Mulungu m’Baibulo ndiponso kuchezerana ndi olambira oona