Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Anali Munthu Wolimbikitsa Nkhondo Kapena Mtendere

Kodi Anali Munthu Wolimbikitsa Nkhondo Kapena Mtendere

Kodi Anali Munthu Wolimbikitsa Nkhondo Kapena Mtendere

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU SWEDEN

Chaka chilichonse anthu kapena mabungwe amene achita zinthu zothandiza kwambiri potukula moyo wa anthu m’njira zosiyanasiyana amawapatsa mphoto imene amaitcha kuti Nobel Prize. Kodi anayamba liti kupereka mphoto imeneyi, ndipo kodi imagwirizana bwanji ndi mtendere wa padziko lonse umene anthu amafuna?

ANTHU akamva dzina lake amaganiza za kutukula moyo wa anthu, koma munthuyu anapeza chuma chosaneneka pogulitsa zida zankhondo. Kodi tikunena ndani? Tikunena Alfred Bernhard Nobel, yemwe anali ndi fakitale yakeyake ndiponso wasayansi ya zamankhwala wa ku Sweden. Anthu akhala akum’tama chifukwa cha ntchito yake yofuna kuthandiza anthu, komanso ena akhala akumutchanso kuti “wamalonda ophetsa anthu.” Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Nobel anatulukira njira yopangira onga wa mzinga, ndipo anapeza ndalama zambiri popanga ndi kugulitsa mizinga yoopsa kwambiri.

Koma Nobel atafa mu 1896, panapezeka chinthu chodabwitsa kwambiri. M’kalata imene anasiya yolangiza anthu za kagaŵidwe ka chuma chake analembamo kuti pa ndalama zake za kubanki apatulepo ndalama zokwana madola 9 miliyoni n’cholinga chakuti pakutha pachaka chilichonse azipereka chiwongola dzanja cha ndalamazi kwa anthu amene achita zinthu zopindulitsa kwambiri pa nkhani za sayansi, zachipatala, zolembalemba, ndi zamtendere.

Poyamba, anthu ambiri anadabwa nazo. Kodi n’chiyani chinam’chititsa munthu wogulitsa mizinga ameneyu kukhala wofunitsitsa kupereka mphoto kwa anthu ochita zinthu zopindulitsa ndiponso zobweretsa mtendere? Anthu ena ananena kuti mwina Nobel chikumbumtima chake chinkam’pweteka chifukwa chakuti ntchito yopanga mizinga imene anaichita m’moyo wake wonse, inaphetsa anthu ambiri. Koma anthu ena ankaona kuti kuyambira kale Nobel anali munthu wofuna zamtendere. N’zoonadi zikuoneka kuti iye ankakhulupirira kuti anthu akamapanga zida zoopsa kwambiri, angathenso kumaopa kuchita nkhondo. Akuti nthaŵi inayake anauza wolemba nkhani wina kuti: “N’kutheka kuti mafakitale anga opanga onga wa mizinga ndiwo adzayambe kuthetsa nkhondo nyumba yanu ya malamulo isanatero.” Ndipo ananenanso kuti: “Ikadzafika nthaŵi yoti mwina magulu aŵiri omenyana nkhondo n’kuphana onse m’kamphindi kochepa chabe, n’kutheka kuti mayiko onse otukuka adzachita mantha n’kutula pansi zida zawo.”

Kodi zimene Nobel analoserazo zinachitikadi? Kodi anthu aphunzirapo chiyani patatha zaka 100 Nobel atafa?

[Mawu Otsindika patsamba 3]

“Ndingakonde nditapanga chida choopsa kwambiri chotha kupulula anthu ochuluka n’kupangitsa anthu kusafunanso kuchita nkhondo mpaka kalekale” anatero ALFRED BERNHARD NOBEL

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Tsamba 2: Bomba: Chithunzi cha U.S. Navy; nyumba zogumuka: CHITHUNZI CHA BUNGWE LA UN 158178/J. Isaac; tsamba 3: Nobel: © Nobelstiftelsen