Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kutengeka ndi Zithunzi Zolaula Kulibe Vuto Lililonse?

Kodi Kutengeka ndi Zithunzi Zolaula Kulibe Vuto Lililonse?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Kutengeka ndi Zithunzi Zolaula Kulibe Vuto Lililonse?

CHA m’ma 1850 akatswiri ena ofufuza za mbiri yakale pokumba m’mabwinja anayamba kukumba mabwinja a ku Pompeii, ndipo anakhumudwa kwambiri ndi zimene anafukula. Pakati pa zithunzithunzi zokongola zozokotedwa pa makoma apulasitala ndi zojambulajambula zina, panalinso zojambulajambula ndiponso ziboliboli zolaula koopsa zimene zinangomwazikana ponsepo. Ponyansidwa nazo zithunzizi, akuluakulu aboma anazibisa m’nyumba zachinsinsi zosungiramo zinthu zakale zochititsa chidwi. Mawu a m’chingelezi amene m’chicheŵa tikuwatchula kuti “zolaula” ndi ochokera ku mawu aŵiri achigiriki amene amatanthauza kuti “kulemba nkhani zokhudza mahule.” Masiku ano tanthauzo la mawu ameneŵa ndilo “kusonyeza zinthu zokhudza kugonana m’mabuku, zithunzi, zosemasema, mafilimu, kapenanso m’zinthu zina zotero n’cholinga chofuna kudzutsa chilakolako chogonana.”

Masiku ano zolaulazi zafala mosaneneka ndipo zikuoneka kuti anthu ambiri amakono amasangalala nazo. Poyamba zinkangopezeka m’malo oonetseramo mafilimu achabechabe ndi m’madera okhala nyumba za mahule, koma masiku ano zili ponseponse m’madera ambiri. Ku United States kokha, zithunzi zolaula zimabweretsa ndalama zoposa madola teni biliyoni pachaka!

Anthu ena okonda zithunzi zolaula amanena kuti zithunzi zimenezi n’zabwino chifukwa zimathandiza kukometsa banja limene zinthu sizikuyenda bwino. Wolemba wina anati: “Zimathandiza kuti m’thupimu muyambenso kutentha. Zimaphunzitsa munthu njira zina n’zina zothandiza kuti azifikapo.” Ena amanena kuti zimathandiza kuti anthu azikhala omasukirana pa nkhani za kugonana. Wolemba wina dzina lake Wendy McElroy anati: “Zithunzi zolaula zimapindulitsa akazi.”

Koma pali anthu ena amene saona kuti zimenezi n’zoona. Zithunzi zolaula nthaŵi zambiri zimabweretsa mavuto ndiponso makhalidwe oipa osiyanasiyana. Anthu ena amanena kuti zinthu zolaula ndizo zimachititsa mavuto monga kugwiririra akazi ndiponso kuzunza akazi ndi ana m’njira zina. Chigaŵenga china choopsa chodziŵika bwino, dzina lake Ted Bundy, chinavomereza kuti chinali “kukonda kwambiri kuona zithunzi zolaula zosonyeza kugwirira akazi.” Chigaŵengachi chinati: “Mwini wakewe sudziŵa msanga kuti wafika potero kapena sudziŵa kuti limeneli ndi vuto lalikulu. . . . Koma maganizo ameneŵa . . . kenaka amakuchititsa kufuna kwambiri kugonana ndi mkazi mochita kum’gwiririra. Ndikufuna ndikutsimikizireni ndithu kuti chikhumbo chimenechi chimayamba kukuloŵerera mwapang’onopang’ono. Sikuti chimangoyamba nthaŵi imodzi ayi.”

Pakuti masiku ano anthu amaganiza zinthu zosiyanasiyana zokhudza nkhani zolaula ndiponso mmene zafalira, mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi Baibulo lili ndi malangizo alionse pankhaniyi?’

Baibulo Silipsatira Mawu Pankhani za Kugonana

M’Baibulo nkhani zokhudza kugonana sizitchulidwa mobisa mawu kapena mwamanyazi. (Deuteronomo 24:5; 1 Akorinto 7:3, 4) Solomo anapereka malangizo akuti: “Ukondwere ndi mkazi wokula naye . . . Mawere ake akukwanire nthaŵi zonse.” (Miyambo 5:18, 19) Baibulo limapereka malangizo omveka bwino pankhani zokhudza kugonana, kuphatikizaponso polekezera kutero. Limaletsa kugonana ndi munthu amene simunakwatirane naye ndiponso limaletsa makhalidwe ena onse onyansa okhudza za kugonana.—Levitiko 18:22, 23; 1 Akorinto 6:9; Agalatiya 5:19.

Ngakhale potsatira zimenezi, munthu ayenera kuchita zinthu modziletsa komanso mwaulemu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse; ndi pogona pakhale posadetsedwa.” (Ahebri 13:4) Malangizo ameneŵa n’ngosiyana kwambiri ndi cholinga cha zithunzi zolaula ndiponso mmene zimakhudzira anthu.

Zithunzi Zolaula Zimanyozetsa Kugonana

M’malo mochititsa anthu kuona kuti kugonana ndi chinthu chosangalatsa ndiponso chosonyezana chikondi pakati pa mwamuna ndi mkazi okwatirana, zithunzi zolaula zimanyozetsa ndiponso zimaipitsa kugonana. Kugonana ndi wina aliyense ukangotentha thupi amakusonyeza ngati kuti n’kosangalatsa ndiponso n’kwabwino. Kumalimbikitsanso kudzisangalatsa pawekha mosaganizira za mnzakoyo.

Zithunzizi zimachititsa kuti akazi, amuna ndiponso ana azikhala ngati anangobadwa n’cholinga choti azigonana basi. Lipoti lina linanena kuti: “Zimachititsanso kuti anthu aziona ngati kuti kukongola kwa munthu kumatengera pa chibadwidwe cha thupi lake, zimene zimawapangitsa kuti azitengeka ndi zinthu zachabechabe.” Lipoti lina linafika ponena kuti: “Kuonetsa akazi ngati ndi tianthu tinatake tosadziŵika bwino timene timangoyembekezera kuti tipeze mwayi, woti amuna azitiseŵeretsa, ndiponso amene amangodzivula kuti anthu awaonere n’cholinga chofuna ndalama ndi kusangalala, sizingathandize anthu kuona kuti nawonso amafunika kukhala ndi ufulu wofanana ndi aliyense, kupatsidwa ulemu ndiponso kuchitiridwa zinthu zabwino.”

Komatu, mtumwi Paulo analemba kuti chikondi “sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha.” (1 Akorinto 13:5) Baibulo limalimbikitsa amuna kuti “azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha” ndi kutinso ‘aziwachitira ulemu,’ osati kumawaona ngati anangobadwira kuti azisangalatsa anthu pogonana nawo basi. (Aefeso 5:28; 1 Petro 3:7) Kodi munthu amene kaŵirikaŵiri amakonda kuona zithunzi zoonetsa anthu ena ali maliseche tingati sakuchitadi zosayenera? Ndipo kodi tingati munthu ameneyo akuchitadi zinthu zaulemu? M’malo mwa chikondi, zithunzi zolaula zimachitisa munthu kukhala ndi chilakolako chosaganizira ena, koma chongofuna kuti zinthu zikuyendere iweyo basi.

Palinso mfundo ina imene tiyenera kuiganizira. Monga mmene zimakhaliranso zinthu zina zodzutsa chilakolako chogonana m’njira yosayenera, chinthu chimene chimam’tenga mtima munthuyo akamaona zithunzi zolaula sichichedwa kum’detsa kukhosi. Munthu wina wolemba nkhani anati “M’kupita kwa nthaŵi [anthu okonda kuona zithunzi zolaula] amafuna kuona zithunzi zochita kuonetseratu umaliseche wonse popanda kubisa kalikonse ndiponso zosemphana kwambiri ndi khalidwe lachibadwidwe . . . Angalimbikitse mkazi kapena mwamuna wawo kuti azigonana m’njira zosayenera . . . , motero n’kulephera kusonyezadi chikondi chawo chenicheni.” Kodi pamenepa mukuona kuti kutengeka ndi zithunzi zolaula kulibe vuto lililonse? Koma palinso chifukwa china chachikulu chimene tiyenera kupeŵera zithunzi zolaula.

Zimene Baibulo Limanena Pankhani ya Kumangolakalaka za Kugonana

Ngakhale kuti anthu ambiri masiku ano amaona kuti kumangoganizira za nkhani za kugonana si kolakwa kapena koopsa, Baibulo siligwirizana nawo. Limalongosola momveka bwino kuti zinthu zimene zimaloŵa m’maganizo athu n’zimene zimatichititsa kukhala ndi khalidwe linalake. Wophunzira wa Kristu, Yakobo anati: “Munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chim’kokera, nichim’nyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.” (Yakobo 1:14, 15) Yesu anati: “Yense wakuyang’ana mkazi kum’khumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.”—Mateyu 5:28.

Apa ndiye kuti mawu a Yakobo ndiponso a Yesu akuonetsa kuti zimene anthu amachita zimayambira m’maganizo mwawo. Zimene amalakalakazo akazilekerera kuti zimere mizu mapeto ake amalephera kukhala popanda kuziganizira m’maganizo mwawo. Zinthu zotere zimavuta kwambiri kuzichotsa m’maganizo ndipo mapeto ake munthuyo angathe kuzichitadi. Motero zinthu zimene timaloŵetsa m’maganizo mwathu zimatha kutichititsa zinthu zinazake mosavuta.

Kutengeka maganizo ndi nkhani za kugonana kumatisokoneza kulambira Mulungu. N’chifukwa chake Paulo analemba kuti: “Chifukwa chake fetsani ziŵalozo . . . dama, chidetso, chifunitso cha manyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano.”—Akolose 3:5.

Palembali Paulo akuti chilakolako cha kugonana n’chimodzimodzi ndi kusirira koipa, kumene kuli kulakalaka kwambiri chinthu chimene munthuwe ulibe. * Kusirira koipa ndi mbali ina ya kupembedza mafano. Chifukwa chiyani? N’chifukwa chakuti kwa munthu amene akusirira chinthu chinachake amaona chinthucho kukhala chofunika kwambiri kuposa chinthu china chilichonse, ngakhale kuposa Mulungu amene. Zithunzi zolaula zimam’pangitsa munthu kumangolakalaka kugonana ndi mkazi kapena mwamuna amene si wako. Wolemba zachipembedzo wina ananena kuti: “Umangofuna mkazi kapena mwamuna amene si wako. . . . M’maganizo mwako mumangodzaza zimenezo basi. . . . Komatu chilichonse chimene timachilakalaka motere ndiye kuti tikuchilambira.”

Zithunzi Zolaula Zimawononga Khalidwe

Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china . . . , zilingirireni izi.” (Afilipi 4:8) Munthu amene amangokhalira kuyang’ana ndiponso kuganizira zithunzi zolaula ndiye kuti sakumvera mawu a Paulo ameneŵa. Zithunzi zolaula n’zosayenera chifukwa mochititsa manyazi zimaonetsa poyera zinthu zongoyenera kudziŵa anthu aŵiri basi ndiponso zachinsinsi kwambiri. N’zonyansiratu kwenikweni chifukwa zimanyazitsa ndi kuchititsa anthu kukhala ngati zinyama. Sizisonyeza chikondi chifukwa sizilimbikitsa anthu kukhala oganizirana. Zimangolimbikitsa anthu kukhala ndi chilakolako chongoganizira za okha basi.

Zithunzi zolaula zimasokoneza zinthu zonse zimene Mkristu amayesa kuchita kuti ‘adane nacho choipa,’ chifukwa zimasonyeza anthu akuchita zinthu zosayenera ndiponso zowachititsa kulakalaka kugonana. (Amosi 5:15) Zimalimbikitsa anthu kuchita machimo ndipo zimatsutsana koopsa ndi zimene Paulo analemba polimbikitsa anthu a ku Efeso kuti “dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima; kapena chinyanso . . . kapena zopusa zimene siziyenera.”—Aefeso 5:3, 4.

Zithunzi zolaula zilibe pokomera. Zimawononga ndi kuipitsa khalidwe la munthu. Zingathe kusokoneza maubwenzi, ndipo zimalepheretsa anthu kuti azikhala ndi chilakolako chogonana ndi mnzawo monga mwachibadwa koma pokhapokha akaona anthu ena ali maliseche kapena kuti akugonana. Zimasokoneza maganizo ndiponso khalidwe la uzimu la munthu wamakhalidwe oterowo. Zimalimbikitsa kamtima kongofuna kuti zinthu zikuyendere iweyo basi komanso kadyera ndipo zimaphunzitsa anthu kuona anzawo ngati kuti anangobadwira kuti adzakhutiritse chilakolako chawo basi. Zimalepheretsa munthu kuyesayesa kuchita zabwino kuti akhale ndi chikumbumtima choyera. Koma choopsa kwambiri n’chakuti zingathe kuwononga ubwenzi wauzimu pakati pa munthuyo ndi Mulungu. (Aefeso 4:17-19) Ndithudi tiyenera kupeŵa zithunzi zolaula.—Miyambo 4:14, 15.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 20 Pa lembali sikuti Paulo anali kunena za chilakolako choyenera chimene munthu amakhala nacho chofuna kugonana ndi munthu amene anakwatirana naye.

[Chithunzi patsamba 14]

Zithunzi zolaula zimachititsa munthu kumaona akazi kapena amuna molakwika