Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kuvutika Ndi Tulo kwa Achinyamata Ndi Nkhani Yodetsa Nkhaŵa?

Kodi Kuvutika Ndi Tulo kwa Achinyamata Ndi Nkhani Yodetsa Nkhaŵa?

Kodi Kuvutika Ndi Tulo kwa Achinyamata Ndi Nkhani Yodetsa Nkhaŵa?

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU CANADA

MUNTHU akamasoŵa tulo amayamba kuchepa nzeru ndiponso amaiwalaiwala, ndipo kaŵirikaŵiri achinyamata ndiwo angathe kuvutika kwambiri ndi vutoli, inatero nyuzipepala ina ya ku Canada yotchedwa Globe and Mail. Nyuzipepalayi inatinso: “Zimene zimachititsanso kuti ana ndiponso achinyamata azisoŵa tulo ndi makhalidwe awo oipa, kukonda kukhumudwa msanga ndiponso kukanika kungokhala popanda kugwiragwira kanthu.” Akatswiri asayansi anafufuza mmene achinyamata okwana pafupifupi 2,200 a kusekondale amagonera ndipo anapeza kuti achinyamata oposa 1,000 sankagona kwa maola okwanira asanu ndi atatu usiku uliwonse.

Ngakhale kuti nthaŵi zambiri zochita za achinyamata zimawasoŵetsa tulo tofunika, “n’kuthekanso kuti achinyamata ena mwina amakhala akudwala matenda ena omwe iwo sawadziŵa,” inatero nyuzipepala yotchedwa Globe. Nyuzipepalayi inanenanso kuti: “Matenda obanika kutulo amagwira ana anayi pa ana 100 alionse, a zaka zoyambira pa 4 mpaka 18.” Akakhala kutulo, njira yodutsa mpweya imene ili kumbuyo kwa m’mero imatha kutsekeka pang’ono kapenanso kutsekekeratu, n’kupangitsa kuti mpweya umene timapuma ulephere kudutsa. Zikatero, ubongo sugwira bwino ntchito yake, ndipo anawa amadzuka ali otopa ndiponso osachedwa kukhumudwa.

Zizindikiro zakuti mwana ali ndi matendaŵa ndi zinthu monga kuliza mkonono kapena kumveka toliralira kukhosi akagona, kumangomva kupweteka mutu m’maŵa uliwonse, ndiponso kuvutika kukumbukira zinthu ndi kusakhala tcheru, komanso kukhala ndi tulo kwambiri masana. Ndi bwino kuti makolo aziti akakhalakhala azimvetsera ana awo akakhala ali m’tulo tofa nato. Dr. Robert Brouillette yemwe ndi katswiri wa matenda a ana pa chipatala cha Montreal Children’s Hospital, ananena kuti mwana amene akudwala matendaŵa angaleke kupuma ali m’tulo, ngakhale kuti pamtima pake pangamagundebe. “Mwanayo amasiya kubanika akadzidzimuka kutuloko kapena akadzuka pang’ono n’kupumako kwa kanthaŵi kochepa kenaka n’kugonanso tulo.” Zoterezi zimatha kuchitika kambirimbiri usiku uliwonse ndipo zikamatero zimam’pangitsa mwana kudzuka ali wotopa kwambiri.

Bungwe lolangiza za kagonedwe kabwino lotchedwa The American Sleep Disorders Association limati ndi bwino kugona m’chipinda chozizira bwino mutazimitsiratu nyali zonse, mopanda zinthu zosokoneza monga ma TV kapena mawailesi. Kugona ndi kudzuka nthaŵi imodzimodzi kungakhale kothandiza kwa ana aang’ono ndiponso achinyamata kuti azigona bwino usiku. Ena amene ali ndi matenda ameneŵa akhala akugwiritsa ntchito kamakina kenakake kamene kamapemerera mpweya m’mfuno ndi m’kamwa kuti kanjira kodutsa mpweya kamene kali kumbuyo kwa m’mero kasatsekeke munthuyo akagona. Katswiri wina wa matenda a ana ananena kuti: “Tulo n’tofunika kwambiri kuposa chakudya chimene timadya. N’tofunika kwambiri kuposa kuchita maseŵera olimbitsa thupi. Tulo timatithandiza kuti thupi lathu lizigwira ntchito bwino, timatithandiza kuganiza bwino ndiponso timatithandiza kukhala ndi chitetezo chokwanira m’thupi mwathu.”