Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinagonjetsa Vuto Langa Losokonezeka Maganizo Nditabereka

Ndinagonjetsa Vuto Langa Losokonezeka Maganizo Nditabereka

Ndinagonjetsa Vuto Langa Losokonezeka Maganizo Nditabereka

Ndikukumbukira nthaŵi ina pamene ndinali kuonerera mwamuna wanga akuseŵera mosangalala ndi kamwana kathu kakhanda kakakazi ndipo mumtimamu ndinkangoti pakanapanda ineyo bwenzi iwo akusangalala kwambiri kuposa mmene ankachitiramo. Ndinkaona kuti ndinasanduka chikatundu cholemera kwa iwowo. Ndinkangofuna nditaloŵa m’galimoto yathu, basi n’kuuyamba ulendo wosabwerera. Sindinkadziŵa n’komwe kuti ndinali nditayamba vuto losokonezeka maganizo limene azimayi ena amakhala nalo akangobereka.

ZAKA khumi zoyambirira ndili m’banja ndinali wosangalala kwambiri. Ineyo ndi mwamuna wanga Jason tinali kulera mosangalala mwana wathu woyamba Liana yemwe ndi wamkazi. Ndiye nditakhalanso ndi pakati pena tonse tinasangalala kwambiri.

Koma mimba imeneyi inali yovuta kwabasi. Ndipotu pang’onong’ono n’kadafa chifukwa cha mavuto ena amene ndinali nawo nditangobereka. Koma zimenezo zisanachitike, nditangotsala pang’ono kubereka, ndinaona kuti maganizo anga ayamba kusakhazikika. Zimenezi zinafika poipa kwambiri titafika kunyumba kuchokera ku chipatala mwana wathu Carly atabadwa. Ndinkangokhala wotopa nthaŵi zonse ndipo ndinkalephera kuganiza pandekha ndikafuna kuchita chinthu, chingachepe motani. Nthaŵi zambiri tsiku lililonse ndinkangomuimbira telefoni Jason ali kuntchito kum’funsa kuti andiuze ntchito yotsatira imene ndiyenera kuchita pakhomo kapena kuti anditsimikizire kuti ntchito inayake imene ndachita ndaichitadi bwino.

Ndinayamba kuopa kucheza ndi anthu ena, ngakhale anzanga enieni. Munthu wina akafika pakhomo pathu mwadzidzidzi, ndinkadzitsekera kuchipinda chogona. M’nyumba ndinkangosiyamo zinthu zitangoti mbwee, ndipo ndinkasokonezeka mosavuta. Munthune ndimakonda kuŵerenga, koma panthaŵiyi sindinkatha n’komwe kuŵerenga chifukwa sindinkatha kuganizira za chinthu chimodzi. Kupemphera nako kunkandivuta, motero thanzi langa lauzimu linayamba kuwonongeka. Maganizo anga anangoti zii, ndipo ndinayamba kudana ndi munthu wina aliyense. Ndinkada nkhaŵa kuti ana anga angakhale pavuto chifukwa chakuti sindinali kuganiza bwinobwino. Ndinayamba kudziona ngati munthu wachabechabe. Ndinkangoti ndipenga basi.

Nthaŵi imeneyo, Jason ankati akabwerako kuntchito ankandithandiza kukonza m’nyumba kapenanso kuphika chakudya cha tonse m’banjamo, koma ineyo ndinkam’psera mtima chifukwa chondithandiza! Ndinkaona ngati kuti akamandithandiza ndiye kuti akufuna kuti ndionekere poyera kuti ndine mayi wosadziŵa ntchito. Komanso akapanda kundithandiza, ndinkamunena kuti sakundiganizira. Jason akanapanda kuchita zinthu mwauchikulire komanso mwachikondi chonchi, vuto langali likanathetsa banja lathu. Bwanji Jason anenepo yekha mmene anavutikira chifukwa cha vuto langali.

Mwamuna Wanga Akusimba Mmene Anavutikira

“Poyamba sindinkamvetsa kuti mkazi wanga Janelle watani makamaka. Anasinthiratu, chifukwatu kale anali munthu wansangala ndiponso wochezeka kwambiri koma tsopano anali kuchita zinthu ngati kuti si iyeyo ayi. Ndikamuuza chilichonse ankangoti ndikumunyoza, ndipo mpaka ankakwiya ndikati ndim’thandizeko ntchito zina. Poyamba, ndinaganiza zoti ndimulumire mano n’kumudzudzula mwamphamvu, koma ndinazindikira kuti ndikatero ndingowonongerawonongera zinthu.

“Tinkangoyambanayambana. Zinkaoneka kuti mkazi wanga Janelle ankaganiza kuti aliyense ankanyansidwa naye. Ndinali nditamva kuti azimayi ena amachita zimenezi akakhala ndi vuto linalake akabereka. Motero nditayamba kum’ganizira kuti akudwala matendaŵa ndinayamba kuŵerenga nkhani zambirimbiri zonena za vutoli. Nkhanizo zinatsimikiziradi zimene ndinali kuganiza. Ndinadziŵanso kuti Janelle sanachitire dala kuti akhale ndi vutoli, ndipo sikuti analekerera penapake ayi.

“Kunena zoona chintchito chomusamalira iyeyo pamodzi ndi ana chinandikulira kwambiri. Kwa zaka ziŵiri ndinalimbana ndi kupita kuntchito komanso kuchita maudindo anga monga mkulu wa mumpingo ndiponso monga mwamuna wokwatira komanso bambo. Mwayi wake ndinasintha nthaŵi yoŵerukira kuntchito kuti ndizifikako pakhomo msanga, makamaka masiku amene timakhala ndi misonkhano yachikristu madzulo. Ndinayenera kukam’thandiza Janelle kunyumba kuti tikonze chakudya chamadzulo komanso tiveke ana nthaŵi isanathe. Choncho tonse tinkakwanitsa kupita kumisonkhano.”

Kuchira Kwanga

Mwamuna wanga akanapanda kundithandiza mwachikondi, ndithu sindikanachira mwamsanga. Jason ankamvetsera mwachifatse ndikamamuuza zinthu zimene zinkandisautsa maganizo. Ndinkaona kuti ndi bwino kwambiri osabisa maganizo anga. Mpaka nthaŵi zina ndimakhala ngati kuti ndikumukalipira. Koma nthaŵi zonse Jason ankanditsimikizira kuti amandikonda ndiponso kuti vutolo linali la tonse. Nthaŵi zonse ankayesetsa kundithandiza kuona kuti zinthu sizinachite kuipa mopitirira muyezo. Ndikanena mawu enaake chifukwa chokwiya pambuyo pake ndinkamupepesa. Ndiye ankandiyankha molimbikitsa pondiuza kuti ndisadandaule popeza kuti ndinanena mawuwo chifukwa cha matendawo. Ndikamaganizira zimenezi, ndimaona kuti kulankhula kwake kwanzeru kunandithandiza kwambiri.

Kenaka tinapeza dokotala womvetsa zinthu kwambiri amene anamvetsera bwinobwino pomuuza mmene ndinkamvera. Anapeza kuti ndinali ndi vuto losokonezeka maganizo limene azimayi ena amakhala nalo akabereka ndipo anati ndi bwino nditalandira mankhwala othandiza kuti ndisamavutike maganizo pafupipafupi. Anandilimbikitsanso kuti ndikalandire chithandizo kwa dokotala wa za matenda okhudza maganizo. Kuphatikizanso apo, anati ndi bwino kuti ndizichitachita maseŵera olimbitsa thupi, amenenso athandiza anthu ambiri kuthana ndi kuvutika maganizo.

Vuto lina lalikulu kwambiri limene ndinakumana nalo nditayamba kuchira linali kuchita manyazi chifukwa cha matenda angaŵa. Nthaŵi zambiri anthu zimawavuta kumvera chifundo munthu amene akudwala matenda amene iwowo samawamvetsa. Vuto la azimayi ena losokonezeka maganizo akabereka silili ngati vuto la kuduka mwendo, lomwe anthu angathe kuliona n’kumamva chisoni. Komabe achibale anga komanso anzanga enieni anandithandiza kwambiri ndiponso anali omvetsetsa.

Achibale Komanso Anzanga Anandithandiza Mwachikondi

Ineyo ndi mwamuna wanga Jason tinayamikira kwambiri zinthu zothandiza zimene amayi anga ankachita panthaŵi yovutayi. Nthaŵi zina, iye ankafuna kupuma n’kuiwalako pang’ono zamavuto amene analipo pakhomo pathu. Komabe nthaŵi zonse amayi anga ankandilimbikitsa ndipo sankayesa kuchita ntchito zanga zonse. M’malo mwake, ankandithandiza n’kundilimbikitsa kuti ndizichita zimene ndikanatha.

Anzathu akumpingo anatithandizanso kwambiri. Ambiri anatitumizira timakalata totiuza kuti anali kundiganizira. Kundilimbikitsa ndi timakalata totere ndinasangalala nako bwanji! Makamaka chifukwa chakuti ndinkavutika kwambiri kulankhula ndi anthu, kaya patelefoni kapena pamaso m’pamaso. Ngakhale kucheza ndi Akristu anzanga misonkhano isanayambe kapena tikamaliza kunkandivuta kwambiri. Motero potilembera makalata, anzathuwo ankasonyeza kuti akuzindikira kuti vuto langalo ndilo linkandilepheretsa kulankhulana nawo bwinobwino komanso ankasonyeza kuti amandikonda ineyo komanso banja langa.

Munthu Sakhala ndi Vutoli Mpaka Kalekale!

Panopo ndikupeza bwino kwambiri chifukwa cha malangizo amene dokotala anandipatsa, chifukwa cha achibale othandiza kwambiri, ndiponso anzanga omvetsa zinthu. Ndimachitabe maseŵera olimbitsa thupi kaŵirikaŵiri, ngakhale ndikamaona kuti ndatopa, chifukwatu maseŵeraŵa andithandiza kupeza bwino. Ndimayesetsanso kumvera zimene ena akundiuza pondilimbikitsa. Zinthu zikandivuta kwambiri ndimamvetsera makaseti a Baibulo ndiponso a ma Kingdom Melodies zimene zili nyimbo zotsitsimula kwambiri zoimbidwa ndi Mboni za Yehova. Zinthu zabwino kwambiri zimenezi zimandilimbikitsa mwauzimu komanso zimandithandiza kuganiza zinthu zothandiza. Posachedwapa ndinafika pokambanso nkhani za ophunzira zochokera m’Baibulo kumisonkhano yampingo.

Zanditengera zaka ziŵiri ndi theka kuti ndifike posonyeza chikondi chenichenidi kwa mwamuna wanga, ana anga ndi anthu ena. Ngakhale kuti banja langa linavutika kwambiri panthaŵiyi, timaona kuti panopo tikugwirizana kwambiri kuposa kale lonse. Makamaka ndimayamikira mwamuna wanga Jason, amene anasonyeza kuti amandikonda kwambiri popirira zonse zimene ndinkachita vuto langa litafika poipa kwambiri, ndi kundithandiza nthaŵi iliyonse imene ndinali kufuna chithandizo. Chachikulu kwambiri n’chakuti tonse aŵiri panopo timam’konda kwambiri Yehova, amene anatilimbikitsadi kwambiri pa mavuto athu.

Ndimavutikabe masiku ena, koma ndimathandizidwa ndi achibale anga, adokotala, anthu akumpingo, komanso mzimu woyera wa Yehova motero sinditaya mtima podziŵa kuti vuto langali lidzatheratu. Inde, anthu sakhala ndi vutoli mpaka kalekale. Tingathe kuligonjetsa ndithu.—Yosimbidwa ndi Janelle Marshall

[Bokosi/Chithunzi patsamba 15]

Zinthu Zimene Zingayambitse Vutoli

Pali zinthu zingapo kuphatikizapo kusintha kwa kayendedwe ka madzi a m’thupi zimene nthaŵi zina zingayambitse vutoli. Nazi zinthuzi:

1. Zimene mayiyo amaganiza pankhani yochembeza, mwina chifukwa chokulira m’mavuto komanso chosaleredwa bwino ndi makolo.

2. Kumangoganizira zinthu zosatheka zimene anthu ambiri amanamiza azimayi kuti ndizo zimene ziwachitikire.

3. Kukhala ndi achibale ena ovutika maganizo.

4. Mavuto a m’banja komanso kusathandizidwa ndi anthu achibale oyamwa bere limodzi kapena achibale ena.

5. Kudziona ngati wopanda ntchito.

6. Kuona kuti chintchito chosamalira ana nthaŵi zonse chimakukulirani.

Apa sikuti tatchulapo zinthu zonse ayi. Palinso zinthu zina zimene zingayambitse vuto losokonezeka maganizo la mayi akangobereka. Inde, zimene zimayambitsa matendaŵa sizimvetsetseka kwenikweni.

[Bokosi patsamba 16]

Sikuti N’kusakhazikika Maganizo kwa Nthaŵi Zonse

Kusokonezeka maganizo kwa azimayi ena akabereka tisakusokoneze ndi kusakhazikika maganizo kwa nthaŵi zonse kumene azimayi ambiri ongobereka kumene amakhala nako. Dr. Laura J. Miller anati: “Vuto lokhudza maganizo lofala kwambiri azimayi akangobereka ndilo kusakhazikika maganizo. . . . Pafupifupi theka la azimayi amene amabereka amakhala ndi vuto longokhala osasangalala limeneli lomwe limawachititsa kulira. Nthaŵi zambiri limafika posautsa kwambiri pakatha masiku atatu kapena mpaka asanu mwana atabadwa ndipo kenaka limayamba kutha lokha pang’onopang’ono pakatha milungu ingapo.” Ofufuza akuona kuti n’kutheka kuti zimenezi zimachitika chifukwa cha kusintha kwa kayendedwe ka madzi a m’thupi kumene kumachitika mzimayiyo akabereka.

Mosiyana ndi vuto limeneli, munthu akakhala ndi vuto la kusokonezeka maganizo akabereka, amavutika kwa nthaŵi yaitali mwina kuyambira panthaŵi imene wangoberekayo kapena mpaka patatha milungu kapenanso miyezi imene. Mayi wongochembeza kumene amene ali ndi vuto limeneli amasangalala kwambiri kwanthaŵi yochepa kenaka n’kuyamba kudandaula kwambiri pasanathe nthaŵi n’komwe mwinanso mpaka kufika pofuna kudzipha. Komanso angakhale wamtima wapachala ndiponso waukali. Angamadzione kuti sakukwanira kukhala mayi ndiponso kuti sakonda mwana wake. Dr. Miller anati: “Azimayi ena odwala matenda ovutika maganizo amadziŵa ndithu kuti ayenera kukonda ana awo, koma amakhala ndi vuto losafuna anawo ndipo amanyong’onyeka, kapenanso kunyansidwa nawo. Ena amaganiza zovulaza kapenanso kupha kumene ana awowo.”

Vutoli silinayambe lero koma n’lakalekale. Kale kwambiri patatsala zaka zopitirira 400 kuti tiyambe zaka za m’nyengo yathu ino dokotala wina wachigiriki dzina lake Hippocrates anaona kuti azimayi ena anali kusintha kwambiri m’maganizo mwawo akangobereka. Nkhani yofotokoza zimene ofufuza anapeza imene inalembedwa m’nyuzipepala ina ya ku Brazil yotchedwa Brazilian Journal of Medical and Biological Research inalongosola kuti: “Vuto losokonezeka maganizo limene azimayi ena amakhala nalo akabereka, ndi vuto lalikulu ndithu limene limagwira azimayi 10 kapena 15 pa azimayi 100 alionse m’mayiko ambiri.” Koma n’zachisoni kuti “ambiri mwa azimayi ameneŵa sawaunika bwinobwino kuti apeze ngati ali ndi vutoli ndipo sapatsidwa mankhwala oyenera,” inatero nyuzipepalayo.

Vuto lina loopsa kwambiri koma limene silichitikachitika mayi akabereka ndi matenda a misala. Odwala matendaŵa amaona zilubwelubwe, amangomva zimawu za anthu m’mutu mwake, ndipo amangoona ngati akulota ngakhale kuti nthaŵi zina angamaganize bwinobwino kwa maola kapena masiku angapo. Zimene zimayambitsa misalayi sizikudziŵika bwinobwino, koma Dr. Miller anati “kutengera magazi oipa, mwinanso kukaphatikizana ndi kusinthasintha kwa madzi a m’thupi, n’kumene kukuoneka kuti makamaka kumachititsa vutoli.” Dokotala wodziŵa bwino matendaŵa angathe kupereka mankhwala othandiza pochiza matendaŵa.

[Bokosi/Zithunzi patsamba 17]

Mmene Mungadzithandizire *

1. Mukapitirira kuvutika maganizo, kaonaneni ndi adokotala. Mukachita zimenezo mofulumira mungathenso kuyamba kuchira mwamsanga. Funani dokotala womvetsa zinthu amene akuwadziŵa bwino matendaŵa. Musachite manyazi ndi matendaŵa kapena kuchita manyazi ndi kumwa mankhwala ngati mukuona kuti muyenera kutero.

2. Chitani maseŵera olimbitsa thupi kaŵirikaŵiri. Ofufuza anaona kuti kuchita maseŵera mokhazikika kumatha kuchiza matendaŵa.

3. Uzani anthu amene ndi anzanu kwambiri mmene mukumvera. Osadzipatula kapena kubisa mmene mukumvera.

4. Kumbukirani kuti simungasamalire nyumba yanu mwakuti n’kukwanitsa zonse zimene mumafuna. Yesetsani kusalira zambiri m’moyo mwanu pomachita zinthu zimene zili zofunika kwenikweni.

5. Pempherani kuti mulimbe mtima komanso kuti mukhale odekha. Ngati mukuona kuti kupemphera kukukuvutani, pemphani munthu wina kuti apemphere nanu. Simungachire msanga ngati mukupitirizabe kumva kuti ndinu wolakwa kapena wopanda ntchito.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 39 Galamukani! siilangiza anthu za chithandizo chilichonse cha mankhwala. Malingaliro amene alembedwa m’nkhani ino okhudza akazi kapena amuna sangagwire ntchito kwa aliyense, ndipo mfundo zina mwina sizingagwire ntchito n’komwe kwa ena.

[Bokosi patsamba 18]

Malangizo kwa Amuna

1. Dziŵani kuti mkazi wanuyo sikuti wachita dala kuti asokonezeke maganizo atabereka. Vuto lakelo likapitirira, m’thandizeni kupeza dokotala amene amadziŵa bwino za vutoli ndiponso amene amamvera ena chisoni.

2. Mvetserani mwachifatse mkazi wanu akamalankhula. Muzimumvetsa akamanena zimene zikum’vutitsa maganizo. Musam’kwiyire chifukwa chokonda kudandaula ndi zilizonse. M’thandizeni mwachifundo kusataya mtima ndipo mtsimikizireni kuti apeza bwino. Musaganize kuti muyenera kuthetsa mavuto onse amene akutchula. Nthaŵi zina amakhala akufuna kum’limbikitsa basi osati kumuuza njira zenizeni zothetsera mavuto akewo. (1 Atesalonika 5:14) Musaiwale kuti, vutoli limachititsa kuti munthu asamaganize molongosoka.

3. Chepetsani kuchita zinthu zosafunika kwenikweni kuti mukhale ndi nthaŵi yambiri yothandiza mkazi wanu. Mukatero iye angathe kuchira msanga.

4. Onetsetsani kuti muzipeza nthaŵi yopuma panokha. Kukhala wathanzi, woganiza bwino, komanso wokonda zinthu zauzimu kungakuthandizeni kuti mum’samale bwino mkazi wanu.

5. Pezani mnzanu woti azikulimbikitsani, mwina mnzanu wokwatira wokhwima mwauzimu amenenso mkazi wake anadwalapo matendaŵa.

[Chithunzi patsamba 18]

Banja la a Marshall