Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Sopo ndi “Katemera Amene Mungadzipatse Nokha”

Sopo ndi “Katemera Amene Mungadzipatse Nokha”

Sopo ndi “Katemera Amene Mungadzipatse Nokha”

“MATENDA oopsa kwambiri omwenso ndi achiŵiri pa matenda amene amapha ana m’dzikoli si malungo, chifuwa cha TB, kapena EDZI. Ndi . . . matenda otsegula m’mimba,” inatero magazini ya The Economist. Komabe, ana ambiri mwa ana amene amafa akanatha kukhala ndi moyo pofika lero ngati iwowo ndi mabanja awo akanakhala kuti ankasamba m’manja ndi sopo nthaŵi zonse.

Ochita kafukufuku a pa sukulu ya zaukhondo ya London School of Hygiene and Tropical Medicine anapeza kuti “kusamba bwinobwino m’manja kungachepetse matenda otsegula m’mimba ndi 43 peresenti,” inatero magazini ya The Economist. “Kusamba m’manja kungathandizenso kwambiri kuchepetsa matenda okhudzana ndi kupuma, amene amapha ana kwambiri kuposa matenda ena onse. Kafukufuku amene anachita pa asilikali ambiri a ku America anasonyeza kuti chimfine ndi chifuwa chinachepa ndi 45 peresenti pamene asilikali ankasamba m’manja mwawo kasanu patsiku.” M’mayiko amene akutukuka kumene mabanja ambiri angathe kugula sopo. N’chifukwa chake, moyenerera sopo akutchedwa kuti “katemera amene mungadzipatse nokha.” Ndipo ndi katemera wosapweteka n’komwe!

Baibulo nalonso limalimbikitsa ukhondo. Lemba la 2 Akorinto 7:1 limati: “Tiyeni tidziyeretse, kusiyana nacho chirichonse chimene chikhoza kudetsa thupi ndi mzimu.” (Chipangano Chatsopano Mu Chichewa Cha Lero) Ngakhale kuti Mulungu amaganizira makamaka za kuyera kwathu kwauzimu, amaonanso ukhondo wa thupi lathu kukhala wofunika kwambiri. (Levitiko, machaputala 12 mpaka 15) N’zoona kuti satiyembekezera kuchita zinthu mopambanitsa. Komabe, tiyenera kukhala ndi chizoloŵezi chosamba m’manja mwathu tikachoka ku chimbudzi, tikasambitsa mwana, kapena tikasintha theŵera lake. Tiyeneranso kusamba m’manja tisanayambe kukonza chakudya kapena kudya, ndiponso pa nthaŵi ina iliyonse pamene zingakhale zotheka kufalitsa tizilombo toyambitsa matenda ta majeremusi kapena mavairasi kwa anthu ena. Mwa kusamba m’manja nthaŵi zonse, timasonyeza chikondi chachikristu ku banja lathu ndi onse amene tingakumane nawo.—Marko 12:31.