Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungalimbane Bwanji ndi Zilakolako Zoipa?

Kodi Mungalimbane Bwanji ndi Zilakolako Zoipa?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Mungalimbane Bwanji ndi Zilakolako Zoipa?

“Pamene ndifuna chabwino, choipa chiliko.”—AROMA 7:21.

MTUMWI Paulo anayesetsa kwambiri kulimbikitsa mfundo zapamwamba zachikristu mwina kuposa mtumwi wina aliyense. (1 Akorinto 15:9, 10) Komabe, iye anavomereza moona mtima mfundo imene ili pamwambapa. Iye anaona kuti panali kulimbana kosatha pakati pa maganizo ake ndi zilakolako zake zoipa. Kodi inunso munamvapo motero monga mmene anamvera mtumwi Paulo? Kunena zoona, monga zolengedwa zopanda ungwiro, ndani wa ife amene sanamvepo kulimbana kotereku mkati mwake?

Kwa anthu ambiri, nkhondo yolimbana ndi zilakolako zoipa ndi yaikulu kwambiri. Ena amalimbana ndi chilakolako chofuna kusangalala ndi kugonana kosayenera. Ena ali mu ukapolo wa chizoloŵezi chotchova njuga, kusuta fodya, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kapena kumwa mowa. Tikakhala ndi zilakolako zowononga ndiponso zoipa, kodi tingalimbane nazo bwanji? Kodi pali thandizo lotani? Kodi nkhondo yolimbana ndi zilakolako zoipa idzatha?

Chikondi N’chofunika Kwambiri Kuti Tilimbane ndi Zilakolako Zoipa

Yesu anatchula malamulo aŵiri aakulu kwambiri a m’Chilamulo cha Mose. Loyamba linali lakuti: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.” (Mateyu 22:37) Ngati tikonda Mulungu monga mmene Yesu anati tiyenera kuchitira, kodi chilakolako chathu chachikulu sichiyenera kukhala kufuna kumukondweretsa? Ngati ndi choncho, chilakolako chabwino chimenechi chingatithandize polimbana ndi zilakolako zoipa ngakhale zitakhala zovuta motani. Zimenezi sizongoganizira chabe. Akristu miyandamiyanda akukwanitsa kulimbana ndi zilakolako zoipa tsiku ndi tsiku. Kodi mungatani kuti mukhale pa ubwenzi wolimba kwambiri wotero ndi Mulungu? Mungatero mwa kusinkhasinkha moyamikira pa zabwino zimene amachita zomwe timaziona m’zinthu zimene analenga, m’Baibulo, ndi mmene amachitira zinthu ndi ifeyo patokha.—Salmo 116:12, 14; 119:7, 9; Aroma 1:20.

Lamulo lachiŵiri lalikulu kwambiri limene Yesu anatchula linali lakuti: “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.” (Mateyu 22:39) Mtumwi Paulo ananena kuti chikondi “sichichita zosayenera” ndiponso kuti “sichitsata za mwini yekha.” Motero, chikondi chopanda dyera choterocho chimatithandiza kupeŵa khalidwe lililonse limene lingavulaze ena. (1 Akorinto 13:4-8) Kodi tingatani kuti tikhale ndi chikondi choterocho? Tiyenera kuganizira kuti anthu enawo akanakhala kuti ndi ife zikanatikhudza bwanji, ndiponso tiyenera kudera nkhaŵa kuchokera pansi pa mtima mmene angamvere mumtima mwawo ndiponso mmene zingakhudzire moyo wawo kwa nthaŵi yaitali.—Afilipi 2:4.

Kodi Pali Thandizo Lotani?

Chifukwa chakuti Mulungu amamvetsa mmene zimativutira kuchita zabwino, wapereka thandizo m’njira zosiyanasiyana. Kudzera m’Mawu ake olembedwa, Baibulo, iye amatiphunzitsa kudana ndi zinthu zoipa ndi kukhala ndi mtima womulemekeza. (Salmo 86:11; 97:10) M’Baibulo muli mbiri za miyoyo ya anthu ena zimene zimasonyeza zinthu zopweteka zimene zimachitika munthu akagonjera zilakolako zoipa. Kuwonjezera pamenepo, Yesu ananena kuti Mulungu adzatipatsa mzimu Wake, womwe ndi chinthu champhamvu kwambiri m’chilengedwe chonse, ngati tim’pempha kuti atipatse. (Luka 11:13) Ungatilimbikitse kuti tipitirize kufuna kuchita zinthu zabwino. Thandizo lina n’lakuti tingalimbikitsidwe ndi Akristu ena omwe nawonso akulimbana ndi zilakolako zoipa. (Ahebri 10:24, 25) Pamene zinthu zothandiza zimenezi ziloŵa m’malo mwa zilakolako zoipa, timathandizidwa pankhondo yathu yofuna kuchita chabwino. (Afilipi 4:8) Kodi zimenezi zimathandizadi?

Tamvani za Fidel yemwe ankadziŵika m’dera limene ankakhala kuti anali chidakwa. Akaledzera, ankasuta fodya, kutchova njuga, ndiponso ankamenyana ndi ena. Kuphunzira Baibulo ndi kucheza ndi Mboni za Yehova kunamuthandiza kugonjetsa makhalidwe amenewo. Masiku ano, iye ali ndi moyo wabwino pamodzi ndi mkazi wake ndi ana awo aŵiri.

Munthu wina angafunse kuti, ‘Koma bwanji ngati ndabwereza zoipa zija?’ Mtumwi Yohane anafotokoza zimene tingachite ngati zitatero. Analemba kuti: “Tiana tanga, izi ndikulemberani, kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, Nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama; ndipo Iye ndiye chiwombolo cha machimo athu; koma wosati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.” (1 Yohane 2:1, 2) Inde, nsembe ya Yesu imaphimba zolakwa za munthu amene walapa ndipo akuyesetsa ndi mtima wonse kuti asinthe pofuna kusangalatsa Mulungu. Poona zimene Mulungu waperekazi, kodi munthu angakhale ndi chifukwa chomveka chogonjera pankhondo yofuna kuchita chabwino?

Zilakolako Zoipa Zidzathetsedwa

Ngati tikonda kwambiri Mulungu ndiponso anthu anzathu ndiponso kugwiritsa ntchito thandizo limene Mulungu wapereka, ngakhale pakalipano tingapambane pa nkhondo yathu yolimbana ndi zilakolako zoipa. Ndiponso, Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti nkhondo imeneyi sidzapitirira mpaka kalekale. Posachedwapa, amene amagwiritsa ntchito zinthu zauzimu zimene Mulungu wapereka adzachiritsidwa kotheratu, m’thupi lawo ndiponso pa moyo wawo wauzimu. (Chivumbulutso 21:3-5; 22:1, 2) Adzamasuka ku uchimo ndiponso ku imfa imene uchimowo umabweretsa. (Aroma 6:23) Koma amene amafuna kukhutiritsa zilakolako zawo zoipa ndiponso zowononga sadzalandira nawo madalitso amenewo.—Chivumbulutso 22:15.

N’zokhazika mtima pansi kudziŵa kuti sitidzalimbana ndi zilakolako zoipa mpaka kalekale. Zidzachotsedwa kotheratu ndipo sizidzayambiranso. Tidzakhaladi pa mpumulo nthaŵi imeneyo.