Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chakudya Chochokera M’dimba Lanu

Chakudya Chochokera M’dimba Lanu

Chakudya Chochokera M’dimba Lanu

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU CENTRAL AFRICAN REPUBLIC

M’MAYIKO ambiri, chimene anthu amada nacho nkhaŵa kwambiri ndi mmene angapezere chakudya cha mabanja awo. Kukwera mtengo kwa ndiwo zamasamba nthaŵi zambiri kumachititsa kudyetsa banja kukhala kovuta kwambiri. Ngakhale zili choncho, anthu ena apeza njira yothandiza yomwe ndi kulima chakudya chawo.

Mwina mungafune kuyamba kulima kadimba kanu. N’zoona kuti, mwina simungakhale ndi malo okwanira pa khomo lanu, koma mwina pali malo ena pafupi amene mungakonze kuti muzilimapo. Tangoganizani za ndalama zonse zimene mungasunge mutamalima chakudya chokoma ndi chopatsa thanzi! Kulima dimba kungakhale njira ina imene mungamalimbitsire thupi. Kulima dimba kungakhalenso ntchito ya banja imene ana anu angaikonde. Kunena zoona, kulima dimba kumaphunzitsa zinthu. Kumaphunzitsa makhalidwe monga kuleza mtima. (Yakobo 5:7) Kuwonjezera apo, kuona zinthu zikukula kungakuchititseni kuyandikira kwambiri kwa Mlengi wa zinthu zonse zabwino.—Salmo 104:14.

Ngakhale zili choncho, musaganize kuti kulima chakudya chanu n’kosavuta kapena kuti mudzapeza zinthu mofulumira. Komabe, khama ndi kudziŵa pang’ono zimene mungachite zingakuthandizeni.

Banja Lina Linakwanitsa Kulima Dimba Lawo

Tiyeni tione chitsanzo cha Timothée ndi Lucie, banja lachikristu la ana aŵiri limene limakhala ku Bangui, likulu la dziko la Central African Republic. Banjali linaona kuti kuyamba kulima dimba lawo kunali kothandiza ndiponso njira yabwino yosungira ndalama zochepa zimene amapeza.

Pamene Lucie anali ndi zaka 13, ankalima kadimba kakang’ono pafupi ndi nyumba yawo. Ankalima kadimba kameneka akaŵeruka kusukulu ndi kumapeto a mlungu. Ankasangalala kuona mbewu zikukula. Komabe, patapita zaka m’pamene anakhala ndi maganizo oyamba kulima dimba la banja lake. Anakonza zogwiritsa ntchito malo omwe anali pafupi amene ankatayapo zinyalala. Lucie anaona kuti malo amenewo akanatha kulimapo. Mmalo mongowasiya malowo kuti azingokhala, zinyalala zimene zinali zitawolerana kwa zaka zambiri zinasanduka nthaka imene akanaigwiritsa ntchito polima zakudya. Lucie ndi Timothée anaganiza zosandutsa malo amenewo kukhala dimba lopindulitsa.

Mmene Anayambira

Komabe, poyamba anafunika kufufuza. Anakambirana ndi anthu ena amene amadziŵa za kalimidwe ka ndiwo zamasamba ndipo anamvetsera mwachidwi. Chifukwa chakuti malowo ankafunika kuthirira, anaphunzira ngakhale mmene angakumbire chitsime chawo. Chinanso chimene chinawathandiza ndi kuŵerenga mabuku okhudza za kalimidwe ka mbewu zakudimba.

Anaŵerenga za mmene mbewu zina zimakhudzira kakulidwe ka mbewu zinzake, ndipo anaphunziranso kuti mbewu zina zimathandiza mbewu zinzake kuti zikule. Komabe, mbewu zina zimalepheretsa mbewu zinzake kukula. Ena amati n’zothandiza kwambiri kudzala kaloti ndi tomato pamodzi m’dimba la ndiwo zamasamba. N’chimodzimodzinso kudzala mbewu ya celery ndi cauliflower pamodzi. Mbewu zimenezi zimathandizana. Ndipo mbewu ya dill ndi “bwenzi” la nsawawa, nkhaka, letesi, ndi anyezi. Koma, mbewu ya green lettuce ndi mbewu ya parsley sizikula bwino zikakhala pamodzi. Anyezi amawononga nyemba zaziŵisi ndi nsawawa. Ngati mbewu zimawononga mbewu zinzake, mbewu zinazo zimafooka ndipo zimaloŵedwa tizilombo towononga mosavuta.

Timothée ndi Lucie anaphunziranso kuti sichinali chinthu chanzeru kulima mbewu imodzi padimbapo. Ngati mbewuyo ikanagwidwa tizilombo kapena matenda, sakanaphulapo kanthu. Kudzala mbewu zosiyanasiyana zimene anazisankha bwino kunawathandiza kuchepetsa vuto limenelo. Zitsamba ndi maluŵa zinachititsa kuti dimba lawo likhale losangalatsa ndiponso lokongola. Maluŵaŵa ankakopa njuchi ndi tizilombo tina tofunika ku mbewuzo.

Banja limeneli linapezanso njira zopeŵera mankhwala a poizoni opopera pa mbewu zawo. Anaphunzira kuti kungodzala adyo kungathandize kuti m’dimba musakhale tizilombo tina. *

Panafunika ntchito yamphamvu ndi kuleza mtima, koma tsopano Timothée ndi Lucie ali ndi dimba losangalatsa kwambiri. Amalima kabichi, parsley, tomato, kaloti, nkhaka, ndi mabilinganya ndipo nthaŵi zina amapeza chakudya chochuluka kuposa chimene banjalo lingathe kugwiritsa ntchito!

Limani Dimba Lanu!

Komabe, si ku Africa kokha kuno kumene anthu ambiri atulukira kufunika kokhala ndi dimba lawolawo. Mwachitsanzo, ku Germany, kuli timadimba ta m’tauni timene amachita kuwagaŵira. Nthaŵi zina timatchedwa kuti Schrebergaerten (kuchokera ku dzina la m’Jeremani yemwe anali katswiri wa za mbewu wotchedwa Daniel von Schreber). Timadimba timeneti ndi timagulu ta malo ang’onoang’ono (amene kukula kwake amakhala pakati pa masikweya mita 200 ndi 400) timene amachititsa lendi kwa anthu okhala mu mzinda. Malinga ndi zimene wochita kafukufuku wina ananena, timadimba ting’onoting’ono timeneti “timathandiza kwambiri kupeza zipatso ndi ndiwo zamasamba.” Timadimba timeneti timakhalanso ngati “paradaiso” kwa olimawo ndipo ndi malo amene amagwirako ntchito ndiponso otherako nthaŵi.

Baibulo limalonjeza kuti tsiku lina posachedwapa, dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso weniweni. (Luka 23:43) Komabe, pakadali pano, mwina mungapeze kachigawo ka malo n’kumapeza chakudya pa kadimba kanu kakang’onoko.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Kuti mudziŵe njira zopeŵera tizilombo ta m’dimba mosagwiritsa ntchito mankhwala opopera, onani nkhani yakuti “Gardening the Organic Way,” mu Galamukani! yachingelezi ya March 22, 2002.

[Chithunzi patsamba 18]

Timothée ndi Lucie akutunga madzi okathirira dimba lawo

[Chithunzi patsamba 18]

Dimba lochita kugaŵiridwa ku Munich, Germany