Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zomera N’zothandiza Kwambiri Popanga Mankhwala

Zomera N’zothandiza Kwambiri Popanga Mankhwala

Zomera N’zothandiza Kwambiri Popanga Mankhwala

Akatswiri ambiri amati pafupifupi gawo limodzi mwa magawo anayi a mankhwala onse amakono a kuchipatala amene anthu amadalira anayamba kuwapanga ndi zomera zokhazokha kapena posakaniza zomera ndi zinthu zina. Kaŵirikaŵiri mfundo imeneyi amaitchulatchula ndi anthu amene amalimbikitsa za mankhwala a zitsamba.

Kafukufuku wambiri wokhudza zomera zopangira mankhwala amene akuchitika makamaka ndi wokhudza zongochotsa m’chomera mankhwala omwe akufunikawo. Chitsanzo chodziŵika bwino choterocho ndi cha asipulini, yemwe amamupanga kuchokera ku zinthu zopezeka m’makungwa a mtengo wotchedwa white willow.

Amati akangochotsa mankhwala ofunikawo m’chomera chinachake, mankhwalawo angathe kuperekedwa kwa wodwala mu miyezo yoyenerera ndiponso yokwanira bwino. Buku lina limati: “N’zovuta kwambiri kuti munthu adye makungwa a mtengo wa willow okwanira mlingo woyenera wa asipulini kapena kuti adye chitsamba chotchewa foxglove chokwanira mlingo wa mankhwala a dijitalisi omwe amachiza bwino anthu n’kuti munthu amwe mankhwalawo atapangidwa mapilitsi.”

Komabe, kuchotsa mankhwala amene akufunika okhawo m’chomera chinachake kulinso m’poipira pake. Mwina n’kutheka kuti kuchita zimenezo kungachititse kuti zinthu zinanso zofunikira m’thupi zimene zili m’chomeracho zingowonongeka. Chinanso n’chakuti, majeremusi ena amene amayambitsa matenda ayamba kusamva mankhwala olimbana nawo.

Mankhwala a kwinini, omwe amawapanga kuchokera ku makungwa a mtengo wotchedwa cinchona, ndiwo chitsanzo cha kuipa kongochotsa m’chomera chinachake mankhwala amene akufunika okhawo. Ngakhale kuti mankhwala a kwinini amapha tizilombo tambiri kwabasi timene timayambitsa malungo , tizilombo tina totere timene mankhwalawo alephera kupha timaswananso kwabasi mpaka kufikanso pochuluka ngati tomwe tija timene taphedwa. Buku lina limafotokoza kuti: “Madokotala ayamba kuda nkhaŵa kwambiri ndi kusamva mankhwala kotereku.”

[Zithunzi patsamba 31]

Asipulini amamupanga kuchokera ku mtengo uwu wotchedwa white willow

[Mawu a Chithunzi]

USDA-NRCS PLANTS Database/Herman, D.E. et al. 1996. North Dakota tree handbook

[Zithunzi patsamba 31]

Mtengo wa cinchona, ndi womwe amapangira mankhwala a kwinini

[Mawu a Chithunzi]

Mwachilolezo cha Satoru Yoshimoto