Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Vuto la Kugona Tulo Tosakwanira Likukulirakulira?

Kodi Vuto la Kugona Tulo Tosakwanira Likukulirakulira?

Kodi Vuto la Kugona Tulo Tosakwanira Likukulirakulira?

ANTHU ochuluka zedi masiku ano akusoŵa chinthu chimenechi. Galimoto zawo zimatha kuchita ngozi ndipo ntchito ngakhalenso mabanja awo amawonongeka chifukwa chosoŵa chinthu chimenechi. Kusoŵa chinthu chimenechi kungawawonongerenso kwambiri moyo wawo, ndipo kungathenso kuufupikitsa. Kumafooketsa mphamvu zoteteza thupi lawo motero thupilo limatha kugwidwa mosavuta ndi matenda osiyanasiyana. Matenda a mitundumitundu monga matenda a shuga, mtima, matenda a kunenepa kwambiri, ndi matenda ena amayenderana ndi kusoŵeka kwa chinthu chimenechi. Koma ambiri mwa anthu osoŵa chinthuchi sadziŵa n’komwe.

Chinthu chimene anthu akusoŵachi ndicho tulo tokwanira. Munthu amene wagona tulo tosakwanira ndi munthu amene sanagone tulo tabwino tofunika kuti munthu akhale wathanzi. Zimenezi zingachitike ngati munthu akuchita kufuna dala kuti asagone chifukwa cha zimene amachita m’moyo wake kapena osati mochita kufunira dala koma chifukwa cha vuto losoŵa tulo lomwe limabwera chifukwa cha matenda ena.

Ofufuza zamatenda amanena kuti padziko lonse, anthu akugona tulo topereŵera ndi ola limodzi usiku uliwonse. Mwina mungaone kuti ola limodzi lokha lilibe kanthu, komatu kuphatikiza pamodzi, anthu onse amapereŵedwa maola 6 biliyoni padziko lonse usiku uliwonse. Zimenezi zachititsa kuti anthu afufuze kuti aone za matenda osiyanasiyana okhudza tulo komanso mmene matendaŵa amakhudzira moyo wathu.

Kale munthu akamasoŵa tulo kwambiri azachipatala ankangoti ali ndi nthenda ya kusoŵa tulo basi. Komano bungwe lokhazikitsidwa ndi Nyumba ya Malamulo ya m’dziko la United States linapeza kuti pali matenda 17 osiyanasiyana okhudza tulo. Komanso nthenda ya kusoŵa tulo imayamba pa zifukwa zosiyanasiyana moti nthaŵi zambiri imatengedwa ngati chizindikiro cha matenda ena, monga mmene kutentha thupi kumasonyezera kuti munthu akudwala matenda enaake.

Kusoŵa tulo ngakhale mwa apo ndi apo n’koopsabe kwambiri. Chitsanzo cha zimenezi ndi munthu wina dzina lake Tom. Ngakhale kuti iyeyu ndi dalaivala wodziŵa bwino kwambiri ntchito yake, nthaŵi ina anapezeka kuti chithiraki chimene anali kuyendetsa chaphonya msewu n’kukawomba chibumi m’mbali mwa msewu, moti asidi wokwana malita 400 amene chigalimotochi chinatenga anataikira mumsewu waukuluwu. Tom anavomereza kuti: “Ndimagona.” Atafufuza m’misewu iŵiri ikuluikulu ya ku United States anapeza kuti madalaivala oyendetsa galimoto tulo tili m’maso ndiwo anachititsa theka la ngozi zonse zoopsa.

Taganiziraninso kuopsa kogwira ntchito ndi munthu amene ali ndi tulo m’maso. Wofufuza wina wa ku Australia, Ann Williamson anati: “[Anthu oyesedwa pa kafukufukuyu] anatha maola pakati pa 17 mpaka 19 osagona kenaka n’kuwayesa pa zinthu zosiyanasiyana, ndipo kunapezeka kuti pa zinthu zina zimene anayesedwapo iwowo sankasiyana ndi munthu womwa mowa wambiri.” Kutanthauza kuti anthuwo ankachita zinthu ngati munthu amene wamwa moŵa kwambiri moti wachita kufika kapenanso kupitirira pa mlingo woyenerera wa kamwedwe ka moŵa umene malamulo a mayiko enaake amalola kwa oyendetsa galimoto! Popeza kuti chaka n’chaka kumachitika ngozi zosaŵerengeka za galimoto ndiponso za pantchito chifukwa cha tulo, ntchito komanso mabanja zikuwonongeka padziko lonse. *

Kodi ndi zinthu zotani zimene zingachititse vuto la kugona tulo tosakwanira? Chinthu chimodzi ndicho moyo wamasiku anowu wokhala ndi zochitikachitika tsiku lililonse, masana ndi usiku womwe. Magazini yotchedwa USA Today inalongosola kuti “moyo umenewu watiwononga kwambiri anthufe,” ndipo inatinso “makono kwabwera malonda ndiponso ntchito zimene siziona kuti masana ndi nthaŵi yogwira ntchito ndipo usiku ndi nthaŵi yogona.” M’mayiko ambiri anthu amaonerera mapulogalamu oonetsedwa usiku wonse pa TV ndipo amatsegula Intaneti panthaŵi yogona. Ndiye palinso vuto la matenda osiyanasiyana osokoneza anthu maganizo, amene makamaka amakhala okhudzana ndi nkhaŵa zomwe zimachuluka chifukwa cha maganizo ndiponso moyo wochulukidwa kwambiri moti n’kumachita kusoŵa popumira. Chotsirizira n’chakuti pali matenda osiyanasiyana amene amatha kum’pangitsa munthu kusagona tulo tokwanira.

Madokotala ambiri amanena kuti n’zovuta kwambiri kuthandiza odwala awo kuti azindikire kuopsa kosagona tulo tokwanira. Dokotala wina anadandaula kuti anthu ena amaona kuti kutopa kwambiri n’chinthu “chopatsa ulemu.” Ndiponso popeza kuti zimatenga nthaŵi ndithu kuti vuto lawo lifike poonekera kuopsa kwake, anthu ambiri amene ali ndi vuto losagona mokwanira sazindikira n’komwe kuti akudwala matenda aakulu osoŵa tulo. Anthu ambiri amangoti, ‘kungoti munthune ndikukalamba’ kapena amati, ‘ndimachulukidwa kwambiri moti nthaŵi zina ndimangozindikira kuti tulo tanditenga’ kapena amati ‘ndimakhala wotopa nthaŵi zonse chifukwa chakuti sinditha kupeza nthaŵi yokwanira yopuma bwinobwino.’

N’kovuta kwambiri kuthetsa vuto limeneli losagona tulo tokwanira. Koma kumvetsetsa mmene tulo tabwino timakhalira ndi kuphunzira mmene mungadziŵire zizindikiro zosonyeza kuti simukugona tulo tokwanira kungakulimbikitseni kuti musinthe. Kudziŵa zizindikiro za nthenda yaikulu ya tulo kungathe kupulumutsa miyoyo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Akuti kutopa ndiko kunachititsa ngozi zambiri zoopsa m’zaka za m’ma 1900. Onani Galamukani! ya February 8, 2001, tsamba 17.

[Chithunzi patsamba 22]

Kusoŵa tulo ngakhale mwa apo ndi apo kungachititse ngozi zoopsa kwambiri