Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Njira ya Anthu Pofunafuna Mulungu”

“Njira ya Anthu Pofunafuna Mulungu”

“Njira ya Anthu Pofunafuna Mulungu”

Nkhani ya mkonzi m’nyuzipepala ya Excelsior ku Mexico City yomwe inatuluka pa September 25, 2002, inali ndi mutu umene uli pamwambawu. Analemba nkhaniyo ndi Carlo Coccioli, katswiri wamaphunziro ndiponso wolemba wodziŵika kwambiri ku Mexico. Nkhani yake inayamba ndi mawu otsatiraŵa.

“Ndangomaliza kuŵerenga, kapena ndinene kuti kuŵerenganso, kaya m’mawu abwino kubwerezabwereza kuŵerenga buku laling’ono lofiira lapadera kwambiri koma osati buku laling’ono lofiira limene linali lotchuka m’masiku a Mao Tse-tung. Buku limeneli [Mankind’s Search for God *] ndi buku lapadera kwambiri ndipo anthu sadzasiya kuliŵerenga, kusiyana ndi ‘Buku Laling’ono Lofiira’ la Mao Tse-tung limene anthu sakuligwiritsiranso ntchito. Mwachidule, buku limeneli, ndi mphatso ya Mboni za Yehova ku dzikoli. Poyerekeza ndi mabuku ambiri, ndi laling’ono, koma lili ndi nkhani zofunika kwambiri. Likhoza kukwana m’thumba, koma ngati mutalipeza mu laibulale ya mabuku 90,000 osiyanasiyana, n’kutheka kuti likhoza kukhala buku lofunika kwambiri kuposa mabuku ena onsewo.”

A Coccioli anapitiriza kufotokoza za nthaŵi imene anali mnyamata pamene anasankha ntchito yoti adzagwire. Anafotokoza kuti: “Maphunziro apadera amene ndinasankha kuti ndikaphunzire ku yunivesite anali ogwirizana ndi nzeru zanga ndiponso zimene ndinkakonda pa moyo wanga: zachipembedzo, makamaka zipembedzo za mayiko a kummaŵa.” Anati maphunziro a zachipembedzo ankawachititsa chidwi kwambiri ndipo nthaŵi ya nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, analandira digiri yapamwamba ya maphunziro a zachipembedzo ameneŵo.

Anafotokoza kuti: “Ndikuona kuti sindikulakwitsa kunena kuti buku laling’ono lofiira limene ndinalandira lili ndi mfundo zazikulu zomveka ndiponso zofunika kwambiri pa nkhani yovuta kumvetsa ya chipembedzo. . . . [Bukuli] liyenera kupezeka m’nyumba iliyonse kuti aziliŵerenga, mobwerezabwereza. Silinena kuti munthu alowe chipembedzo chinachake, koma limangofotokoza chikhalidwe cha anthu amene mitima yawo imakonda kufufuza zinsinsi za Mulungu.”

Kumapeto kwa nkhani yawo, a Coccioli anapereka nambala ya telefoni ya munthu wa Mboni amene anawapatsa bukulo. Kuchokera pa nthaŵiyo munthu wa Mboniyo wakhala akulandira matelefoni oitanitsa bukuli, moti ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Mexico yaonetsetsa kuti onse amene akufuna buku la Mankind’s Search for God alilandira. Munthu wina amene anaitanitsa mabuku 20 oti agaŵire abale ake ndi anzake akulimbikira kwambiri kuphunzira Baibulo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Buku limeneli sanalimasulire m’Chichewa. Mabuku amene asindikizidwa posachedwapa ali ndi chikuto chofeŵa ndipo alibe chikuto chofiira.