Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chinthu Chabwino Koposa Kusintha Kotereku

Chinthu Chabwino Koposa Kusintha Kotereku

Chinthu Chabwino Koposa Kusintha Kotereku

MTENGO ukamabala zipatso zachabechabe, sungakonzeke poudula nthambi zingapo chabe. Koma mtengo wonsewu uyenera kudulidwa, mitsitsi yakenso kuizula, n’kudzalapo mtengo wina wobala zipatso zabwino.—Matthew 7:16-20.

Motero, ngakhale anthu a mtima wofunadi kusintha zinthu amangolimbana n’kuthetsa mavuto owonekera pamwamba basi, monga ziphuphu, kusoŵa chilungamo, umphaŵi, ndi umbava. Komatu mavutoŵa amachokera patali kwambiri. Chofunika kusintha ndi kayendetsedwe ka dziko lonseli. Zimenezi n’zimene Baibulo limalonjeza.

Ufumu wa Mulungu ndiwo boma la kumwamba limene lidzachite zambiri osati kungosintha zinthu mwa apo ndi apo. Boma limeneli lidzasinthiratu kayendetsedwe ka zinthu zonse zokhudza anthu, ndipo lidzagwirizanitsa anthu onse muulamuliro wake. Bomali lidzakonza zinthu monga zamaphunziro, zantchito, pokhala, chakudya, zaumoyo, ndi zachilengedwe.

Lemba la Salmo 72:12-14 limalongosola mwaulosi zimene Mfumu ya Umesiya idzachitire anthu: “Pakuti adzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, adzapulumutsa moyo wa aumphaŵi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa.”

Koma kuti ziphuphu, kupanda chilungamo, ndi umphaŵi zidzatheretu m’dziko muno, ndithu si boma lokha loyenera kusintha komanso anthu. Motero Ufumuwo udzasonyeza munthu aliyense zoyenera kuchita kuti akhale ndi moyo wosangalatsa komanso wopindulitsa. Baibulo limalonjeza kuti Ufumu wa Mulungu udzathandiza nzika zake zapadziko lapansi kuti zisinthe khalidwe lawo pazokha. Kodi udzachita bwanji zimenezi?

Ufumuwo udzaphunzitsa nzika zake kukhala ndi nzeru za Yehova Mulungu, motero zidzakhala ndi chikhulupiriro ndiponso chikondi. (Yesaya 11:9) Kukonda Mulungu kumachititsa munthu kuchita zinthu kuchokera pansi pamtima. Mwachitsanzo m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, Yesu anakumana ndi Zakeyu, mkulu wa amisonkho yemwe ankawonjezera ndalama ku mitengo ya msonkho umene anthu ankadula pofuna kuti ndalama zinazo zizipita m’thumba mwake. Yesu sanam’chititse manyazi wachikulire waboma wakatangaleyu pofuna kum’siyitsa khalidwe lakelo. M’malo mwake, Yesu anam’thandiza Zakeyu kuzindikira kulakwa kwake ndipo kenaka n’kulapa. Zakeyu anakhudzika mtima chifukwa chozindikira mfundo za umulungu ndiponso chifukwa chokonda Mulungu. Motero anasintha kwambiri.—Luka 19:1-10.

Kodi imeneyi si ndiyo njira yabwino koposa yothetsera mavuto a anthu? Inde, payenera kukhala boma langwiro ndiponso lolungama loti liziyang’anira anthu, komanso munthu aliyense ayenera kukhala wofunitsitsa kusintha zochitika zake. Motero kodi zinthu zikadzafika pamenepa tingadzafunenso kuti zisinthe? Ayi ndithu, chifukwatu Mulungu adzakhala atakonza zinthu zonse n’kukhala zatsopano. Zakalezi zidzachoka.—Chivumbulutso 21:4, 5.

[Zithunzi patsamba 10]

Ufumu wa Mulungu sudzasintha zinthu mwa apo ndi apo ayi, koma udzasinthiratu zinthu zonse

[Chithunzi patsamba 11]

Ali padziko lapansi pano Yesu anathandiza anthu osiyanasiyana kusintha zochitika zawo