Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Tizivutika?

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Tizivutika?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Tizivutika?

“Mulungu akungodzisangalalira kumwambako, n’kungotisiya ifeyo tizivutika pansi pano,” anatero Mary. *

ACHINYAMATA a masiku ano abadwira m’dziko lamavuto kwambiri. Kulikonseko zivomezi zoopsa ndiponso masoka ena achilengedwe akutha anthu. Nkhani zimangokhala za nkhondo ndiponso zigaŵenga. Matenda, chiwawa ndiponso ngozi zikutilanda okondedwa athu. Mary, amene tam’tchula pamwambayu anakumana nazo zoterezi. Mawu ake okhumudwawo anawanena bambo ake atamwalira.

Tikakumana ndi tsoka, si zachilendo kwa anthufe kukhumudwa, kusoŵa pogwira, ngakhale kupsa mtima kumene. Timadzifunsa kuti ‘Kodi tsoka limeneli lachokera kuti?’ ‘Ndalakwanji ine?’ kapena ‘Kodi zatani kuti tsokali lindigwere nthaŵi inoyo?’ Mafunso angati ameneŵa amafuna mayankho ogwira mtima. Koma kuti tipeze mayankho otere, tiyenera kupita kwa anthu oyenerera. Malingana ndi zimene ananena wachinyamata wina dzina lake Turrell, nthaŵi zina “anthufe mtima umatipweteka kwambiri moti timalephera kuganiza bwinobwino.” Choncho, ndi bwino kupeza njira yokuthandizani kuti mtima wanu ukhazikike kuti muthe kuganiza bwinobwino ndiponso mwanzeru.

Kukumana ndi Zosautsa

Ngakhale kuti n’zovuta kuzoloŵera, komatu imfa ndiponso mavuto ndiwo moyowo. Yobu ananena mosapsatira kuti: “Munthu wobadwa ndi mkazi n’ngwa masiku oŵerengeka, nakhuta mavuto.”—Yobu 14:1.

Baibulo limalonjeza dziko latsopano ndipo “m’menemo mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4) Komano dziko labwinoli lisanafike, anthu ayenera kukumana ndi zosautsa zosaneneka. Baibulo limati: “Zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa.”—2 Timoteo 3:1.

Kodi nthaŵi zosautsazi zikhalapo mpaka liti? Ophunzira a Yesu anafunsa funso langati lomweli. Koma Yesu sanawauze tsiku kapena ola lenileni limene dziko lodzaza ndi mavutoli lidzathe. M’malo mwake Yesu anati: “Iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.” (Mateyu 24:3, 13) Mawu a Yesuŵa amatilimbikitsa kuti tiziganizira zam’tsogolo kwambiri. Tiyenera kukonzekera kukumana ndi masautso ambirimbiri chimaliziro chisanafike.

Kodi Mulungu Ndiye Wolakwa?

Kodi n’zomveka munthu akakwiyira Mulungu chifukwa cholola kuti tizivutika? Ayi, n’zosamveka chifukwatu Mulungu analonjeza kuti adzathetsa mavuto onseŵa. Ndiponso n’zosamveka kuloza chala Mulungu kuti ndiye amachititsa zoipazi. Masoka ambiri amachitika mwangozi chabe. Mwachitsanzo, tingoyerekezera kuti chimphepo chagwetsa mtengo ndiye mtengowo wavulaza munthu. Zikatere anthu ena amati ndi mmene Mulungu mwiniwake anakonzera. Komatu Mulungu si amene anagwetsa mtengowo ayi. Baibulo limatithandiza kumvetsa kuti zoterezi zimangochitika mwangozi chifukwa “yense angoona zom’gwera m’nthaŵi mwake.”—Mlaliki 9:11.

Nthaŵi zinanso mavuto amabwera chifukwa chochita zinthu mosaganizira bwino. Ingoyerekezerani kuti kagulu ka achinyamata kakumwa moŵa ndipo kenaka kakupita pa ulendo pagalimoto. Ndiyeno kakuchita ngozi. Kodi pamenepa wolakwa ndani? Mulungu? Ayi ndithu. Izi n’zoziyamba dala chifukwa cha kuganiza kwawo kopereŵera.—Galatians 6:7.

Mwina mungafunse kuti ‘Koma kodi Mulungu alibe mphamvu zokwanira kuthetsa kuvutikaku? Anthu ena okhulupirika a m’Baibulo ankadzifunsanso chimodzimodzi. Mneneri Habakuku anafunsa Mulungu kuti: “Mupenyereranji iwo akuchita mochenjerera, ndi kukhala chete pamene woipa am’meza munthu wolungama woposa iye mwini.” Komabe Habakuku sanapupulume n’kuyamba kuganiza molakwa. Iye anati: “Ndidzayang’anira ndione ngati adzanenanji mwa ine.” Kenaka Mulungu anamulimbitsa mtima kuti pa “nyengo yoikidwiratu” Iye adzathetsa kuvutikaku. (Habakuku 1:13; 2:1-3) Motero tiyenera kuleza mtima, podikirira kuti Mulungu adzathetse kuipa pa nthaŵi yoikika ya Mulunguyo.

Peŵani kufulumira kuganiza kuti mwina Mulungu akuchita kufuna kuti tizivutika kapena kuti iyeyo ndiye akutiyesa. N’zoona kuti mavuto angathe kutiphunzitsa zambiri ndiponso n’zoona kuti Baibulo limati mayesero amene Mulungu amalola kuti tikumane nawo angathe kulimbitsa chikhulupiriro chathu. (Ahebri 5:8; 1 Petro 1:7) Ndipotu anthu ambiri amene anakumana ndi mayesero kapena zosautsa zosiyanasiyana amaphunzirapo kuleza mtima ndiponso chifundo. Koma tisamafulumire kuganiza kuti Mulungu ndiye anachititsa kuti avutike choncho. Kuganiza koteroko kumakhala kuiwala za chikondi ndiponso nzeru za Mulungu. Baibulo limanena mosabisa kuti: “Munthu poyesedwa, asanena, ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu.” M’malo mwake, Mulungu amatipatsa “mphatso ili yonse yabwino, ndi chininkho chili chonse changwiro!”—Yakobo 1:13, 17.

Chifukwa Chimene Mulungu Walolera Zoipa Kuchitika

Nanga kodi zoipazi zimachokera kuti? Musaiwale kuti Mulungu ali ndi om’tsutsa, makamaka “iye wotchedwa mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse.” (Chivumbulutso 12:9) Mulungu anaika makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava, m’dziko lopanda mavuto. Koma Satana anachititsa Hava kukhulupirira kuti zinthu zingamuyendere bwino popanda kulamulidwa ndi Mulungu. (Genesis 3:1-5) N’zomvetsa chisoni kuti Hava anakhulupirira mabodza a Satanawo n’kuchita zinthu zosamvera Mulungu. Naye Adamu anatsatira zomwezo. Mapeto ake? Baibulo limati: “Imfa inafikira anthu onse.”—Aroma 5:12.

M’malo mongothana nako kamtima kosamveraka popha Satana ndi om’tsatira ake, Mulungu anaona kuti ndi bwino kuti papite kaye nthaŵi. Kodi anatero chifukwa chiyani? Chifukwa chimodzi n’chakuti amafuna kuti Satana aonekere kuti n’ngwabodza! Ankafuna kuti umboni upezeke wosonyeza kuti kusamvera Mulungu kumangobweretsa chiwonongeko basi. Kodi zimenezi si ndizo zikuchitika panopa? “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Ndiponso “wina apweteka mnzake pom’lamulira.” (Mlaliki 8:9) Zipembedzo zili ndi ziphunzitso zotsutsana zosiyanasiyana. Makhalidwe a anthu sanaipeko chonchi n’kale lonse. Palibe mtundu wa boma umene anthu sanayesepo polamulira dziko. Anthu amasainira mapangano komanso amapanga malamulo osiyanasiyana, koma zofuna za anthu wamba sizinakwaniritsidwebe. Nkhondo ndiye zimangowonjezera mavutoŵa.

N’zoonekeratu apa kuti m’pofunika kuti Mulungu achitepo kanthu n’kuthetsa zoipazi! Koma zimenezi zidzachitika panthaŵi yake ya Mulunguyo basi. Komano pakali pano ifeyo tili ndi mwayi wapadera wokhala mbali ya ulamuliro wa Mulungu pomvera malamulo ndi mfundo zake zomwe zimapezeka m’Baibulo. Zoipa zikamachitika, tingathe kulimba mtima poyembekezera mosakayikira n’komwe kuti tingathe kudzakhala m’dziko lopanda mavuto.

Simuli Nokha

Tikakumana ndi vuto longokhudza ifeyo patokha timatha kungoyamba kudzifunsa kuti, ‘Ndalakwa chiyani ineyo makamaka?’ Komabe mtumwi Paulo anatikumbutsa kuti si kuti tili ndi mavuto ndife tokha ayi. Iye anati ‘cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zowawa pamodzi kufikira tsopano.’ (Aroma 8:22) Kudziŵa zimenezi kungakuthandizeni kupirira mukakumana ndi mavuto. Mwachitsanzo, Nicole anasokonezeka maganizo chifukwa cha zauchigaŵenga zimene zinachitika pa September 11, 2001, ku New York City ndi ku Washington, D.C. Iye anati: “Ndinagwidwa nthumanzi kwambiri.” Koma ataŵerenga nkhani zosimba zimene Akristu anzake anachita kuti asasauke nazo maganizo zimenezi, mtima wake unakhazikika. * “Ndinazindikira kuti si ine ndekha ndikumva choncho. Chisoni changa chikutha pang’onopang’ono.”

Nthaŵi zina ndi bwino kupeza munthu amene mungamuuze zakukhosi, mwina mayi kapena bambo anu, mnzanu woganiza mwachikulire, kapena mkulu wachikristu. Kuuza zakukhosi munthu wina amene mumamukhulupiririra kungachititse kuti akuuzeni “mawu abwino” okulimbikitsani. (Miyambo 12:25) Mnyamata wina wachikristu ku Brazil anati: “Bambo anga anatisiya zaka naini zapitazo, ndipo ndimadziŵa kuti tsiku lina Yehova adzawaukitsa. Komabe kulemba zinthu zimene zikundisautsa mumtima mwanga kunandithandiza kwambiri. Chinanso, ndinkauza Akristu anzanga zimene zikundisautsa maganizo.” Kodi inuyo muli ndi “bwenzi” lenileni lililonse loti mungaliuze zakukhosi? (Miyambo 17:17) Ndiyetu musazengereze kulandira thandizo lawo lachikondi! Musamachite manyazi kulira kapena kuonetsa pankhope panu mmene mukumvera mumtimamu. Chifukwatu ngakhale Yesu panthaŵi inayake “analira” m’nzake atafa momvetsa chisoni!—Yohane 11:35

Baibulo limatitsimikizira kuti tsiku lina ‘tidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi’ ndi “kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Nthaŵi imeneyi isanafike anthu ambiri abwino azivutika. Koma limbani mtima chifukwa mwadziŵa chifukwa chimene anthu akuvutikira chonchi, ndiponso kuti kuvutikaku kutha posachedwa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Mayina ena tawasintha.

^ ndime 20 Onanani nkhani zotsatizana za mutu wakuti “Kulimba Mtima Panthaŵi ya Zoopsa,” m’magazini ya pa January 8, 2002 ya Galamukani!

[Chithunzi patsamba 14]

Zingakuthandizeni kusabisa mmene mukumvera mumtima mwanu