Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mungathe Kuthetsa Khalidwe Lotaya Mtima

Mungathe Kuthetsa Khalidwe Lotaya Mtima

Mungathe Kuthetsa Khalidwe Lotaya Mtima

KODI mavuto amene mumakumana nawo mumawaona motani? Akatswiri ambiri amakhulupirira kuti munthu amadziŵika kuti ali ndi khalidwe lotaya mtima kapena losataya mtima malingana ndi yankho lake pa funso limeneli. Tonsefe timakumana ndi zovuta zambiri m’moyo wathu ndipo ena zimawachulukira koposa ena. Komano n’chifukwa chiyani zimaoneka kuti anthu ena sachedwa kuiwalako zovuta zawozo ndipo amayambiranso kuyesayesa, pamene ena sachedwa kugonja ngakhale atakumana ndi zovuta zazing’ono chabe?

Mwachitsanzo, ingoyerekezani kuti mukufunafuna ntchito. Motero mukupita kokafunsidwa mafunso oona ngati muli woyenerera ndiyeno akukukanani pa ntchitoyo. Kodi zimenezi zingakukhudzeni bwanji? Mwina mungakhumudwe nazo kwambiri ndipo mungadzione kuti ndinu munthu wokanika, n’kumaganiza kuti, ‘Palibe amene angalembe ntchito munthu ngati ineyo. Zolembedwa ntchito ndingoiwalako basi.’ Mwinanso chifukwa cha zomwezi mungayambe kuona kuti zochitika zanu zonse n’zolephera, n’kumaganiza kuti, ‘Ndine munthu wachabechabe ine. Palibe amene angandione ngati munthu wofunika.’ Maganizo onse otereŵa amasonyeza kutaya mtima.

Kulimbana ndi Khalidwe Lotaya Mtima

Kodi mungalimbane nawo bwanji maganizoŵa? Chinthu choyamba chofunika ndicho kuzindikira kuti muli ndi maganizo otere. Chachiŵiri ndicho kulimbana nawo. Yesani kuganizira zifukwa zina zomveka zimene zachititsa kuti asakulembeni ntchitoyo. Mwachitsanzo, kodi n’zoonadi kuti sanakulembeni chifukwa chakuti palibe amene akanakonda kukulembani ntchito? Kapena kodi n’zotheka kuti pantchitoyo amafuna munthu wodziŵa zinthu zina zimene inuyo simudziŵa?

Mutaganizira mfundo zinazake bwinobwino mungathe kuona kuti maganizo anuwo n’ngokokomeza chabe zinthu. Kodi kukanidwa ntchito kamodzi kokha kumatanthauza kuti ndinu munthu wokanika, moti n’zoona kuti palibiretu zinthu zina m’moyo wanu zimene mumatha kuziyendetsa bwino? Zinthu monga zauzimu, zinthu zokhudza anthu a m’banja mwanu, kapenanso anzanu? Maganizo osathandiza akakufikirani phunzirani kungowakankhira kunkhongo podziŵa kuti inuyo ndi amene mukungowakulitsa m’maganizo mwanumo. Ndiponso kodi mungadziŵedi kuti simudzapezanso ntchito? Pali zina zambiri zimene mungachite kuti musakhale ndi maganizo olefula.

Kuganiza Kwabwino Kofuna Kukwanitsa Zolinga Zanu

Masiku ano tanthauzo la chiyembekezo limene ofufuza anapanga, n’lochititsa chidwi ngakhale kuti n’lopereŵera mwina ndi mwina. Iwowo amanena kuti chiyembekezo chimatanthauza kukhulupirira kuti ukwaniritsa zolinga zako. Monga mmene nkhani yathu yotsatira isonyezere, kwenikweni chiyembekezo chimatanthauzanso zinthu zina zambiri, komano tanthauzo la ofufuzali likuoneka kuti n’lothandiza m’njira zingapo. Kuganizira kwambiri mbali imeneyi ya chiyembekezo kungatithandize kuti tizikhala ndi maganizo abwino, ofuna kukwanitsa zolinga zathu.

Chimene chingatilimbitse mtima kuti tikwaniritse zolinga zathu za m’tsogolo ndicho kukhala ndi chizoloŵezi chopanga zolinga n’kumazikwanitsa. Ngati mukuona kuti mulibe chizoloŵezi chotere, ndi bwino kuganizapo bwino pa zolinga zimene mumapanga. Poyamba, kodi muli ndi cholinga chilichonse chimene mumafuna mutakwanitsa? M’posavuta kumangotanganidwa ndi zochitika zina popanda kuganizirapo kuti n’chiyani makamaka chimene chili chofunika kwambiri pamoyo wathu. Pa mfundo yothandiza yomaona kaye kuti chinthu chofunika kwambiri n’chiti, timapezanso kuti kalekale Baibulo linalondola ponena kuti tiyenera “kusankha zimene zili zofunika kwenikweni.”—Afilipi 1:10, Chipangano Chatsopano Mu Chicheŵa Cha Lero.

Tikatsimikizira zinthu zimene zili zofunika kwambiri kwa ifeyo, sizikhala zovuta kusankha zinthu zofunika kwambiri pamoyo wathu wauzimu, pabanja lathu, kapena pantchito yathu. Komabe ndi bwino kusakhala ndi zolinga zambirimbiri poyamba ndiponso cholinga chilichonse chimene tapanga chizikhala choti tingathe kuchikwanitsa mosavuta. Ngati cholinga chathu chili chovuta kwambiri kukwanitsa, tingathe kufooka n’kugonja. Motero, nthaŵi zambiri zimathandiza kugaŵa zolinga zanu zikuluzikulu m’magawo a zolinga zing’onozing’ono.

“Kanthu n’khama,” anatero akuluakulu akale, ndipotu mawuŵa n’ngoona ndithu. Tikaganizira zolinga zathu zofunika kwambirizo, timafunika kutsimikiza, kufunitsitsadi kuzikwanitsa. Chimene chingatithandize kuti chikhumbo chathuchi chikule ndicho kuganizira ubwino wa zolinga zathuzo ndi mmene zidzatipindulitsire ngati titazikwanitsa. Inde, tidzapeza zovuta zina, koma tiyenera kuona kuti n’zotheka osati ngati kuti n’zosatheka kuzithetsa.

Komanso, tiyenera kuganizira za njira zina zotithandiza kukwanitsa zolinga zathu. Wolemba mabuku wina, C. R. Snyder, yemwe anafufuza kwambiri za phindu la chiyembekezo, anati ndi bwino kuganizira njira zingapo zokwanitsira cholinga chathu. Motero njira imodzi ikakanika, tingathe kuyesa yachiŵiri, kaya yachitatu, n’kumapita m’tsogolo.

Snyder anatinso ndi bwino kuphunzira kudziŵa nthaŵi yosiyira kulimbana n’cholinga chinachake n’kupeza cholinga china choloŵa m’malo mwake. Ngati kukwanitsa cholinga chinachake kukutivuta kwambiri, kudandaula nazo kwambiri kungangotifooketsa. Komano tikakhala n’cholinga china chotheka choloŵa m’malo mwa cholinga chimenecho tingapeze polimbira mtima.

Pankhaniyi, Baibulo lili ndi chitsanzo chothandiza kwambiri. Mfumu Davide anali ndi cholinga choti adzamange kachisi wa Mulungu wake, Yehova. Koma Mulungu anamuuza Davide kuti mwana wake Solomo ndiye adzakhale ndi mwayi wochita zimenezo. M’malo monyanyala kapena kuchita makani atamva zokhumudwitsazi, Davide anangosintha zolinga zake. Ndi mphamvu zake zonse anasonkhanitsa chuma ndiponso zipangizo zimene mwana wake adzafunikire kuti athe kumanga kachisiyu.—1 Mafumu 8:17-19; 1 Mbiri 29:3-7.

Ngakhale ifeyo patokha titakwanitsa kukhala ndi chiyembekezo poyesetsa kukhala ndi maganizo abwino ofuna kukwanitsa zolinga zathu, chiyembekezo chathu chingakhalebe chopereŵera kwambiri. Kodi zingatheke bwanji? Zingatheke chifukwa chakuti masiku ano zinthu zambiri zimene zimatisoŵetsa chiyembekezo ndi zinthu zoti sitingathe kuchitapo kanthu kuti tizisinthe. Kodi tingakhale bwanji ndi chiyembekezo tikamaganizira za mavuto aakulu amene akusautsa anthu, monga umphaŵi, nkhondo, kupanda chilungamo, kuopsa kwa matenda ndiponso imfa?

[Chithunzi patsamba 15]

Kodi akapanda kukulembani ntchito imene mumafuna, mumangofulumira kuganiza kuti simudzapezanso ntchito?

[Chithunzi patsamba 16]

Mfumu Davide anasonyeza kuti anali munthu wololera kusintha zolinga zake