Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chiyembekezo Chodalirika Mungachipeze Kuti?

Kodi Chiyembekezo Chodalirika Mungachipeze Kuti?

Kodi Chiyembekezo Chodalirika Mungachipeze Kuti?

WOTCHI yanu yaima ndipo ikuoneka kuti yawonongeka. Mukuganiza zoikonzetsa ndipo mukupeza kuti pali njira zambirimbiri zoikonzetsera. Onenerera malonda okonza mawotchi angoti mbwee, ndipo ngakhale kuti onsewo akudzitama kuti ndi akatswiri, zonena zawo zina zikutsutsana. Ndiye kodi mungatani ngati mutadziŵa kuti munthu amene mukukhala moyandikana naye ndiye katswiri amene anapanga wotchi yanuyo zaka zambiri zapitazo? Kuphatikizanso apo, mukumva kuti iyeyo angakukonzereni wotchiyo, kwaulere. Kodi pamenepa mungavutikenso n’kuganiza zopita kwina?

Ndiyeno yerekezani wotchiyo ndi mmene chiyembekezo chanu chilili. Ngati mukuona kuti chiyembekezo chanu chikuchepa, monga mmenenso chikuchitira kwa anthu ambiri m’masiku ovuta ano, kodi mungagwire mtengo wanji? Anthu ambiri amanena kuti angathe kuthetsa vuto lotere, koma zinthu zambirimbiri zimene amanena zimakhala zosokoneza ndipo mwinanso zotsutsana kumene. Motero pachiyambi pomwe, bwanji osangopita kwa Iye amene anapanga anthu m’njira yakuti azikhala ndi chiyembekezo? Baibulo limanena kuti iye “sakhala patali ndi yense wa ife.”—Machitidwe 17:27; 1 Petro 5:7.

Tanthauzo Lenileni la Chiyembekezo

Chiyembekezo chotchulidwa m’Baibulo chili ndi tanthauzo latsatanetsatane ndiponso lokhudza zinthu zambiri kuposa tanthauzo limene madokotala, asayansi, ndiponso akatswiri ambiri a zamaganizo amanena. Mawu a chinenero choyamba cha Baibulo amene amamasuliridwa kuti “chiyembekezo” amatanthauza kudikirira mtima uli m’mwamba ndiponso kuyembekezera zabwino. Kwenikweni, chiyembekezo chili mbali ziŵiri. Chili ndi mbali ya chikhumbo chofuna chinthu chinachake chabwino komanso chifukwa chomveka choganizira kuti chabwinocho chichitika. Chiyembekezo cha zinthu zotchulidwa m’Baibulo si cha zinthu zosatheka zimene timangolakalaka chabe ayi. N’chiyembekezo chokhala ndi zifukwa zotsimikizika ndiponso zokhala ndi umboni.

Pa mbali imeneyi, chiyembekezo n’chofanana ndi chikhulupiriro, chifukwa nacho chimayenera kukhala ndi umboni, osati kungokhulupirira zinthu motengeka maganizo ayi. (Ahebri 11:1) Ngakhale zili choncho, Baibulo limasiyanitsa chikhulupiriro ndi chiyembekezo.—1 Akorinto 13:13.

Mwachitsanzo: Mukafunsa mnzanu wapamtima kuti akuthandizeni penapake, mumakhala ndi chiyembekezo chakuti aterodi. Chiyembekezo chotere chili ndi maziko enieni, pakuti mnzanuyo mumamukhulupirira chifukwa chomudziŵa bwino ndipo mwamuonapo akuchita zinthu mokoma mtima ndiponso mowoloŵa manja. Chikhulupiriro ndi chiyembekezo chanu ndi zinthu zoyenderana kwambiri, komabe n’zosiyana. Kodi mungakhale bwanji ndi chiyembekezo chotere mwa Mulungu?

Chifukwa Chokhalira N’chiyembekezo

Mulungu ndiye mwini wa chiyembekezo chodalirika. M’nthaŵi za m’Baibulo, Mulungu ankatchedwa kuti “chiyembekezo cha Israyeli.” (Yeremiya 14:8) Chiyembekezo chilichonse chodalirika chimene anthu ake anali nacho chinkachokera kwa iyeyo, motero Mulunguyo ndiye anali chiyembekezo chawo. Chiyembekezo chimenechi si chinali kungolakalaka zinthu. Mulungu anawapatsa chifukwa chachikulu chokhalira ndi chiyembekezo. Kwa zaka zochuluka, Mulungu anawaonetsa kuti akalonjeza chinthu amachikwaniritsadi. Mtsogoleri wawo, Yoswa ananena mawu aŵa kwa Aisrayeli: “Mudziŵa . . . kuti pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu, sanasoŵapo mawu amodzi.”—Yoswa 23:14.

Patha zaka zambirimbiri mawuŵa atanenedwa ndipo Yehova akusungabe malonjezo ake onse. Baibulo lili ndi malonjezo ambiri a Mulungu ndiponso mbiri yolondola ya mmene anawakwaniritsira. Malonjezo ake aulosi n’ngodalirika kwambiri mwakuti nthaŵi zina amalembedwa ngati kuti anali atakwaniritsidwa kale.

N’chifukwa chake tingathe kunena kuti Baibulo ndi buku la chiyembekezo. Mukamaŵerenga mmene Mulungu wakhala akuchitira ndi anthu, mudzakhala ndi zifukwa zamphamvu zokhalira ndi chiyembekezo mwa Iye. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.”—Aroma 15:4.

Kodi Mulungu Amatipatsa Chiyembekezo Chotani?

Kodi ndi panthaŵi yanji pamene timaona kuti tikufunikira kwambiri chiyembekezo? Kodi si panthaŵi ya imfa? Komabe kwa anthu ambiri, panthaŵi yangati imeneyi, mwachitsanzo panthaŵi imene imfa yawalanda munthu amene amam’konda, m’pamene chiyembekezo chimawathaŵira. Chifukwa amaganiza kuti popeza munthu wafa kale, n’chiyaninso angayembekezere? Imfa sitopa ndipo siyang’ana nkhope. Inde, tingathe kuipeŵa kwa kanthaŵi, koma sitingathe kuigonjetsa. M’pake kuti Baibulo limati imfa ndi “mdani wotsiriza.”—1 Akorinto 15:26.

Motero, kodi tingakhale bwanji ndi chiyembekezo imfa ikationekera? Vesi la m’Baibulo limene limati imfa ndi mdani wotsiriza limanenanso kuti mdaniyu “adzathedwa.” Yehova Mulungu ndi wamphamvu kuposa imfa. Anatsimikiza zimenezi nthaŵi zingapo. Kodi anatero motani? Anatero poukitsa akufa. Baibulo limatchulapo nthaŵi zisanu ndi zinayi zimene Mulungu anaukitsa anthu akufa ndi mphamvu zake.

Modabwitsa, Yehova anapatsa mphamvu Mwana wake Yesu, kuti aukitse Lazaro, mnzake wapamtima amene anali atamwalira kwa masiku anayi. Yesu anachitadi zimenezi ndipo sanazichite mwachinsinsi ayi, koma mwapoyera, pamaso pa anthu ambirimbiri.—Yohane 11:38-48, 53; 12:9, 10.

Mwina mungadzifunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani anaukitsa anthu? Kodi anthuwo sanadzakalambenso n’kufabe ndithu?’ Inde anatero. Komano chifukwa cha nkhani zodalirika za chiukiriro ngati zimenezi, ifeyo sitimangolakalaka chabe komanso tili ndi zifukwa zokhutiritsa zakuti anthu apamtima pathu amene anamwalira adzaukitsidwa. M’chicheŵa china tingati, tili ndi chiyembekezo chenicheni.

Yesu anati: “Ine ndine kuuka ndi moyo.” (Yohane 11:25) Iyeyu ndi amene Yehova adzam’patse mphamvu zoukitsa anthu padziko lonse. Yesuyu anati: “Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu [a Kristu], nadzatulukira.” (Yohane 5:28, 29) Inde, anthu onse amene akugona m’manda angadzaukitsidwe n’kudzakhala padziko lapansi la paradaiso.

Mneneri Yesaya analemba mawu ochititsa chidwi aŵa osimba za chiukiriro: “Akufa ako ali moyo, matupi awo adzaukanso. Iwo akugona m’nthaka adzauka ndi kusangalala; pakuti mame ako ali mame a kuwala konyezimira, ndipo dziko lidzabalanso iwo amene anafa kalekale.”—Yesaya 26:19, The New English Bible.

Kodi zimenezi si zolimbikitsa? Anthu akufa ali pabwino kwambiri, monga mmene mwana amakhalira m’mimba mwa amayi ake. Inde, iwo amene akupuma m’manda akusungidwa bwinobwino m’maganizo a Mulungu Wamphamvuyonse yemwe alibe malire a zinthu zimene angathe kukumbukira. (Luka 20:37, 38) Ndipo posachedwapa adzaukitsidwanso, n’kufika m’dziko la anthu osangalala, omwe adzawalandire ndi manja aŵiri monga mmene banja limalandirira khanda lobadwa kumene! Motero, ngakhale munthu atafa pamakhala chiyembekezo.

Mmene Chiyembekezo Chingakuthandizireni

Paulo anatiphunzitsa zinthu zambiri zokhudza kufunika kwa chiyembekezo. Ananena kuti chiyembekezo ndi chisoti, chomwe ndi mbali yofunika kwambiri ya zida zathu zauzimu. (1 Atesalonika 5:8) Kodi ankatanthauzanji ponena mawu amenewo? M’nthaŵi za m’Baibulo, msilikali akamapita kunkhondo ankavala chisoti chachitsulo, ndipo nthaŵi zambiri m’kati mwake ankavalamo kansalu kapena kachipewa. Chifukwa cha chisotichi, zida zambiri za adani zinkalephera kufika m’mutu n’kumuvulaza msilikaliyo. Ndiye kodi mfundo ya Paulo inali yotani? Chiyembekezo chimateteza maganizo, monga mmene chisoti chimatetezera mutu. Ngati muli ndi chiyembekezo champhamvu chogwirizana ndi zolinga za Mulungu, simungasokonezeke maganizo chifukwa cha mantha kapena kusoŵa pogwira mukakumana ndi mavuto. Kodi tingati alipo amene safunikira chisoti chotere?

Paulo anatchulanso chitsanzo china chosavuta kukumbukira pofotokoza za chiyembekezo chokhudzana ndi chifuno cha Mulungu. Iye analemba kuti: “[Chiyembekezo] chimene tili nacho ngati nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso.” (Ahebri 6:19) Paulo ankadziŵa bwino kufunika kwa nangula chifukwa anali atapulumukapo pa ngozi ya chombo cha m’madzi kangapo. Amalinyero akakumana ndi mafunde ankaloŵetsa nangula pansi pa nyanja. Nangulayo akakafika pansi n’kukakola bwinobwino, ndiye kuti chombocho chimatha kupulumuka chimphepocho m’malo mokaponyedwa m’mphepete mwa nyanja n’kukamenyetseka ku miyala.

Chimodzimodzinso, ngati ifeyo timaona kuti malonjezo a Mulungu ndi chiyembekezo ‘chokhazikika ndi cholimba,’ chiyembekezo chimenecho chingatithandize kulimbana ndi chimphepo cha mavuto a masiku anoŵa. Yehova amalonjeza kuti posachedwapa anthu sadzasautsidwanso ndi nkhondo, uchifwamba, chisoni, ngakhalenso imfa. (Onani bokosi patsamba 10.) Kukhala ndi chiyembekezo chimenechi kungatithandize kupeŵa zinthu zotiika m’mavuto, n’kutipangitsa kukhala ndi mtima wofunitsitsa kugwirizana ndi mfundo zimene Mulungu amatipatsa m’malo motsatira mzimu wachisokonezo, komanso wokonda zoipa womwe wafala kwambiri m’dziko muno masiku ano.

Chiyembekezo chimene Yehova akupereka chimakukhudzaninso inuyo panokha. Iye akufuna kuti muzikhala moyo wangati umene iyeyo ankafuna pachiyambi. Iye amafuna kuti “anthu onse apulumuke.” Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Choyamba aliyense wa anthuŵa amayenera kuti ‘afike pozindikira choonadi.’ (1 Timoteo 2:4) Ofalitsa magazini ino akukulimbikitsani kuti muphunzire choonadi chopatsa moyo chimenechi cha Mawu a Mulungu. Chiyembekezo chimene Mulungu adzakupatseni mukatero n’choposa chiyembekezo chilichonse chimene mungachipeze m’dziko lino.

Ndi chiyembekezo chotere, palibe chifukwa chosoŵera pogwira, pakuti Mulungu angathe kukupatsani mphamvu zimene mukufunikira kuti mukwaniritse zolinga zanu zilizonse zomwe zili zogwirizana ndi cholinga chake. (2 Akorinto 4:7; Afilipi 4:13) Kodi ichi sindicho chiyembekezo chimene mukufunikira? Motero ngati mukusoŵa chiyembekezo, ndipo ngati mwakhala mukuchifunafuna, limbani mtima. Chiyembekezo chilipo. Mungathe kuchipeza!

[Bokosi/Chithunzi patsamba 18]

Zifukwa Zokhalira ndi Chiyembekezo

Malemba aŵa angakuthandizeni kukhala ndi chiyembekezo champhamvu:

Mulungu amalonjeza tsogolo losangalatsa.

Mawu Ake amanena kuti dziko lonse lidzasanduka paradaiso wokhala ndi anthu osangalala ndiponso ogwirizana.—Salmo 37:11, 29; Yesaya 25:8; Chivumbulutso 21:3, 4.

Mulungu sanganame.

Iye amadana ndi bodza la mtundu wina uliwonse. Yehova ndi woyera ndiponso wolungama mopanda malire, motero n’kosatheka kuti aname.—Miyambo 6:16-19; Yesaya 6:2, 3; Tito 1:2; Ahebri 6:18.

Mulungu ali ndi mphamvu zopanda malire.

Yehova yekha ndiye wamphamvuyonse. Palibe chilichonse m’chilengedwe chonse chimene chingamuletse kukwaniritsa malonjezo ake.—Eksodo 15:11; Yesaya 40:25, 26.

Mulungu amafuna kuti mukhale ndi moyo wosatha.

Yohane 3:16; 1 Timoteo 2:3, 4.

Mulungu ali n’chiyembekezo chakuti tichita bwino.

Safuna kuona zophophonya ndiponso zolakwa zathu, koma makhalidwe ndi zochita zathu zabwino. (Salmo 103:12-14; 130:3; Ahebri 6:10) Iye ali n’chiyembekezo chakuti tichita bwino ndipo amasangalala tikaterodi.—Miyambo 27:11.

Mulungu amalonjeza kuti azikuthandizani kukwanitsa zolinga zanu zaumulungu.

Atumiki ake sayenera kumva kuti akusoŵa pogwira. Mulungu amapereka mzimu wake woyera mowoloŵa manja kuti utithandize, ndipotu mzimu umenewu ndi mphamvu yoposa mphamvu ina iliyonse.—Afilipi 4:13.

Simudzakhumudwapo chifukwa chokhala ndi chiyembekezo mwa Mulungu.

Mulungu n’ngodalirika kwambiri, motero sangakukhumudwitseni ngakhale pang’ono.—Salmo 25:3

[Chithunzi patsamba 20]

Chiyembekezo chimateteza maganizo monga mmene chisoti chimatetezera mutu

[Chithunzi patsamba 20]

Monga nangula, chiyembekezo cholimba chingatipangitse kukhala wokhazikika

[Mawu a Chithunzi]

Courtesy René Seindal/Su concessione del Museo Archeologico Regionale A. Salinas di Palermo