Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’kulakwa Kupita ku Malo Ovinira a Achinyamata?

Kodi N’kulakwa Kupita ku Malo Ovinira a Achinyamata?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi N’kulakwa Kupita ku Malo Ovinira a Achinyamata?

“Ndinkapitirako chinthu chimodzi; kukasangalala basi,” anatero Shawn.

“Kunena zoona, zinali zosangalatsa mosasimbika! Tinavina kwambiri, mpaka kuchezera usiku wonse,” anatero Ernest.

MALO ovinirako a achinyamata atchuka m’zaka zaposachedwapa. Achinyamata ambiri ofuna kusangalala sasoŵa kumalo otere.

Inde, tonse timafuna kusangalala. Ndipo Baibulo limanena kuti pali “nyengo ya kuseka” ngakhalenso “nyengo ya kuvina.” (Mlaliki 3:4) Komano kodi kumalo ovinira a achinyamata kumakhala chisangalalo chabwino? Kapena kodi pali zifukwa zomveka zoyenera kuziganizira mofatsa musanapite ku malo otere?

“Mapwando Achipwirikiti”

Ngakhale kuti Baibulo sililetsa mapwando aang’ono bwino, limati “mchezo,” kapena kuti “mapwando achipwirikiti” n’ngofunika kuchenjera nawo. (Agalatiya 5:19-21, Byington) M’nthaŵi za m’Baibulo, mapwando otere nthaŵi zambiri ankachititsa chipwirikiti. Mneneri Yesaya analemba kuti: “Tsoka kwa iwo amene adzuka m’mamaŵa kuti atsate zakumwa zaukali; amene achezera usiku kufikira vinyo awaledzeretsa! Ndipo zeze ndi mgoli, ndi lingaka ndi chitoliro, ndi vinyo, zili m’mapwando awo; koma iwo sapenyetsa ntchito ya Yehova.”—Yesaya 5:11, 12.

Pamapwando otere pankakhala “zakumwa zaukali” ndiponso nyimbo zopokosera. Ankayamba masanasana ndithu ndipo ankafika mpaka usiku. Onaninso kuti anthu opezeka pamapwando otere ankachita zinthu ngati kuti kulibe Mulungu! Motero, n’zosadabwitsa kuti Mulungu analetsa mapwando otere. Komano kodi masiku ano Mulungu amamva bwanji akaona zimene zimachitika m’malo ambiri ovinira a achinyamata?

Taganizirani zimene zimachitikako. Kumalo ena otere amavina mwachiwawa, moduka mutu. Buku lina linati kuvina kotereku “kunayamba m’ma 1985, m’malo ovinira a magulu oloŵerera a achinyamata ku United States. Kenaka kunasintha n’kufika pomavina mogundanagundana.” Povina m’njira imeneyi amadumphadumpha, akugwedeza mutu modzikhutchumula n’kumayerekeza kugundana mitu ngati ziŵeto, komanso kuwombanawombana. Si zachilendo kuthyoka manja kapena miyendo, ndipo ena avulalako msana ngakhalenso mutu. Ena afa kumene. Pali kuvina kwina kumene chigulu cha anthu chimanyamula munthu m’mwamba kupitirira pamitu yawo, n’kumamuyendetsa pamanja awo. Ambiri akhala akuwagwetsa, n’kuvulala. Komanso nthaŵi zambiri atsikana amagwidwa ndi kusisitidwa m’malo osayenerera.

N’zosachita kufunsa kuti Mulungu amadana nawo makhalidwe otere. Ndiponsotu Mawu ake amalamulira Akristu ‘kukana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi ndi kukhala ndi moyo wodziletsa.’—Tito 2:12.

Nyimbo ndi Mankhwala Osokoneza Ubongo

Ganiziraninso, nyimbo zimene zimaimbidwa m’malo ambiri ovinira. M’malo ena amakonda kuika nyimbo za chamba chotchedwa hard rock kapena heavy metal, zomwe zimagunda monyamula mtima ndiponso zimakhala zotukwana. Koma m’malo ambiri otere, amakonda nyimbo za rapu. Nazonso ndi nyimbo zokhudza kugonana, chiwawa, ndi kupanduka. Kodi kumvera nyimbo zoterezi komanso muli pamalo oipa choncho kungakuwonongeni? David Hollingworth, yemwe ndi katswiri wodziŵa bwino za malo ovinirako usiku anati: “Nyimbo zimasokoneza anthu kwambiri. Anthu akakhalapo chigulu, nyimbo zimatha kuwachititsa zinthu zoopsa.” N’zosadabwitsa kuti m’malo ovinira a m’mizinda ingapo ya ku United States mwakhala mukuchitika ziwawa zambiri. Anthu ambiri amaona kuti zimenezi zimachitika chifukwa cha nyimbo zolimbikitsa kuchita zinthu zamanyazi ndiponso zachiwawa. *

M’zaka zaposachedwa, chinanso chimene chafala m’malo ovinira ndicho mankhwala osokoneza ubongo. Wofufuza wina anati “zikuoneka kuti malo ovinira atchuka chifukwa chakuti mankhwala osokoneza ubongo akuchulukako, akupezekako m’mitundu yake yosiyanasiyana, ndiponso akugwiritsidwa ntchito kwambiri . . . ” Ndipotu pali mankhwala ena osokoneza ubongo amene anachita kuwatcha kuti ovinira. Anthu ena amene amapitapita ku malo ovinira amasakaniza mankhwala osokoneza ubongo angapo. Pa mankhwala amene amakonda kusakanizidwa motere pali ketamine amene amatha kuchititsa munthu kupepera, kuzunguzika, kuvutika popuma, ndiponso kuwonongeka ubongo. Mankhwala a mtundu wotchedwa methamphetamine angathe kulepheretsa munthu kukumbukira zinthu, kum’chititsa kukhala wovuta, wachiwawa, mwinanso kumuwononga mtima kapena ubongo. Mankhwala otchuka kwambiri a mtundu umenewu amatchedwa ecstasy. Mankhwalaŵa angachititse munthu kusokonezeka, kukhala ndi nkhaŵa, kugunda kwambiri mtima, kuthamanga magazi, ndiponso kutentha thupi moopsa. Anthu ena afapo nawo mankhwalaŵa.

Kugwiritsa ntchito mankhwala oletsedwa n’kosemphana ndi lamulo la Baibulo lakuti “tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu.” (2 Akorinto 7:1) Motero kodi n’kwanzeru kupita dala kumalo amene kuli anthu a mankhwala osokoneza ubongo?

Mayanjano Oipa

Kumbukirani chenjezo lotsatirali, lomwe limatchulidwatchulidwa: “Mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Monga ankachitira anthu opita ku mapwando achipwirikiti a m’nthaŵi za m’Baibulo, achinyamata ambiri amene amakonda kupita ku malo ovinira, zokondweretsa Mulungu alibe nazo ntchito. Kwenikweni, ambiri mwa iwo tingati ndi anthu “okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.” (2 Timoteo 3:4) Kodi n’zoona kuti inuyo mungafune kugwirizana kwambiri ndi anthu otere?

Ena amaganiza kuti sangadziike pangozi kwenikweni ngati atapita ku malo ovinira ali ndi Akristu anzawo achinyamata. Komabe, achinyamata achikristu amene alidi “chitsanzo kwa iwo okhulupirira . . . m’mayendedwe” sangafune kupita kumalo otere. (1 Timoteo 4:12) Ngakhale gulu la achinyamata achikristu litapita ku malo ovinira n’kukakhaladi pamodzi, sikuti angapeŵe nyimbo zoipa ndiponso malo oipawo ayi. Ngati anzawo atawaitana kuti avine angavutike kukana ndiponso angakhale pachiyeso. Achinyamata ena mpaka apezeka akuchita nawo ndeu! Motero mawu a m’Baibulo aŵa ndi oona: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.”—Miyambo 13:20.

Kuvina Kodzutsa Chilakolako

Ndiyeno palinso nkhani ya mavinidwe. Mavinidwe achilendo atchuka kwambiri pakati pa achinyamata ku United States. Nthaŵi zambiri amavina nyimbo za rapu zomwe zimakhala ndi mawu olaula. Komanso mavinidwewo pawokha amakhala oyerekezera kugonana. Motero, mavinidweŵa anawatcha kuti ‘n’kugonana kosachita kuvula zovala.’

Kodi Mkristu wachinyamata angafune kuvina nawo gule wotere? Sangatero ngati akufuna kukondweretsa Mulungu, amene amatilamula kuti “thaŵani dama.” (1 Akorinto 6:18) Ena angamaganize kuti, ‘zikanakhala kuti n’zolakwika kwabasi si bwenzi anthu ambirimbiri akuzichita.’ Koma dziŵani kuti ngakhale zochita za anthu ambiri zimatha kukhala zolakwika. (Eksodo 23:2) Limbani mtima kukana zofuna za anzanu kuti mukhale ndi chikumbumtima chabwino ndi Mulungu!—1 Petro 4:3, 4.

Kusankha Chochita

Izi sizikutanthauza kuti kuvina kulikonse n’kolakwika. Baibulo limatiuza kuti Mfumu Davide anasangalala kwambiri likasa lopatulika la chipangano atabwerera nalo ku Yerusalemu moti “anavina ndi mphamvu yake yonse.” (2 Samueli 6:14) M’fanizo la Yesu la mwana wosakaza, mwanayo atabwerera, panachitika chikondwerero chimenenso panali “kuimba ndi kuvina.”—Luka 15:25.

Pali kuvina kwina kumenenso Akristu a m’dera lanulo amaona kuti n’kwabwino. Komabe m’pofunika kuchita zinthu mosatayirira ndiponso mwanzeru. Malo abwinodi kumvetsera nyimbo ndiponso kuvina si malo ovinira a achinyamata ayi koma ku mapwando a Akristu kumene sikukhala chipwirikiti ndiponso kumene zochitika zonse zimayang’aniridwa bwinobwino. M’mapwando oyang’aniridwa bwino a Akristu, achinyamata samadzipatula koma amacheza ndi Akristu anzawo a zaka zosiyanasiyana.

Inde, mwina kumene mukukhalako kuli malo odyerako anthu kumene kumakhala nyimbo ndiponso komwe anthu amavina modzilemekeza. Koma musanavomere kupita ku malo aliwonse otere, mungachite bwino kudzifunsa kaye mafunso monga akuti: Kodi malowo ali ndi mbiri yotani? Kodi ndi malo a achinyamata okhaokha? Ngati n’choncho, kodi angakhaledi malo abwino kupitako? Kodi amaimbako nyimbo zotani? Kodi kumeneko amavina motani? Kodi makolo anga akuvomereza kuti ndingathe kupitako? Kudzifunsa mafunso ngati ameneŵa kungakuthandizeni kuti musagwe m’mavuto.

Shawn, amene tam’tchula kumayambiriro uja, ananena mosapita m’mbali. Iyeyu ankakonda kupita ku malo otere asanakhale Mkristu. Iye anati: “Ku malo ovinirako usiku kumachitika zinthu zambiri zotayirira. Nyimbo zake nthaŵi zambiri zimakhala zamanyazi, mavinidwe ake nthaŵi zambiri amakhala onyansa, ndipo anthu ambiri amapitako n’cholinga chimodzi basi, choti akapezeko winawake woti agonane naye.” Shawn anasiya kupita ku malo otere ataphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Iye anapereka malangizo aŵa, mogwirizana ndi zimene anakumana nazo: “Ameneŵa si malo oyenerera Akristu ayi.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Onani nkhani yakuti “Chifukwa Chimene Nyimbo Zimatikhudzira,” m’magazini ya Galamukani! ya October 8, 1999.

[Chithunzi patsamba 26]

Achinyamata ena adziika pachiyeso chifukwa chopita ku malo ovinira