Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Amabadwa ndi Ludzu Lofuna Kuphunzira

Anthu Amabadwa ndi Ludzu Lofuna Kuphunzira

Anthu Amabadwa ndi Ludzu Lofuna Kuphunzira

“Mbalame zimauluka, nsomba zimasambira, munthu amaganiza ndi kuphunzira.”—ANATERO JOHN HOLT, MLEMBI NDIPONSO MPHUNZITSI.

MPHALAPALA yongobadwa kumene imakhala ndi chilakolako chofuna kuimirira ndi miyendo yake yaitali, yosalimba kuti itsatire mayi ake. Koma mwana wa munthu akhoza kutha chaka asanayende. Komabe, anthu anapatsidwa mphatso ya ubongo wochititsa chidwi ndiponso wapamwamba kwambiri poyerekezera ndi ubongo wa nyama ina iliyonse. Timadziŵa kuti anthu alidi ndi ubongo wapamwamba tikaona mmene mwana amakhalira ndi chilakolako chachikulu chofuna kutulukira ndi kudziŵa zinthu zatsopano.

Pofuna kukhutiritsa chilakolako chimenechi, ana athanzi amene akukula bwinobwino amaona kuti chilichonse chowazungulira n’chinthu choti achiyese. Mukawapatsa chinthu chilichonse, amachiyesa pogwiritsa ntchito manja, makutu, mphuno, maso, ngakhale kuchiika m’kamwa kumene. Ndipo kuyesako sikuthera pomwepo. Monga momwe kholo lililonse likudziŵira, ana amapinda zinthu, kuzimenyetsa pansi, kuzigwedeza, ndi kuziphwanya, ndipo nthaŵi zambiri amasangalala kwambiri akamachita zimenezi, pofuna kumvetsetsa zinthu zowazungulira.

Chilakolako chimene ana ali nacho chofuna kudziŵa zinthu chimaonekera kwambiri akayamba kulankhula, ndipo kuti ayambe kulankhulako si ntchito yamaseŵera ayi! Zimaoneka ngati kuti mwadzidzidzi, m’mutu mwawo mumangodzaza mafunso okhaokha. Mafunso monga ‘N’chifukwa chiyani?’ ‘Bwanji?’ ‘Kuti?’ ‘Liti?’ ‘Ndani?’ amatuluka pakamwa pawo mosalekeza, zimene zimayesa kuleza mtima kwa makolo ambiri. John Holt, mlembi tinamutchula kale uja, anati: “Ana amafuna kuphunzira zinthu zambiri panthaŵi yochepa ndipo akafuna kuphunzira chinthu, saletseka.”

Kenaka, pakatha zaka zingapo, ana m’mayiko ambiri amayamba kuphunzira zinthu mwanjira ina, ndipo amayamba kukhala ndi aphunzitsi, mabuku, madesiki, ndipo mwina ana enanso ambirimbiri. Koma n’zomvetsa chisoni kuti akatha zaka zingapo ali pasukulu, achinyamata ambiri sasangalalanso kuti aziphunzira m’njira imeneyi. Ena mpaka amayamba kuona sukulu ngati chinthu chotopetsa kapena chokola. Mwina pali maphunziro kapena aphunzitsi ena omwe sawafika pamtima. Kapena mwina anthu akamawayembekezera kuti azikhoza bwino kusukulu zimawapatsa nkhaŵa yaikulu.

Kusasangalala ndi kuphunzira m’njira imeneyi kungathe kupitirirabe mpaka akakula kapena ngakhale akakalamba, ndipo anthu osasangalala ndi kuphunzira oterowo amapeŵa chilichonse chokhudza kuganiza kwambiri, kuphunzira, kapena kufufuza. Anthu okalamba alinso ndi chinthu china chimene amafunika kulimbana nacho. Chinthu chimenechi ndicho zimene anthu ambiri amakhulupirira zoti munthu akamakalamba sathanso kuphunzira zinthu zatsopano. Koma monga momwe tionere, zimenezo zilibe maziko alionse.

Kodi mukufuna kupititsa patsogolo luso lanu ndi chilakolako chanu chophunzira, kaya muli ndi zaka zingati? Ngati ndinu kholo, kodi mukufuna kuti ana anu aziphunzira bwino ndiponso azisangalala ndi kuphunzira pamene ali pasukulu mpaka m’tsogolo? Ngati ndi choncho, pitirizani kuŵerenga nkhani zotsatirazi.

[Chithunzi patsamba 19]

Ana amakonda kuphunzira

[Chithunzi patsamba 20]

N’zomvetsa chisoni kuti ana ambiri amakhala ndi nkhaŵa yaikulu kusukulu