Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoseŵeretsa Ana Zabwino Kwambiri

Zoseŵeretsa Ana Zabwino Kwambiri

Zoseŵeretsa Ana Zabwino Kwambiri

Kodi mwana wanga ndimupezere zoseŵeretsa zotani? Kodi ndiwononge ndalama zingati? Ngati ndinu kholo, mwina munafunsapo mafunso ameneŵa kambirimbiri. Nkhani yabwino n’njoti, zoseŵeretsa ana zabwino kwambiri zikhoza kukhala zimene zili zotsika mtengo zedi.

Buku lotchedwa Motivated Minds—Raising Children to Love Learning limati: “Ana amapindula kwambiri akamapanga ndi kufufuza okha zinthu m’malo momangoonerera, choncho zoseŵeretsa zosavuta kuseŵera nazo zimene zimafuna kuti mwanayo aziganiza n’zabwino kusiyana ndi magalimoto okwera mtengo oyendera mabatire kapena zidole zolankhula, zimene zimachepetsa zimene mwana wanu angachite.” Zidole zomalizirazi “zikhoza kukhala zosangalatsa poyamba, koma ana sachedwa kutopa nazo chifukwa siziwalola kuyesera kuchita zinthu zina, kufufuza, ndi kupanga zinthu.”

Mogwirizana ndi msinkhu wa mwanayo, zoseŵeretsa zomuthandiza kuganiza zikhoza kukhala zinthu zosavuta kupeza monga tinjerwa tomangira zinthu, mabokosi opanda kanthu, mapepala, zojambulira, ngakhale mchenga ndi madzi. Buku la Motivated Minds limati “zoseŵeretsa zing’onozing’ono zopanga, monga za ziweto, zimamupatsa [mwana] mwayi woika zinthu zofanana pamodzi, kuziika pagulu, ndi kuziyerekezera ndi zina, ndiponso kukulitsa luso lake lolankhula mwa kupeka tinkhani.” Bukulo limati mungagwiritsenso ntchito zida zoimbira nyimbo zosavuta kuseŵeretsa, ngati muli okonzeka kupirira phokosolo, chifukwa zimenezi zimathandiza ana kuphunzira za mapokoso ndi kamvekedwe kake.

Ana ali ndi luso labwino kwambiri lotha kupanga zithunzi m’maganizo mwawo, ndipo amafunitsitsa kuphunzira ndi kuseŵera. Bwanji osawathandiza m’mbali zitatu zonsezi mwa kuwasankhira mwanzeru zinthu zoseŵeretsa.