Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Vuto la Mabanja Opanda Atate Likukula

Vuto la Mabanja Opanda Atate Likukula

Vuto la Mabanja Opanda Atate Likukula

ATATE ochulukirachulukira akusiya mabanja awo. Kumapeto kwa zaka za m’ma 1990, nyuzipepala yotchedwa USA Today inanena kuti dziko la United States “ndi limene lili ndi mabanja ambiri opanda atate kuposa mayiko ena onse.” Komabe, vuto la mabanja opanda atate n’lapadziko lonse.

Ku Brazil, kalembera amene anachitika m’chaka cha 2000 anasonyeza kuti mabanja amene amatsogoleredwa ndi akazi analipo 11.2 miliyoni pa mabanja 44.7 miliyoni amene ali m’dzikomo. Ku Nicaragua, ana 25 pa ana 100 alionse amakhala ndi amayi awo okha. Ku Costa Rica, chiŵerengero cha ana amene atate awo sawaona ngati ana awo chinakwera m’zaka za m’ma 1990 kuchoka pa ana pafupifupi 21 pa ana 100 alionse kufika pa ana pafupifupi 30 pa ana 100 alionse.

Ziŵerengero zochokera m’mayiko atatu ameneŵa ndi chitsanzo chabe cha zimene zikuchitika padziko lonse. Taganizirani mbali ina ya vuto limeneli.

Atate Oti Alipo Koma Amakhala Ngati Kulibe

Onani bokosi lakuti “Ababa, Mubweranso Liti?” Nao, amene tsopano ali ndi zaka 23 anafotokoza kuti: “Ndisanayambe sukulu ya pulayimale, nthaŵi zambiri Bambo sindinkawaona. Tsiku lina, pamene ankachoka, ndinawachonderera kuti, ‘Mubwerenso, chonde.’”

Mabanja amene zochitika zake zimakhala ngati mmene zinalili ndi Nao ndi bambo ake ndi amene anachititsa Mlembi wina wa ku Poland dzina lake Piotr Szczukiewicz kunena kuti: “Ndikuona kuti tate ndi munthu wofunika kwambiri amene mabanja ambiri alibe.” N’zoona kuti atate ambiri amakhala ndi mabanja awo ndipo amawapezera zosowa pamoyo wawo. Koma, monga momwe magazini ya Chifalansa yotchedwa Capital inanenera, “atate ambiri amakhutitsidwa ndi kungopezera ana awo chakudya basi, popanda kuwaphunzitsa.”

Nthaŵi zambiri atate amakhala oti alipo m’banjamo koma zochita za ana awo siziwakhudza. Mtima wawo umakhala uli kwina. Magazini ya Chifalansa yotchedwa Famille chrétienne inati: “Ngakhale [atate] akhalepo, maganizo awo akhoza kukhala ali kwina.” N’chifukwa chiyani atate ambiri masiku ano maganizo ndi mitima yawo imakhala kwina, osati m’mabanja mwawo?

Monga momwe magazini ya Famille chrétienne ikufotokozera, chifukwa chachikulu n’choti “amalephera kumvetsa udindo wa tate kapena mwamuna.” Atate ambiri amaganiza kuti tate wabwino ndi amene amapezera banja lake ndalama zokwanira basi. Monga momwe mlembi wina wa ku Poland dzina lake Józef Augustyn ananenera, “atate ambiri amaganiza kuti iwowo ndi makolo abwino chifukwa chakuti amapezera banja lawo ndalama.” Koma kuchita zimenezo ndi mbali imodzi chabe ya udindo wa tate.

Mfundo n’njakuti, ana sayerekezera phindu la bambo awo ndi ndalama zimene bambowo amapeza kapena mphatso zimene amawapatsa. M’malo mwake, zimene ana amafuna kwenikweni, kuposa kupatsidwa mphatso, ndi zoti bambo awo aziwakonda, azicheza nawo mokwanira, ndiponso aziwalabadira. Zimenezi n’zimene zili zofunikadi kwa ana.

Atate Afunika Kuonanso Bwinobwino Moyo Wawo

Malinga ndi zimene linanena lipoti lochokera ku bungwe loona za maphunziro ku Japan la Japanese Central Council for Education, “atate afunika kuonanso bwinobwino moyo wawo, chifukwa amadzipereka mopitirira muyeso pa ntchito yawo.” Choncho funso n’lakuti, Kodi tate angasinthe moyo wake kuti asangalatse ana ake? Nyuzipepala ya ku Germany yotchedwa Gießener Allgemeine inafalitsa kafukufuku amene anapeza kuti atate ambiri amene anafunsidwa mafunso anakana kuika ana awo patsogolo pa ntchito yawo.

Ana angakhumudwe kwambiri bambo awo akamaoneka ngati sawaganizira n’komwe. Lidia, amene tsopano ali ndi zaka 21, akukumbukira bwino kwambiri mmene bambo ake analili iye ali mtsikana wamng’ono ku Poland. Akufotokoza kuti: “Bambo sankatilankhulitsa. Zinkaoneka ngati amakhala kwina. Sankadziŵa kuti ndikafuna kusangalala ndinkapita ku madisiko.” N’chimodzimodzinso ndi Macarena, mtsikana wa zaka 21 wa ku Spain, amene anafotokoza kuti ali mwana, bambo ake “ankapita koyenda ndi anzawo kumapeto kwa sabata kukasangalala, ndipo nthaŵi zina ankakhalako kwa masiku angapo.”

Kuika Zinthu Zofunika Patsogolo

Atate ambiri angazindikire kuti sacheza ndi ana awo mokwanira ndiponso sawalabadira mokwanira. Abambo a mnyamata wina ku Japan anati: “Ndikukhulupirira kuti mwana wanga adzamvetsa vuto langa. Nthaŵi zonse ndimakhala ndikuganiza za iyeyo, ngakhale ndikhale wotanganidwa.” Komabe, kodi kungokhulupirira kuti mwana adzamvetsa chimene chimachititsa kuti bambo ake asamakhalepo kungathetse vutolo?

N’zachionekere kuti m’pofunika khama, ngakhale kudzimana kumene, kuti kholo lipatse mwana wake zonse zimene amafunikira. Zoonadi, kupatsa ana zimene amafunikira kwambiri, kutanthauza kuti kuwakonda, kucheza nawo mokwanira, ndi kuwalabadira, sikophweka. Yesu Kristu anati: “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate [kapena chakudya]” chokha. (Mateyu 4:4) Ndi zoonanso kuti ana sangakule bwino pongowapatsa zinthu basi. Monga tate, kodi ndinu wokonzeka kudzimana zinthu zimene zingakhale za mtengo wapatali kwa inu, zinthu monga nthaŵi yanu kapena ngakhale mwayi wopititsa patsogolo ntchito yanu, kuti muzitha kucheza ndi ana anu mokwanira?

Nyuzipepala yotchedwa Mainichi Daily News ya pa February 10, 1986, inalemba nkhani ya tate amene anadzazindikira kufunika kwa ana ake. Nyuzipepalayo inati: “Bwana wamkulu pa kampani ya sitima ya Japanese National Railways (JNR) anasankha kusiya ntchito yake m’malo mopitiriza kusaonana ndi banja lake.” Nyuzipepalayo kenaka inamugwira mawu bwanayo akunena kuti: “Munthu aliyense akhoza kukhala bwana wamkulu pakampani. Koma bambo wa ana anga ndine ndekha.”

Zoonadi, chinthu choyamba chofunika kudziŵa ndicho mtundu wa tate amene ana amafunikira. Tiyeni tione zomwe zimafunika kuti munthu akhale tate woteroyo.

[Bokosi patsamba 19]

“Ababa, Mubweranso Liti?”

Limenelo ndi funso limene Nao, mtsikana wa ku Japan wa zaka zisanu, anafunsa bambo ake tsiku lina pamene bambowo amapita kuntchito. Ngakhale kuti amakhala pakhomopo, Nao nthaŵi zambiri sankawaona. Nthaŵi zonse amabwera kunyumba kuchokera ku ntchito Nao atagona ndipo ankachoka iye asanadzuke.