Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kuphunzitsa Mwana Kuyambira Ali Wakhanda N’kofunika Motani?

Kodi Kuphunzitsa Mwana Kuyambira Ali Wakhanda N’kofunika Motani?

Kodi Kuphunzitsa Mwana Kuyambira Ali Wakhanda N’kofunika Motani?

FLORENCE anali ndi zaka 40 ndipo anali woyembekezera. Ankafuna kwambiri kukhala ndi mwana. Dokotala atamuuza kuti mwana wake adzabadwa ndi vuto lolephera kuphunzira, iye anakana kuchotsa mimbayo, ndipo anabereka mwana wamwamuna wabwinobwino.

Mwana wake, Stephen, atangobadwa kumene, Florence anayamba kumuŵerengera ndi kulankhula naye nthaŵi zonse. Pamene amakula, ankaseŵera naye, kupita naye koyenda, kuyesera kuŵerenga naye limodzi manambala, ndi kuimba naye nyimbo. Florence akukumbukira kuti, “ngakhale ndikamamusambitsa, tinkaseŵera maseŵera a mtundu winawake.” Zimenezi zinamuthandiza kwambiri mwanayo.

Pamene Stephen anali ndi zaka 14, anamaliza maphunziro ake ku yunivesite ya Miami ndipo anakhoza bwino zedi. Patatha zaka ziŵiri, ali ndi zaka 16, anamaliza maphunziro a uloya, ndipo malinga ndi zimene analemba mu nkhani ya moyo wake, anakhala loya wamng’ono kwambiri m’dziko lonse la United States. Mayi ake, Dr. Florence Baccus, amene kale anali mphunzitsi ndiponso mlangizi wa chikhalidwe, akhala akuphunzira kwa nthaŵi yaitali za mmene makanda amaphunzirira. Iwo akukhulupirira kuti nthaŵi imene anathera akuchita zinthu limodzi ndi mwana wawo, komanso kumulimbikitsa kwawo kuchita zinthu zosiyanasiyana, zinasintha tsogolo lake.

Kodi N’chibadwa Kapena ndi Mmene Analeredwera?

Chaposachedwapa, akatswiri a mmene ana amaganizira akhala akukambirana nkhani inayake yofunika kwambiri koma osagwirizana chimodzi. Nkhani yake ndi ya zimene zimakhudza kakulidwe ka mwana, kuti kaya ndi mmene mwanayo amabadwira kapena ndi mmene amaleredwera ndi kuphunzitsidwira. Ochita kafukufuku ambiri akukhulupirira kuti zinthu ziŵirizi zimakhudza kakulidwe ka mwana.

Katswiri wina wa kakulidwe ka ana, Dr. J. Fraser Mustard, anafotokoza kuti: “Zimene tikudziŵa panopa malinga ndi zimene taona, n’zoti zimene mwana amakumana nazo pa zaka zoyambirira za moyo wake zimakhudza mmene ubongo wake umakulira.” Pulofesa wina dzina lake Susan Greenfield nayenso anati: “Mwachitsanzo, tikudziŵa kuti mbali ya ubongo wa anthu oimba bangwe yokhudzana ndi kuyendetsa zala zakumanzere imakhala yaikulu kwambiri kusiyana ndi mbali yomweyo ya ubongo wa anthu ena.”

Kodi Aphunzitsidwe Chiyani?

Poona zimene ochita kafukufuku apezazi, makolo ambiri amayesetsa kutumiza ana awo ku sukulu zamkaka zabwino kwambiri, ndiponso amawononga ndalama zambiri powapezera aphunzitsi ophunzitsa kaimbidwe ka nyimbo ndi zojambulajambula. Ena amaganiza kuti ngati mwana ayesera kuchita chinthu chilichonse, akadzakula adzatha kuchita chilichonse. Masiku ano maphunziro apadera a ana ndiponso sukulu zamkaka zikuchuluka. Makolo ena amayesetsa kuchita chilichonse chomwe angathe kuti athandize ana awo kudziŵa zinthu zambiri kuposa ana ena.

Kodi kuyesetsa kuchita zinthu zonsezi n’kothandizadi? Ngakhale kuti zimenezi zingawapatse ana mwayi wotha kuchita zinthu zosiyanasiyana, nthaŵi zambiri ana ameneŵa saphunzira zinthu zimene munthu amadziŵa akamachita maseŵera osachita kukonzedwa ndi munthu wina. Aphunzitsi amati maseŵera amene mwana amachita pamene wafuna kuseŵera amamulimbikitsa kutulukira zinthu, ndipo amamuthandiza kudziŵa kucheza ndi anthu, kuganiza, ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi mmene akumvera mumtima mwake.

Akatswiri ena a kakulidwe ka ana akukhulupirira kuti maseŵera ochita kukonzedwa ndi makolo akuchititsa ana kukhala ndi mavuto atsopano. Zonse zimene ana ameneŵa amachita zimakhala zochita kuuzidwa ndi makolo awo ndipo amakhala opanikizika, osakhazikika maganizo, amavutika kugona, ndipo amadandaula kuti akumva kupweteka ndi kuphwanya m’thupi. Katswiri wina wamaganizo anati ana ameneŵa akamafika zaka zapakati pa 13 ndi 19, ambiri a iwo amakhala asanaphunzire kuthana ndi mavuto paokha ndipo amakhala “otopa kwambiri, osakonda kucheza ndi anzawo, ndiponso osamvera.”

Choncho, makolo ambiri sakudziŵa chochita. Iwo akufuna kuthandiza ana awo kuti azitha kuchita zonse zimene angathe. Komabe, akudziŵa kuipa kokakamiza ana aang’ono kuchita zinthu zambirimbiri panthaŵi yochepa. Kodi zingatheke kuthandiza ana moyenera? Kodi ana angadziŵe zinthu zochuluka bwanji, ndipo angalimbikitsidwe bwanji kudziŵa zinthu zimenezo? Kodi makolo angachite chiyani kuti ana awo zinthu zidzawayendere bwino? Nkhani zotsatirazi ziyankha mafunso ameneŵa.

[Chithunzi patsamba 3]

Zimene mwana amaphunzira ali wamng’ono zingakhudze mmene ubongo wake umakulira

[Chithunzi patsamba 4]

Maseŵera amathandiza mwana kutulukira zinthu zatsopano ndiponso kukulitsa luso limene ali nalo