Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulera Ana M’maleredwe a Mulungu

Kulera Ana M’maleredwe a Mulungu

Zimene Baibulo Limanena

Kulera Ana M’maleredwe a Mulungu

“M’mene Mungakhazikitsire Malamulo Oti Ana Anu Sangaphwanye”

“Mfundo Zisanu Zimene Muyenera Kuphunzitsa Mwana Wanu Pomafika Zaka Zisanu”

“Zinthu Zisanu Zimene Mwana Aliyense Ayenera Kudziŵa Zomuthandiza Kuchita Zinthu Bwino Kaya Akhale Kuti Akumva Bwanji Mumtima Mwake”

“Zizindikiro Zisanu Zosonyeza Kuti Ana Anu Mukuwalekerera”

“Chilango Choperekedwa mu Mphindi Imodzi Yokha Koma Chabwino Kwambiri”

NGATI kulera ana kukanakhala kosavuta, sibwenzi anthu akukhala ndi chidwi kwambiri ndi nkhani za m’magazini ngati zimene zalembedwa pamwambazo. Olemba mabuku othandiza anthu kulera ana sakanapitiriza kulemba mabuku awo ambirimbiri. Koma kulera ana nthaŵi zonse kwakhala kovuta. Ngakhale zaka zambirimbiri zapitazo, munthu wina ananena kuti “mwana wopusa achititsa atate wake chisoni, namvetsa zowawa amake wom’bala.”—Miyambo 17:25.

Masiku ano, ngakhale kuti pali malangizo ochuluka pankhani imeneyi, makolo ambiri sakudziŵa bwinobwino mmene angalerere ana awo. Kodi Baibulo lingawathandize bwanji?

Tanthauzo Lenileni la Kulera Mwana

Baibulo limafotokoza bwinobwino udindo wa makolo wolera ana awo. Mwachitsanzo, lemba la Aefeso 6:4 limati: “Atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” Lemba limeneli likutchula makamaka atate kuti ndi amene ayenera kutsogolera pa ntchito yolera ana. Komabe, amayi amathandizana ndi amuna awo pantchito imeneyi.

Mawu oyambirira a Chigiriki amene anawamasulira kuti “m’maleredwe” pa Aefeso 6:4 amaphatikizapo zambiri osati kuphunzitsa, kulangiza, ndi kudziŵitsa kokha. Amaphatikizaponso kudzudzula, kuwongolera, ndi kulanga. Choncho kulera ana kumaphatikizapo kuwalanga komanso kuwaphunzitsa zinthu zonse zimene amafunikira kuti akule bwino. Koma kodi makolo angatani kuti asakwiyitse ana awo?

Khalani Womvetsetsa

Kodi n’chiyani chimene chimakwiyitsa mwana? Tayerekezerani izi. Muli ndi mnzanu wa kuntchito amene sachedwa kupsa mtima ndiponso ndi wosaleza mtima. Palibe chimene amakonda mwa inu. Amaoneka kuti sasangalala ndi chilichonse chimene mumanena ndi kuchita. Nthaŵi zambiri mukagwira ntchito amati simunaigwire bwino ndipo amakuchititsani kumva kuti ndinu munthu wolephera. Kodi zimenezo sizingakukwiyitseni ndi kukugwetsani ulesi?

Zimenezo zingachitikenso kwa mwana ngati makolo ake nthaŵi zonse amangokhalira kumudzudzula ndi kumuwongolera mokwiya. N’zoona kuti ana amafunika kuwawongolera nthaŵi ndi nthaŵi ndiponso kuti makolo anapatsidwa mphamvu yochita zimenezo m’Baibulo. Komabe, kukwiyitsa mwana chifukwa chomuchitira zinthu mwankhanza ndiponso mopanda chikondi kungamuvulaze m’maganizo, pa moyo wake wauzimu, ndiponso thupi lake.

Ana Anu Amafunika Kuti Muzicheza Nawo

Makolo ayenera kupeza nthaŵi yocheza ndi ana awo. Ponena za malamulo a Mulungu, lemba la Deuteronomo 6:7 limalangiza atate kuti: “Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.” Ana mwachibadwa amafuna aziona kuti makolo awo amawakonda kwambiri. Kucheza ndi ana anu mwachifatse tsiku lililonse kungakuthandizeni kudziŵa mmene akumvera. Zimenezi zingachititse kuti musavutike kuwafika pamtima mukamawaphunzitsa mfundo zamakhalidwe abwino za m’Baibulo, kuwalimbikitsa ‘kuopa Mulungu ndi kusunga malamulo ake.’ (Mlaliki 12:13) Imeneyi ndi mbali imodzi yolera ana m’maleredwe a Mulungu.

Makolo akamalera ana awo ndi kuwatsogolera moyenera, akhoza kuwaphunzitsa makhalidwe abwino ndi kuwathandiza kulimbana ndi mavuto amene angakumane nawo pamoyo wawo. Lemba la Miyambo 23:24, 25 limafotokoza zotsatirapo zake makolo akachita zimenezi. Limati: “Atate wa wolungama adzasekeradi; wobala mwana wanzeru adzakondwera naye. Atate wako ndi amako akondwere, amako wakukubala asekere.”

[Bokosi/Chithunzi patsamba 27]

“CHILANGIZO CHA AMBUYE”

Lemba la Aefeso 6:4 limanena za “chilangizo cha Ambuye.” Mawu oyambirira a Chigiriki amene anawamasulira kuti “chilangizo,” m’mabaibulo ena anawamasulira kuti “kalingaliridwe,” “kuchenjeza,” ndi “uphungu.” Mawu onseŵa akusonyeza kuti mabanja ayenera kuchita zambiri osati kungoŵerenga Baibulo kapena mabuku ofotokoza za m’Baibulo nthaŵi ndi nthaŵi basi. Makolo ayenera kuonetsetsa kuti ana awo akumvetsa bwino tanthauzo la Mawu a Mulungu, akumvetsa kufunika komvera, ndiponso akumvetsa mmene Yehova amawakondera, ndi mmene amawatetezera.

Kodi angachite bwanji zimenezi? Judy, mayi wa ana atatu, anaona kufunika kochita zambiri m’malo momangokhalira kukumbutsa ana ake mfundo za Mulungu. “Ndinaona kuti sankasangalala ndikamangowauza zinthu zimodzimodzi m’njira yomweyomweyo nthaŵi zonse. Ndinayamba kufunafuna njira zatsopano zowaphunzitsira. Njira imodzi yomwe ndinatsatira inali yofufuza nkhani m’magazini a Galamukani! zimene zinkafotokoza zinthu zomwezo m’njira ina. Choncho ndinaphunzira kukumbutsa ana anga zinthu zimene ankafunikira kudziŵa popanda kuwakwiyitsa.”

Angelo, amene banja lake linakumana ndi mavuto aakulu, akufotokoza mmene anaphunzitsira ana ake aakazi anayi kusinkhasinkha za Mawu a Mulungu. Iye akuti: “Tinkaŵerengera limodzi mavesi a m’Baibulo, ndiyeno ndinkasankhapo mawu ena n’kufotokoza mmene ankagwirizanirana ndi zimene zinali kuchitika pa moyo wawo. Kenaka, akamaŵerenga okha Baibulo, ndinkawaona akuganiza kwambiri, akusinkhasinkha za tanthauzo la zimene ankaŵerengazo kwa iwo.”