Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndani Amavutika Chifukwa cha Kuba M’masitolo?

Kodi Ndani Amavutika Chifukwa cha Kuba M’masitolo?

Kodi Ndani Amavutika Chifukwa cha Kuba M’masitolo?

KU Japan, mwini sitolo wina anagwira mnyamata wamng’ono akuba m’sitolo mwake ndipo anaitana apolisi. Apolisiwo atafika, mnyamatayo anayamba kuthawa, ndipo apolisiwo anamuthamangitsa. Pamene mnyamatayo amawoloka njanji, anagundidwa ndi sitima n’kufera pomwepo.

Chifukwa choti nkhaniyi inafala, anthu ena anati mwini sitoloyo analakwa kuitana apolisi. Iye anatseka sitolo yake kuti nkhaniyo iyambe yazizira. Atatsegulanso sitoloyo, munabweranso anthu ambirimbiri akuba. Koma pokumbukira zomwe zinali zitangomuchitikira kumene zija, ankachita mantha kuti achitepo kanthu. Sitolo yake inatchuka kuti ndi yosavuta kubamo zinthu. Pasanapite nthawi yaitali, anatsekeratu sitoloyo.

N’zoona kuti zomwe zinachitikazi zinali zomvetsa chisoni kwambiri kuposa momwe zimakhalira nthawi zambiri, koma zikusonyeza mfundo ina yofunika kwambiri. Kuba m’masitolo kumapweteketsa anthu ambiri ndiponso kumapweteketsa m’njira zambiri. Tiyeni tione bwino mmene anthu amavutikira chifukwa cha kuba m’masitolo.

Mmene Eni Masitolo Amavutikira

Chaka chilichonse, kuba m’masitolo kumaluzitsa eni masitolo padziko lonse lapansi ndalama zokwana madola mabiliyoni ambiri. Anthu ena ananenapo kuti n’kutheka kuti ku United States kokha ndalama zimene zimaluzika zimapitirira madola 40 biliyoni. Kodi ndi mabizinesi angati amene angakwanitse kuluza ndalama zochuluka choncho? Masitolo ambiri akuvutika kwambiri chifukwa cha zimenezi. Akuba akalowa m’sitolo, bizinesi imene munthu waivutikira kwa moyo wake wonse ikhoza kugwa.

Luke, yemwe ali ndi sitolo mu mzinda wa New York, anati: “Kuwonjezera pa kupikisana ndi masitolo ena, kuba m’masitolo ndi vuto linanso lomwe timada nalo nkhawa. Sindikudziwa kuti ndingakwanitse kuyendetsabe bizinesi yangayi mpaka liti.” Iwo sangakwanitse kugula zida zamagetsi zotetezera sitolo ndiponso kuonera akuba m’sitolomo. Ponena za akubawo, iye anati: “Aliyense akhoza kukhala akundibera, ngakhale makasitomala anga odalirika.”

Ena amaganiza kuti vuto la Luke si lalikulu kwenikweni. Iwo amati: “Masitolo amenewa amapanga ndalama zambiri, choncho zomwe ine ndimatengako n’kadontho chabe.” Koma kodi phindu limene masitolo amapeza n’lalikuludi choncho?

Masitolo m’madera ena amapeza phindu ndithu akagulitsa katundu wawo, koma sikuti phindu lonselo limapita m’thumba mwa eni sitolowo. Mwini sitoloyo amagwiritsa ntchito phindu limene wapezalo kulipirira zinthu zosiyanasiyana zofunika poyendetsa bizinesiyo. Zinthuzi ndi monga lendi, misonkho, kulipira antchito ndi kuwalipirira inshuwalansi, penshoni, ndi zina zotero. Amafunikanso kukonzetsa sitolo yakeyo, kukonzetsa katundu akawonongeka, kulipira inshuwalansi, magetsi, madzi, zotenthetsera m’nyumba, telefoni, ndi zida zotetezera malowo. Akachotsapo ndalama zonsezi, phindu lotsala likhoza kukhala lochepa kwabasi. Choncho munthu akaba m’sitolo, amakhala akutenga kaphindu kotsala kochepa kaja.

Nanga Bwanji Kuba Zinthu Zing’onozing’ono?

Kamnyamata komwe kali ndi mayi ake m’sitolo kakupita kokha pamene pali masiwiti. Pamenepo kakutsegula bokosi la masiwiti n’kutenga siwiti imodzi kuika m’thumba mwake. Kodi kuba zinthu zing’onozing’ono ngati zimenezo kungaluzitse mwini sitoloyo?

Bungwe la mabizinesi ang’onoang’ono ku America lotchedwa U.S. Small Business Administration, linafotokoza m’kabuku kake kotchedwa Curtailing Crime—Inside and Out, kuti: “Kuba zinthu zing’onozing’ono kungaoneke ngati si nkhani yaikulu kwa mbava imene imaba zinthu zing’onozing’ono ngati zolembera, makakyuleta kapena kuti zowerengetsera masamu za m’thumba, ndi zina zotero. Koma kwa mabizinesi ang’onoang’ono amene akuyesetsa kuti bizinesi yawo isafe, zimenezi zikhoza kugwetsa bizinesiyo.” Popeza phindu limene amapeza limakhala lochepa, kuti abwezeretse katundu amene amabedwa pachaka wokwana madola 1,000, mwini sitolo ayenera kugulitsa masiwiti ena 900 kapena zitini za supu 380 tsiku lililonse. Choncho ngati tianyamata tambirimbiri tikuba masiwiti m’sitolo, zikhoza kupha bizinesiyo. Ndipo vuto limene lilipo n’loti anthu amene amaba zinthu zing’onozing’onowa alipo ambiri.

Anthu mamiliyoni ambiri, achinyamata ndi achikulire omwe, olemera ndi osauka, ochokera m’mafuko osiyanasiyana ndiponso okulira kosiyanasiyana, amaba m’misika ndi m’masitolo. Kodi zotsatirapo zake n’zotani? Bungwe loletsa umbanda ku America lotchedwa U.S. National Crime Prevention Council linati bizinesi imodzi pa mabizinesi atatu alionse ku United States imagwa chifukwa cha umbava. Mosakayikira mabizinesi m’mayiko ena akukumananso ndi vuto lomweli.

Makasitomala Amavutika

Anthu akamaba m’masitolo, mitengo ya zinthu imakwera. Choncho, m’madera ena anthu amalipira ndalama zowonjezereka zokwana madola 300 pachaka chifukwa cha mitengo imene imakwera chifukwa cha anthu oba m’masitolo. Zimenezi zikutanthauza kuti ngati mumalipidwa ndalama zokwana madola 60 patsiku, pachaka chimodzi mumagwira ntchito ya mlungu umodzi kuti mulipirire zinthu zimene ena amaba. Kodi mungakwanitse kuchita zimenezo? Kwa anthu opuma pantchito amene amadalira ndalama za penshoni, kapena mayi amene akulera yekha ana ake, ndipo akuvutika kuti apezere banja lake zosowa za pamoyo, kutaya ndalama za mlungu umodzi m’njira imeneyi n’kopweteka kwambiri. Koma kuvutikako sikuthera pamenepo.

Anthu onse okhala ku dera linalake akhoza kuvutika ngati sitolo yam’deralo yatsekedwa. Posachedwapa sitolo inayake yogulitsa mankhwala ku dera linalake ku United States, komwe anthu ake amadziwana bwino, inatsekedwa akuti chifukwa cha kuba. Kuti akagule mankhwala, anthu ambiri okalamba ndiponso odwala a m’deralo tsopano akumayenda ulendo wokwana makilomita awiri ndi theka kupita ku sitolo ina yogulitsa mankhwala. Mkulu wina wa boma anati: “Tangoganizani momwe munthu woti ali pa njinga ya opuwala amavutikira kuyenda mtunda umenewo.”

Makolo Amavutika Nazo

A Chabwera ndi bambo amene amatsatira mfundo zapamwamba zamakhalidwe abwino ndipo amaphunzitsa ana awo kukhala oona mtima. Tsiku lina mwana wawo wamkazi anamugwira akuba. Iwo anati: “Ndinakhumudwa kwambiri. Tangoganizirani mmene mungamvere mutalandira foni yokuuzani kuti mwana wanu amugwira akuba m’sitolo. Zaka zonsezi takhala tikumuphunzitsa mwana wathuyu kuti akhale ndi khalidwe labwino, koma lero tikumva zimenezi. Sitinaganizepo kuti angadzapanduke chonchi.”

A Chabwera anali ndi nkhawa kwambiri poganizira za mwana wawo ndi tsogolo lake. Kuwonjezera apo, anatula pansi udindo womwe anali nawo ngati mphunzitsi wachipembedzo wongodzipereka. Iwo anati: “Ndikanatha bwanji kuyang’ana mpingo ndili pa pulatifomu? Kodi ndikanatha bwanji kuwaphunzitsa ndi chikumbumtima choyera mmene angalerere ana awo? Ndinaona kuti chikumbumtima changa sichingandilole kuchita zimenezo.” Zikuoneka kuti mwana wawoyo sanaganizire mofatsa momwe kuba kwakeko kungapweteketsere bambo ake.

Mmene Akubawo Amavutikira

Kale, eni masitolo akagwira anthu akuba m’masitolo mwawo, nthawi zambiri ankawachenjeza mwamphamvu kuti asadzabenso kenaka n’kuwasiya. Masiku ano eni masitolo amamangitsa ngakhale anthu amene ndi nthawi yawo yoyamba kuba. Zikatero akubawo amazindikira kuti mlandu wawowo ndi waukulu. Mtsikana wina dzina lake Titha anakumanapo n’zimenezi.

Titha anati: “Chifukwa choba kwambiri, ndinayamba kudzidalira. Ndinkaganiza kuti ngakhale atandigwira, ndalama zolipirira loya ndiponso kukhoti zingakhalebe zochepa poyerekezera ndi ndalama zomwe ndikanawononga ndikanati ndilipirire madiresi onse okongola omwe ndinaba.” Koma maganizo akewa anali olakwika.

Titha anamugwira akuba diresi, ndipo apolisi anamutenga atamumanga unyolo. Ku polisiko, anamuuza kuti adinde chidindo ndi chala chake, ndipo anamutsekera m’chipinda limodzi ndi zigawenga zina. Anakhala mmenemo maola ambirimbiri akudikira makolo ake kuti adzamutulutse pa belo.

Titha amauza aliyense amene akuganiza za kuba kuti: “Mverani malangizo anga, ndipo ingogulani diresi kapena jinzi mukufuna kubayo basi.” Iye anati, mukaba “mudzanong’oneza bondo kwa nthawi yaitali kwambiri.”

Kudziwika kuti unachitapo zaumbanda n’chinthu chomvetsa chisoni kwambiri. Anthu oba m’masitolo amene anagwidwapo amadandaula akaona kuti mlandu wawowo amavutika nawobe nthawi ndi nthawi ndipo sufufutika, monga momwe imachitira diresi kapena shati yothimbirira. Munthu amene anagwidwa akuba m’sitolo angafunike kuulula zimenezi pa fomu yolowera ku yunivesite. Angavutike kuyamba ntchito inayake, monga ya udokotala wa matenda osiyanasiyana, ya udokotala wa mano, kapena ya zomangamanga. Makampani ena sangafune kumulemba ntchito. Ndipo angakumane ndi mavuto amenewa ngakhale kuti analipira ndalama zimene akhoti anamuuza kuti alipire ndiponso ngakhale kuti anasiya kubako.

Kuba m’masitolo kungamukhaulitse munthu m’njira zina ngakhale atakhala kuti sanagwidwepo. Mavuto, amene tinamutchula kale mu nkhani zino, anadzionera yekha zimenezi. Iye anati: “Nthawi zonse ndinkapulumuka. Sindinagwidwepo ndikuba.” Koma anakumana ndi mavuto ena. Poganizira zakale, iye anati: “Ndikuganiza kuti achinyamata ayenera kumvetsa mfundo imodzi: Umatuta zomwe wafesa. Ngakhale apolisi asakugwire, umavutikabe.”

Kuba m’masitolo kumapweteketsa anthu ambiri, ndipo winawake amafunika alipire zinthu zimene akubawo amaba. Aliyense amene amaba m’masitolo ayenera kusiyiratu khalidwe limeneli. Koma kodi munthu woba m’masitolo angathe bwanji kusiyiratu kuba? Kodi khalidwe loipali lidzatha?

[Chithunzi patsamba 23]

Kuba m’masitolo kumagwetsa mabizinesi

[Chithunzi patsamba 23]

Aliyense amavutika chifukwa cha kuba m’masitolo

[Zithunzi patsamba 24]

Kuba m’masitolo kumawononga tsogolo lanu

[Mawu a Chithunzi]

Fingerprints: © Morocco Flowers/Index Stock Imagery