Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

“Chaka chilichonse” ku United States “kumakhala munthu mmodzi mwa anthu anayi alionse amene ali ndi vuto linalake la matenda a m’maganizo, ndipo pafupifupi mmodzi mwa anthu awiri alionse amadwala matenda a mtunduwu pa nthawi inayake m’moyo wake.”—SCIENCE NEWS, U.S.A.

Mu September 2004, mphepo ya mkuntho yotchedwa Hurricane Ivan inachita mafunde osachepera 24 otalika mamita 15 ku Gulf of Mexico. Ndipo funde lina linali lalitali pafupifupi mamita 28.—SCIENCE MAGAZINE, U.S.A.

Kulankhula pa telefoni ya m’manja mukuyendetsa galimoto kumachulukitsa kuwirikiza kanayi mpata wochita ngozi yofunika kutengera munthu ku chipatala, kaya dalaivalayo akugwiritsa ntchito zipangizo zothandiza kuti asagiwire foniyo m’manja kapena ayi.—BMJ, BRITAIN.

▪ Buku lina latsopano lothandiza anthu omasulira Baibulo lili ndi mndandanda wa zinenero 6,912 zimene anthu akulankhulabe panopo.—THE NEW YORK TIMES, U.S.A.

▪ Ngakhale kuti azimayi oyembekezera kapena oyamwitsa ku Poland amachenjezedwa kuti akhoza kuvulaza ana awo ndi fodya, azimayi 30 mwa azimayi 100 alionse oyembekezera ndi oyamwitsa kumeneko amasutabe fodya.—ZDROWIE MAGAZINE, POLAND.

Mmene Anthu Amaonera Chuma

Bungwe lina ku Australia litafufuza mmene anthu amaonera chuma linapeza kuti munthu mmodzi yekha mwa anthu 20 alionse achuma kwambiri ku Australia ndi amene amadziona kuti ndi wolemera, inatero ABC News Online. Mogwirizana ndi Clive Hamilton, mkulu wa bungwe limeneli, “tikamalemera kwambiri, m’pamenenso timakhala osakhutira kwambiri ndi zinthu zimene tikuzipeza.” Ndiponso, anthu 13 okha mwa anthu 100 alionse omwe ali m’gulu la anthu opeza ndalama zambiri ndi amene amakhutitsidwa ndi moyo. Hamilton anati: “Munthu ungadabwe chifukwa chimene anthufe timafunira kukhala ndi chuma chambiri kuposa china chilichonse, pamene maumboni onse amasonyeza kuti zinthu zina zomwe timachita pa moyo n’zimene zimatithandiza kukhala osangalaladi.”

Makina Owonongeka Amene Ali Mumlengalengamu

“Taganizani mmene anthu angakwiyire ngati madalaivala atasiya magalimoto awo m’misewu ya mu mzinda chifukwa choti atha mafuta,” inatero magazini ya New Scientist. Ndipo zimenezi zikufanana ndi zomwe zikuchitika ndi makina otha ntchito ojambulira zinthu omwe ali mumlengalengamu, ndipo chifukwa cha zimenezi, n’zotheka kuti zombo zatsopano ziombane ndi makina owonongeka amenewa. Akuti makina pafupifupi 1,120 aakulu kupitirira masentimita 60 m’lifupi mwake, ali pafupi ndi njira imene zombozo zimadutsa, ndipo amenewo ndi malo amene anthu amakonda kuikamo zipangizo zimenezi, komano makina 300 okha pa makina onsewa ndi amene akugwira ntchito. Ena mwa makina oopsa kwambiri otha ntchito amene anangowasiya m’malo osiyanasiyana, ndi makina 32 omwe ankadziwitsa anthu za mphamvu ya nyukiliya.

Zida ndi Nkhondo

Chidani chachikulu cha pakati pa mayiko a America ndi Soviet Union chitatha, malonda a zida zankhondo analowa pansi. Komabe, m’zaka zowerengeka zapitazo, malondawa ayambiranso kuyenda bwino. M’chaka cha 2004, mogwirizana ndi lipoti la a Stockholm International Peace Research Institute (SIPRI), ndalama zimene dziko lonse lapansi linagwiritsa ntchito pa zankhondo zinakwana madola mabiliyoni 1,000. Ndalama zimenezi atati azigawe kwa mwamuna, mkazi, ndi mwana aliyense padziko lapansi pano, aliyense angalandire madola 162. Mogwirizana ndi a SIPRI, m’chaka cha 2004 munali kumenyedwa nkhondo 19 ndipo iliyonse mwa nkhondozi inaphetsa anthu oposa 1,000. Pa nkhondo zimenezo, nkhondo 16 zinakhala zikumenyedwa kwa zaka zoposa 10.

Magalimoto Oyendera Mafuta Amitundu Iwiri

Imodzi mwa magalimoto atatu atsopano amene akugulitsidwa ku Brazil tsopano ndi yoyendera mafuta amitundu iwiri, inatero magazini yotchedwa Veja. Magalimoto amenewa amayendera petulo, kachasu wa nzimbe, kapena kuphatikiza zinthu ziwirizi, mulimonse mmene munthu angasakanizire. Kuchokera m’chaka cha 2003 mpaka 2004, malonda a kachasu woyendetsera magalimoto anakwera ndi 34 peresenti. Izi sizikukhudzana ndi nkhawa zimene anthu ali nazo pa za chilengedwe. Kungoti madalaivala amaona kuti kugwiritsa ntchito kachasu sikuwawonongetsa ndalama zambiri. Magalimoto oyendera mafuta amitundu iwiri amenewa angathandize kuti “eni magalimotowo asamavutike ndi kukwera mitengo kwa mafuta,” anatero Rafael Schechtman, mkulu wa Brazilian Center of Infrastructure. “Mitengo ya kachasu ikakwera, anthu azigwiritsa ntchito petulo ndipo mitengo ya petulo ikakwera, azigwiritsa ntchito kachasu.”