Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Yesu Anaferadi Pamtanda?

Kodi Yesu Anaferadi Pamtanda?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Yesu Anaferadi Pamtanda?

MTANDA ndi chimodzi mwa zizindikiro zomwe anthu amazidziwa kwambiri zimene zipembedzo zimagwiritsa ntchito. Anthu mamiliyoni ambiri amaulambira, poganiza kuti ndi chinthu chopatulika chomwe anapherapo Yesu. Wolemba mabuku wina yemwenso ndi katswiri wa mbiri ya zinthu zakale zokumbidwa pansi, wa chipembedzo cha Roma Katolika, dzina lake Adolphe-Napoleon Didron anati: “Anthu akhala akulambira mtanda pafupifupi kufanana, kapena kufanana kumene, ndi mmene amachitira ndi Kristu; anthu amakonda mtengo umenewu kutsala pang’ono kufanana ndi mmene amakondera Mulungu Weniweniyo.”

Ena amati mtanda umawathandiza kuona kuti ayandikana kwambiri ndi Mulungu akamapemphera. Ena amaugwiritsa ntchito ngati chithumwa, poganiza kuti umawateteza ku mizimu yoipa. Koma kodi Akristu ayenera kulambira mtanda? Kodi Yesu anaferadi pamtanda? Kodi Baibulo limaphunzitsa zotani pankhani imeneyi?

Kodi Mtanda Umaimira Chiyani?

Kale kwambiri Chikristu chisanayambe, anthu akale a ku Babulo ankagwiritsa ntchito mitanda monga zizindikiro za kupembedza kwawo mulungu wa mphamvu za kubereka, dzina lake Tammuz. Kugwiritsa ntchito mtanda kunafalikira mpaka ku Egypt, India, Syria, ndi China. Kenako, patapita zaka zambirimbiri, Aisrayeli anaphatikiza kulambira Yehova ndi kulambira mulungu wonyenga uja Tammuz. Baibulo limati kulambira kotereku ndi “zonyansa zazikulu.”—Ezekieli 8:13, 14.

Mauthenga Abwino a Mateyu, Marko, Luka, ndi Yohane amagwiritsa ntchito mawu a Chigiriki akuti stau·rosʹ potchula chinthu chomwe Yesu anaferapo. (Mateyu 27:40; Marko 15:30; Luka 23:26) Mawu akuti stau·rosʹ amatanthauza mtengo woongoka. Buku lakuti The Non-Christian Cross, lomwe analemba J. D. Parsons, limati: “M’mabuku onse a Chipangano Chatsopano, omwe ali m’Chigiriki choyambirira, mulibe chiganizo n’chimodzi chomwe chimene chimasonyeza ngakhale mosachita kutchuliratu kuti mtengo womwe anapherapo Yesu sunali mtengo wamba; ndipo palibe umboni wosonyeza kuti silinali thabwa limodzi, koma matabwa awiri okhomedwa mopingasa.”

Malinga ndi zimene zili pa Machitidwe 5:30, mtumwi Petro anagwiritsa ntchito mawu akuti xyʹlon otanthauza “mtengo,” omwe ndi ofanana ndi akuti stau·rosʹ, osati kutanthauza mtanda wa matabwa awiri, koma thabwa kapena mtengo wamba wowongoka. M’mbuyomo anthu sankaganizira zoti Yesu anaphedwera pamtanda wa matabwa awiri, mpaka patatha zaka pafupifupi 300 kuchokera pamene iye anaphedwa. Panthawiyi anthu ena odzitcha Akristu anayamba kuphunzitsa zoti Yesu anam’phera pamtanda wa matabwa awiri. Koma maganizo amenewa anayambika chifukwa cha miyambo chabe ndiponso kusokoneza mawu a Chigiriki akuti stau·rosʹ. N’zochititsa chidwi kuti zojambula zina zamakedzana zosonyeza mmene Aroma ankanyongera anthu zimasonyeza mtengo umodzi wowongoka.

“Dzisungireni Nokha Kupewa Mafano”

Nkhani yofunika kwambiri kwa Akristu oona ndi yofuna kudziwa ngati ndi bwino kulambira chinthu chimene anagwiritsa ntchito kuphera Yesu. Kaya unali mtengo umodzi wowongoka, mtanda, muvi, mkondo, kapena mpeni, kodi anthu ayenera kugwiritsa ntchito chinthu choterocho polambira?

Yerekezani kuti munthu wina amene munali kum’konda, waphedwa mwankhanza ndipo chida chomwe anam’phera chinaperekedwa ku khoti monga umboni. Kodi mungayese kutenga chida chomwe anaphera munthucho, n’kuchitola zithunzi, ndi kusindikiza zithunzi zina zambirimbiri n’kumagawira anthu? Kodi mungapange zizindikiro za chidacho zazikulu mosiyanasiyana? Ndiyeno kodi mungapange zinthu monga ndolo kapena mphete za tizifanizo ta chidacho? Kapena kodi mungakonze zoti kampani ina ikupangireni zinthu zoterozo n’kumazigulitsa kwa anzanu ndi achibale anu kuti azizilambira? N’zodziwikiratu kuti simungaganize n’komwe zochita zimenezo. Komatu izi n’zimene anthu achita ndi mtanda!

Komanso, kugwiritsa ntchito mtanda polambira sikusiyana ndi kugwiritsa ntchito zifanizo polambira, ndipo Baibulo limaletsa mchitidwe umenewu. (Eksodo 20:2-5; Deuteronomo 4:25, 26) Mtumwi Yohane anasonyeza bwino ziphunzitso za Chikristu choona pamene analimbikitsa Akristu anzake kuti: “Dzisungireni nokha kupewa mafano.” (1 Yohane 5:21) Iwo anachita zimenezi ngakhale pamene kutero kunatanthuza kuti aphedwa m’bwalo la masewera la Aroma.

Komabe, Akristu oyambirira anali kulemekeza kwambiri imfa ya nsembe ya Kristu. N’chimodzimodzinso masiku ano, ngakhale kuti chinthu chomwe anagwiritsa ntchito pozunza ndi kupha Yesu sichiyenera kulambiridwa, Akristu oona amakumbukira imfa ya Yesu monga njira yomwe Mulungu amapulumutsira anthu opanda ungwiro. (Mateyu 20:28) Chisonyezero chapamwamba kwambiri chimenechi cha chikondi cha Mulungu chidzapangitsa kuti anthu okonda choonadi apeze madalitso osaneneka, kuphatikizapo chiyembekezo chodzakhala ndi moyo kwamuyaya.—Yohane 17:3; Chivumbulutso 21:3, 4.

[Chithunzi patsamba 12]

Zojambula zina zamakedzana zimasonyeza kuti Aroma ankagwiritsa ntchito mtengo umodzi wowongoka ponyonga anthu

[Mawu a Chithunzi]

Rare Books Division, The New York Public Library, Astor, Lenox and Tilden Foundations