Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungapewe Kukalamba?

Kodi Mungapewe Kukalamba?

Kodi Mungapewe Kukalamba?

“Timakhala zaka 70 zokha, mwina 80 ngati tili ndi mphamvu; . . . kenako moyo umatha ndipo sitikhalakonso.”—SALMO 90:10, TODAY’S ENGLISH VERSION.

TANGOYEREKEZERANI mutamangokhalabe wachinyamata mpaka kalekale. Yerekezeraninso mutakhala ndi thanzi labwino ndiponso nzeru zambiri mpaka kalekale. Kodi mukuganiza kuti zimenezo sizingachitike? Ngati ndi choncho, taganizirani mfundo yochititsa chidwi iyi: Ngakhale kuti mbalame zina za m’gulu la zinkhwe zimatha kukhala zaka 100, mbewa nthawi zambiri sizipitirira zaka zitatu. Kusiyanasiyana kwa utali wa moyo kumeneku kwachititsa akatswiri ena a sayansi ya zamoyo kunena kuti pali chinthu chimene chimachititsa zamoyo kukalamba, ndi kuti ngati kukalamba kuli ndi chochititsa, ndiye kuti kukhoza kukhala ndi mankhwala.

Kufunafuna mankhwala oletsa kukalamba kwachititsa makampani opanga mankhwala kulowetsa ndalama zambiri ku ntchito yopezera mankhwalawo. Komanso, anthu amene anabadwa nkhondo yachiwiri yapadziko lonse itatha, omwe panopa akuyandikira zaka 60 ali ndi chidwi kwambiri ndi nkhani yopeza njira yoletsera kukalamba.

Anthu ambiri ochita kafukufuku wokhudzana ndi chibadwa komanso kapangidwe ka zamoyo, moyo wa zinyama, ndi a sayansi ya kukalamba, ayamba kuona maphunziro okhudzana ndi kukalamba kukhala ofunika kwambiri. Buku lotchedwa Why We Age (Chifukwa Chake Timakalamba), lolembedwa ndi Steven Austad limati: “Masiku ano, akatswiri a sayansi ya kukalamba akakumana, zimakhala zoonekeratu kuti anthuwo ali ndi chidwi ndi nkhani imeneyi. Tatsala pang’ono kupeza zomwe zimayambitsa kukalamba ndi momwe kumachitikira.”

Anthu ali ndi maganizo osiyansiyana pa nkhani ya zinthu zimene zimayambitsa kukalamba. Ena amati kukalamba kumayamba chifukwa cha kuwonongeka kwa maselo m’thupi; pamene enanso amati munthu anapangidwa kuti azikalamba basi. Ena amatinso kukalamba kumabwera chifukwa cha zinthu ziwiri zonsezi. Kodi anthu amakumvetsetsa bwino kukalamba? Kodi pali chifukwa chilichonse choyembekezera kuti tingadzapeze mankhwala oletsa kukalamba?

[Tchati/Zithunzi pamasamba 2, 3]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

ZAKA ZIMENE ZAMOYOZI ZINGAFIKE

Njuchi

Masiku 90

Mbewa

Zaka zitatu

Galu

Zaka 15

Nyani

Zaka 30s

Mng’azi

Zaka 50

Njovu

Zaka 70

Munthu

Zaka 80

Chinkhwe

Zaka 100

Kamba wamkulu

Zaka 150

Mtengo wa sekwaya

Zaka 3,000

Mtengo wa paini

Zaka 4,700

[Chithunzi patsamba 3]

Zinkhwe zina zikhoza kukhala ndi moyo zaka 100, koma anthu amakhala ndi moyo zaka pafupifupi 80. Ochita kafukufuku amafunsa kuti: “N’chiyani chimayambitsa kukalamba?”