Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Timakalamba?

N’chifukwa Chiyani Timakalamba?

N’chifukwa Chiyani Timakalamba?

“Munthu, wobadwa mwa mkazi, amakhala ndi moyo waufupi koma wodzaza mavuto.”—YOBU 14:1, THE JERUSALEM BIBLE.

MWINA munaganizapo kuti zamoyo zonse pomalizira pake ziyenera kuwonongeka. Galimoto ndi wailesi zoti zikugwira ntchito tsiku lililonse, zimayamba kuwonongeka pang’onopang’ono kenako zimafa n’kusiya kugwira ntchito. N’zophwekerapo kuganiza kuti zinyama zimakalamba ndi kufa m’njira yofanana ndi imeneyi. Koma pulofesa wa moyo wa zinyama, dzina lake Steven Austad, anafotokoza kuti: “Zamoyo n’zosiyana kwambiri ndi makina. Ndipotu, chinthu chimene chimasiyanitsa kwambiri zamoyo ndi zopanda moyo, n’choti zamoyo zimatha kudzikonza zokha.”

Njira imene thupi lanu limadzikonzera mukavulala n’njochititsa chidwi kwambiri. Koma tikaganizira mmene limadzikonzera lokha nthawi zonse, n’zochititsa chidwi kuposa pamenepa. Mwachitsanzo, taganizirani mafupa anu. Magazini yotchedwa Scientific American inafotokoza kuti: “Ngakhale kuti mafupa amaoneka ngati opanda moyo, ali ndi moyo ndipo mosalekeza amakhala akudziwononga ndi kudzikonza kwa moyo wonse wa munthu. Chifukwa cha kusintha kumeneku, munthu amakhala ndi mafupa atsopano m’thupi lonse pomatha zaka 10 zilizonse.” Mbali zina za thupi lanu zimasinthidwa pafupipafupi kwambiri. Maselo ena a pakhungu, m’chiwindi, ndi m’matumbo mwanu mwina amasinthidwa pafupifupi tsiku lililonse. Pa sekondi iliyonse, thupi lanu limapanga maselo atsopano 25 miliyoni oti alowe m’malo mwa maselo akale. Zimenezi zikanakhala kuti sizichitika ndipo mbali zonse za thupi lanu sizinali kukonzedwa ndi kulowedwa m’malo, mukanakalamba mukadali mwana.

Mfundo yoti maselo athu amadzikonza inaoneka kuti ndi yochititsa chidwi kwambiri pamene akatswiri a sayansi ya zamoyo anayamba kuphunzira za zinthu zimene zili m’kati mwa maselo amoyo. Maselo anu akamalowedwa m’malo ndi maselo atsopano, selo latsopano lililonse liyenera kukopera DNA yanu, yomwe imakhala ndi pafupifupi zonse zimene maselo amafunika kudziwa kuti athe kupanga maselo ena atsopano m’thupi lanu lonse. Tangoganizirani za kuchuluka kwa nthawi zomwe DNA yakopedwa, osati pamoyo wanu wokha m’thupi mwanu koma kuyambira pamene anthu anayamba kukhalapo. Kuti muzindikire kudabwitsa kwa zimenezi, taganizirani zomwe zingachitike ngati mungagwiritse ntchito makina ochitira fotokope kukopera chikalata kenaka n’kugwiritsa ntchito chikalata chomwe mwakopacho kukoperanso chikalata china. Ngati mutachita zimenezi mobwerezabwereza, zikalata zomwe mukukopazo sizingamaoneke bwino ndipo pamapeto pake simungathe kuziwerenga. Koma n’zosangalatsa kuti DNA yathu siwonongeka pamene maselo athu akuikopera n’kumagawikana mobwerezabwereza. N’Chifukwa chiyani? Chifukwa choti maselo athu ali ndi njira zambiri zokonzera DNA yomwe yakopedwa molakwika. Zimenezi zikanakhala kuti sizichitika, bwenzi anthu atasiya kalekale kukhalapo!

Popeza mbali zonse za m’thupi mwathu, kuyambira ziwalo zikuluzikulu mpaka tinthu ting’onoting’ono ta m’kati mwa maselo, nthawi zonse zimakhala zikusinthidwa kapena kukonzedwa, sitinganene kuti timakalamba chifukwa cha kuwonongeka kwa maselo. Mbali zosiyanasiyana za thupi zimadzikonza kapena kudzisintha zokha kwa zaka zambirimbiri, ndipo mbali iliyonse imadzisintha m’njira yosiyana ndiponso pa liwiro losiyana ndi mbali zina. Choncho, kodi n’chifukwa chiyani mbali zonse za thupi zimayamba kusiya kugwira ntchito bwino pa nthawi imodzimodzi?

Kodi Anthu Anapangidwa Kuti Azikalamba?

N’chifukwa chiyani mphaka amakhala ndi moyo zaka 20, koma nyama inayake ya saizi yomweyo, yomwe imanyamula ana ake kumimba ndipo imapezeka ku North America, imakhala zaka zitatu zokha? N’chifukwa chiyani mleme amatha kukhala zaka 20 kapena 30, koma mbewa imakhala zaka zitatu zokha? N’chifukwa chiyani akamba akuluakulu amatha kukhala zaka 150, koma njovu imakhala zaka 70 zokha? Zinthu ngati chakudya, kulemera kwa thupi, kukula kwa ubongo, kapena nthawi imene zimatenga kuti zikule, si zimene zimachititsa kuti nyama zimenezi zizikhala ndi moyo wautali mosiyanasiyana choncho. Buku la Encyclopædia Britannica limati: “M’kati mwa maselo muli malangizo amene amanena zaka zimene chamoyocho sichingapitirire.” M’maselo ndi mmene mumakhala malangizo onena za kutalika kwa moyo umene chamoyocho chingakhale. Komano, pamene nthawi imene chamoyocho chimafa ikuyandikira, n’chiyani chimachititsa thupi kuleka kugwira ntchito bwino?

Katswiri wina wa sayansi ya zamoyo dzina lake Dr. John Medina analemba kuti: “Zikukhala ngati pali zizindikiro zina zake zosadziwika bwino zimene zimayamba kugwira ntchito pa nthawi inayake n’kuuza maselo a chamoyo chokhwima msinkhu kuti asiye kugwira ntchito yawo.” Iye ananenanso kuti: “Pali zinthu za m’kati mwa maselo zimene zimatha kuuza maselowo, ngakhalenso chamoyo chonsecho, kuti chikalambe ndi kufa.”

Thupi lathu tingaliyerekezere ndi kampani imene yakhala ikuchita bwino bizinesi yake kwa zaka zambiri. Mwadzidzidzi, mabwana ake akusiya kulemba anthu ntchito ngakhale kuphunzitsa ntchito anthu atsopano, akusiya kukonza makina ndi kugula ena atsopano, ndipo akusiya kukonza ndi kumanganso malo ochitira bizinesiyo. Pasanapite nthawi yaitali, bizinesiyo ingayambe kulowa pansi. Koma kodi n’chifukwa chiyani mabwana onsewo anasintha njira yawo yabwino yochitira bizinesi? Funso limenelo n’lofanana ndi limene akatswiri a sayansi ya zamoyo amene amafufuza za kukalamba akukumana nalo. Buku lakuti The Clock of Ages limati: “Pakafukufuku wa kukalamba, chinthu chimodzi chovuta kwambiri kuchimvetsa ndicho chifukwa chimene maselo amasiyira kugawikana n’kuyamba kufa.”

Kodi Ukalamba Uli ndi Mankhwala?

Kukalamba akuti ndi “chinthu chovuta kwambiri kuchimvetsa pa zinthu zonse zovuta kumvetsa zokhudza zinthu zamoyo.” Patatha zaka zambiri, kafukufuku amene asayansi achita sanapeze chimene chimayambitsa kukalamba, kapena mankhwala a ukalamba. Mu 2004, magazini yotchedwa Scientific American inafalitsa chenjezo lomwe asayansi 51 omwe amaphunzira za kukalamba anapereka. Chenjezolo linati: “Palibe mankhwala alionse amene akugulitsidwa masiku ano, ngakhale ndi amodzi omwe, amene asonyeza kuti amatha kuchedwetsa, kuletsa, kapena kuthetsa kukalamba kwa anthu.” Ngakhale kuti kudya mosamala ndi kuchita zinthu zolimbitsa thupi kukhoza kukuthandizani kuti mukhale ndi thanzi labwino ndi kuti musafe msanga ndi matenda, palibe chimene chasonyeza kuti chimachedwetsa kukalamba. Zimenezi zikutikumbutsa mawu a Yesu opezeka m’Baibulo akuti: “Ndani wa inu ndi kudera nkhawa angathe kuwonjezera pa msinkhu wake mkono umodzi?”—Mateyu 6:27.

Pofotokoza mwachidule zomwe apeza pa ntchito yawo yofuna kupeza mankhwala a ukalamba, Medina analemba kuti: “Sitikudziwa n’komwe kuti n’chifukwa chiyani timakalamba . . . Pambuyo polimbana ndi khansa kwa zaka makumi angapo, sitinapezebe mankhwala ake. Komano zimene zimachitika munthu akamakalamba n’zovuta kwambiri kuzimvetsa poyerekeza ndi zimene zimachitika munthu akamadwala khansa.”

Kafukufuku Watithandiza Kumvetsa Mfundo Yofunika Kwambiri

Kafukufuku wa momwe zamoyo zimagwirira ntchito ndi chifukwa chomwe zimakalambira sanathetseretu chiyembekezo chokhala ndi moyo wautalipo. Ena apeza kuti kafukufuku wawo wawakakamiza kuvomereza mfundo imene ili yofunika kwambiri kuti amvetse zomwe zimayambitsa kukalamba. Katswiri wina wa zimene zimachitika m’maselo a zinthu zamoyo dzina lake Michael Behe analemba kuti: “Pazaka makumi anayi zapitazi sayansi yamakono ya zimene zimachitika m’maselo a zinthu zamoyo yatulukira zinthu zimene kale sizimadziwika. . . . Zotsatirapo za kafukufuku yense amene wachitika wofuna kumvetsa zamoyo poona zomwe zimachitika m’kati mwa maselo, n’zakuti tapeza popanda kukayikira n’komwe kuti zamoyo zinalengedwa ndi winawake.” Alipo winawake amene analenga zinthu zamoyo mwanzeru. Ndipotu, Behe si munthu woyamba kuzindikira zimenezi. Ataganizira mozama za momwe thupi la munthu linapangidwira, wamasalmo wina wakale analemba kuti: “Chipangidwe changa n’choopsa ndi chodabwitsa.”—Salmo 139:14.

Ngati zinthu zonse zamoyo zinachita kulengedwa, pali funso lochititsa chidwi limene limabuka, lakuti, Kodi Mulungu, amene analenga zinthu zonse, analenga anthu kuti akhale ndi moyo wotalika mofanana ndi wa zinyama zambiri, kapena akufuna kuti tikhale ndi moyo wautali kuposa wa zinyama?

[Mawu Otsindika patsamba 6]

‘Tinalengedwa Modabwitsa’

[Chithunzi pamasamba 4, 5]

Kodi timakalamba chifukwa cha kuwonongeka kwa maselo?

[Mawu a Chithunzi patsamba 6]

DNA: Photo: www.comstock.com