Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndiziwerenga Chifukwa Chiyani?

Ndiziwerenga Chifukwa Chiyani?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Ndiziwerenga Chifukwa Chiyani?

“Kuwerenga kumanditopetsa. Bolani kuonera TV.”—Anatero Margarita wa zaka 13, wa ku Russia.

“Ndikati ndisankhe kusewera mpira ndi kuwerenga buku, ndimasankha kusewera mpira.”—Anatero Oscar wa zaka 19, wa ku United States.

NGATI mwawerenga nkhaniyi kufika pano, ndiye kuti mukuzindikira kufunika kowerenga. Komabe, mwina mukaganiza zowerenga buku kapena magazini mumangomva ngati mmene mumamvera mukafuna kumwa mankhwala: Inde, mumadziwa kuti n’zofunika, koma sizikusangalatsani.

Atolankhani a Galamukani! anafunsa achinyamata ochokera m’mayiko 11 kuti anene chifukwa chake kuwerenga kumawavuta ndi phindu limene amapeza akamawerenga. Izi n’zimene ananena.

Kuwerenga kumakuvutani chifukwa chiyani?

“Nthawi zambiri sindipeza nthawi yowerenga.”—Anatero Semsihan wa zaka 19, wa ku Germany.

“Kuwerenga kumafuna khama. Ndikuganiza kuti ndili ndi kaulesi pang’ono.”—Anatero Ezekiel wa zaka 19, wa ku Philippines.

“Ndimadana nazo akamandiumiriza kuwerenga nkhani zosasangalatsa.”—Anatero Christian wa zaka 15, wa ku England.

“Ndimafuna kuwerenga buku likakhala laling’ono. Koma lalikulu limandigwetsa mphwayi.”—Anatero Eriko wa zaka 18, wa ku Japan.

“Sinditha kuika maganizo anga pa chinthu chimodzi. Ndimakonda kutengeka ndi zinthu zina.”—Anatero Francisco wa zaka 13, wa ku South Africa.

Achinyamata achikristu amalimbikitsidwa kuwerenga Baibulo. (Salmo 1:1-3) Kodi zimenezi zimakuvutani? Nanga zimakuvutani chifukwa chiyani?

“Baibulo ndi buku lalikulu kwabasi! Ndikuganiza kuti sindingalimalize ngakhale n’taliwerenga moyo wanga wonse.”—Anatero Anna wa zaka 13, wa ku Russia.

“Mbali zina za Baibulo n’zovuta kuzimva ndipo sizosangalatsa kwenikweni.”—Anatero Jezreel wa zaka 11, wa ku India.

“Zimandivuta kuwerenga Baibulo mosadukizadukiza chifukwa chakuti ndandanda yanga ndi yosalongosoka.”—Anatero Elsa wa zaka 19, wa ku England.

“Ndimakanika kuwerenga Baibulo chifukwa chakuti ntchito za panyumba ndi za kusukulu zimandidyera nthawi yambiri.”—Anatero Zurisadai wa zaka 14, wa ku Mexico.

“Kuwerenga Baibulo kumandivuta chifukwa chakuti zinthu zimene ndimachita panthawi yopuma zimandidyera nthawi yambiri.”—Anatero Sho wa zaka 14, wa ku Japan.

Inde, kuwerenga n’kovuta. Koma kodi n’kofunikira? Kodi kuwerenga kwakuthandizani bwanji?

“Kuwerenga kwandithandiza kudziwa zinthu zambiri, ndipo zimenezi zandithandiza kuti ndisamadzikayikire polankhula ndi anthu.”—Anatero Monisha wa zaka 14, wa ku India.

“Kuwerenga kumandikhazikitsa mtima pansi ndipo kumandithandiza kuti ndileke kuganiza za mavuto anga.”—Anatero Alison wa zaka 17, wa ku Australia.

“Kuwerenga kumanditengera kumalo oti sindikanatha n’komwe kufikako.”—Anatero Duane wa zaka 19, wa ku South Africa.

“Kuwerenga kumandithandiza kuti ndizifufuza zinthu ndekha, m’malo momangodalira kuuzidwa ndi anthu ena.”—Anatero Abihú wa zaka 16, wa ku Mexico.

Kodi n’chiyani chakuthandizani kuti muzikonda kuwerenga?

“Kuyambira ndili wamng’ono makolo anga anandilimbikitsa kuti ndiziwerenga mokweza mawu.”—Anatero Tanya wa zaka 18, wa ku India.

“Makolo anga anandilimbikitsa kuti ndiziganizira zimene ndikuwerengazo, n’kumakhala ngati ndikuona zimene zikuchitika.”—Anatero Daniel wa zaka 18, wa ku England.

“Bambo anga anandiuza kuti ndiyambe ndi mabuku a m’Baibulo amene amandisangalatsa, monga Masalmo ndi Miyambo. N’chifukwa chake masiku ano kuwerenga Baibulo kumandisangalatsa, ndipo sikukhalanso ngati mtolo wolemetsa.”—Anatero Charene wa zaka 16, wa ku South Africa.

“Pamene ndimafika zaka zinayi, makolo anga anali atandipatsa tebulo lowerengera ndi shelefu yodzadza ndi mabuku amene anakhala akundisungira kuyambira n’tangobadwa kumene.”—Anatero Airi wa zaka 14, wa ku Japan.

Kodi n’chifukwa chiyani mukuganiza kuti n’kofunika kuwerenga Baibulo?

“Anthu amakhulupirira zinthu zambiri zokhudza Baibulo zimene sizoona. Ndi bwino kuliwerenga wekha Baibulo kuti ufufuze zinthu zimenezi.” (Machitidwe 17:11)—Anatero Matthew wa zaka 15, wa ku United States.

“Kuwerenga Baibulo kumafuna kuganiza kwambiri, koma kwandithandiza kulankhula mosadzikayikira ndi momveka bwino ndikamauza ena zimene ndimakhulupirira.” (1 Timoteo 4:13)—Anatero Jane wa zaka 19, wa ku England.

“Ndikamawerenga Baibulo, ndimamva ngati kuti Yehova akulankhula nane. Nthawi zina zimandikhudza mtima kwambiri.” (Ahebri 4:12)—Anatero Obadiah wa zaka 15, wa ku India.

“Kuwerenga Baibulo kwayamba kundisangalatsa chifukwa chakuti limandiuza mmene Yehova amandionera ndipo limandipatsa malangizo abwino kwambiri.” (Yesaya 48:17, 18)—Anatero Viktoriya wa zaka 14, wa ku Russia.

Kodi mumawerenga Baibulo ndi mabuku ofotokoza za m’Baibulo nthawi yanji?

“Ndili ndi ndandanda imene ndimatsatira. Ndimawerenga chaputala chimodzi cha m’Baibulo ndikangodzuka m’mamawa uliwonse.”—Anatero Lais wa zaka 17, wa ku Brazil.

“Ndimawerengera Baibulo ndi mabuku ena achikristu m’sitima ndikamapita kusukulu. Ndakhala ndikuchita zimenezi kwa zaka zinayi tsopano.”—Anatero Taichi wa zaka 19, wa ku Japan.

“Ndimawerenga Baibulo pang’ono pokha usiku uliwonse ndisanagone.”—Anatero Maria wa zaka 15, wa ku Russia.

“Ndimawerenga masamba anayi a ‘Nsanja ya Olonda’ kapena a ‘Galamukani!’ tsiku lililonse. Ndimakwanitsa kumaliza kuwerenga magazini iliyonse imene ndalandira, ina isanafike.”—Anatero Eriko wa zaka 18, wa ku Japan.

“Ndimawerenga Baibulo m’mamawa uliwonse ndisanapite kusukulu.”—Anatero James wa zaka 17, wa ku England.

Mogwirizana ndi zimene achinyamatawa ananena, kuwerenga kungakuthandizeni kuti musamadzikayikire ndipo mumadziwa zinthu zambiri. Kuwerenga Baibulo ndi mabuku ofotokoza za m’Baibulo, monga magazini ino, kungakuthandizeni ‘kuyandikira kwa Mulungu.’ (Yakobo 4:8) Choncho, musaleke kuwerenga ngakhale ngati sikukusangalatsani.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Kodi mumafunika kuwerenga Mawu a Mulungu chifukwa chiyani?

▪ Kodi mungatani kuti ‘muwombole nthawi’ yowerenga Baibulo ndi mabuku ofotokoza za m’Baibulo?—Aefeso 5: 15, 16.

[Bokosi patsamba 16]

GWIRIZANITSANI

Gwirizanitsani zimene mukuwerenga ndi zimene mukudziwa kale zokhudza inuyo ndi malo okuzungulirani. Ganizirani izi:

Zimene Mukuwerenga ndi Zimene Munawerenga Kale Kodi nkhaniyi ikufanana ndi zimene ndinawerengapo kale m’mabuku, m’magazini, kapena m’nkhani zina? Kodi anthu a m’nkhaniyi akufanana ndi anthu amene ndinawawerengapo kale?

Zimene Mukuwerenga ndi Inuyo Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi moyo wanga, chikhalidwe changa, mavuto anga? Kodi ingandithandize bwanji kulimbana ndi mavuto anga kapena kusintha moyo wanga?

Zimene Mukuwerenga ndi Malo Okuzungulirani Kodi nkhaniyi ikundiphunzitsa chiyani chokhudza zachilengedwe, malo amene ndikukhala, chikhalidwe cha anthu osiyanasiyana, kapena mavuto amene anthu ali nawo? Kodi nkhaniyi ikundiphunzitsa chiyani chokhudza Mlengi?