Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kumvera Machenjezo Kunawathandiza

Kumvera Machenjezo Kunawathandiza

Kumvera Machenjezo Kunawathandiza

TSIKULO linali Lachitatu, pa August 24, 2005. Linali tsiku lotentha mu mzinda wa New Orleans, m’chigawo cha Louisiana ku United States, monga momwe amakhalira masiku ambiri. Alan ndi banja lake anachoka kunyumba kwawo kupita ku ulendo wa masiku angapo ku Beaumont, m’chigawo cha Texas, womwe unali mtunda wa makilomita 300 kumadzulo. Anatenga zovala zokwanira masiku asanu. Alan anafotokoza kuti: “Sitinkadziwa kalikonse za mphepo yamkuntho yotchedwa Katrina, yomwe panthawi imeneyo inali itayamba kale kum’mawa kwa chigawo cha Florida. Komabe, pofika Lachisanu usiku, zinali zitadziwika kuti mzinda wa New Orleans ukanthidwa ndi mphepo yamkutho yoopsa kwambiri.”

Pofika Lamlungu, pa August 28, zinaonekeratu kuti mphepo yamkuntho yotchedwa Katrina ikhala yamphamvu kwambiri. Meya wa mzinda wa New Orleans analamula kuti aliyense achoke mu mzindawo. Chifukwa cha lamulo limeneli, magalimoto ambirimbiri anayamba kupita kumpoto ndi kumadzulo kwa mzindawu, ndipo misewu inadzaza ndi magalimotowo. Anthu ena ambiri amene analibe magalimoto anathawira ku malo obisalirako kapena ku sitediyamu yaikulu yotchedwa Superdome. Ena sanachoke, ndipo anaganiza kuti akhoza kukhala bwinobwino m’nyumba zawo mpaka mphepo ya mkunthoyo itadutsa.

‘Zikadzachitikanso, Ndidzakhala Woyamba Kuchoka!’

Joe, wa Mboni za Yehova, ndi munthu mmodzi amene sanachoke kunyumba kwake. Iye anali kukhulupirira kuti akhoza kupulumuka bwinobwino mphepo ya mkunthoyo ali m’nyumba mwake. Iye anadzilimbitsa mtima pokumbukira kuti mphepo za mkuntho za m’mbuyomu sizinawononge zinthu kwambiri ngati mmene akuluakulu a boma ananenera. Iye anati: “Ndinkakhulupirira kuti nditha kupulumuka. Koma maganizo anga anasintha mwamsanga. Kunabwera mphepo ndi mvula yoopsa kwambiri. Pasanapite nthawi, denga la nyumba yanga linasasuka. Kenaka madzi anayamba kukwera mwamsanga ndiponso mochititsa mantha kwambiri. Anakwera mamita atatu pa maola atatu. Ankalowa m’nyumbamo mwamsanga kwambiri moti ndinathawira pa nsanja yachiwiri. Ndinachita mantha kwambiri chifukwa mphepoyo inali kuchita chimkokomo ndipo makoma a nyumbayo ankaoneka ngati agwera m’kati nthawi iliyonse. Siling’i inayamba kugwa. Tsopano ndinayamba kuganiza za njira yopulumukira.

“Ndinaganiza kuti mwina ndidumphire m’madzi amene anali kuthamangawo. Koma kunja kunali mafunde oopsa. Mphepo inali kuchititsa mafunde aakuluakulu m’misewu yapafupi. Ndinadziwa kuti ndikadumpha, ndikhoza kumira.”

Patapita nthawi kunabwera bwato limene linadzamupulumutsa Joe n’kumusiya pa mlatho. M’madzimo munkayandama mitembo ya anthu ndipo paliponse panali nyansi zochokera m’zimbudzi. Anagona usiku umodzi pamwamba pa galimoto. Kenaka anadzamutenga pa helikopita yomwe inamupititsa ku basi, yomwe inamutengera ku Civic Center ya ku New Orleans. Iye anati: “Anthu kumeneko anandikomera mtima. Panthawi inayake ndinkachita kulephera kulankhula. Chomwe ndinali kuganizira kwambiri panthawi imeneyo chinali choti, ‘Kaya madzi akumwa ndiapeza kuti?’”

Poyang’ana m’mbuyo, Joe anazindikira kuti akanatha kupewa mavuto akewo. Iye anati: “Zimenezi zandiphunzitsa kanthu. Akadzanenanso kuti ‘Chokani,’ ndidzakhala woyamba kuchoka!”

Sanamvere Machenjezo, Kenako Anathawira Mumtengo

Mizinda ya Biloxi ndi Gulfport, m’mphepete mwa mtsinje wa Mississippi, inasakazidwa koopsa ndipo anthu ambiri anafa. Malinga ndi zimene inanena nyuzipepala ya The New York Times ya pa August 31, 2005, Vincent Creel, mkulu womva za madandaulo a anthu mu mzinda wa Biloxi, anati: “Anthu ambiri sanamvere lamulo loti achoke chifukwa iwowo, kapena nyumba zawo, zinapulumuka ku mphepo ya mkuntho yotchedwa Camille [ya mu 1969].” Mphepo ya mkuntho ya Camille akuti mwina inali yamphamvu kwambiri kuposa ya Katrina, koma, monga momwe Creel ananenera, mphepo ya mkuntho ya Katrina ‘inabweretsa chiphiri chachikulu cha madzi chosaimitsika chimene chinali chofanana ndi tsunami.’

Munthu wina wokhala m’derali amene ananyalanyaza machenjezo ndi Inell, amene wakhala ku Biloxi pafupifupi moyo wake wonse. Iye anati: “Tinapulumuka mphepo za mkuntho zambiri m’mbuyomu. Choncho sindinkachita mantha kwambiri ndi Katrina.” Inell atakatenga apongozi ake aakazi a zaka 88, mwana wake wamwamuna, mwana wake wamkazi, ndi mpongozi wake wamwamuna, limodzi ndi agalu awiri ndi amphaka atatu, anaganiza zoti asachoke m’nyumba yawo, imene inali yomangidwa bwino. Kenaka mphepo ya mkunthoyo inafika ku Biloxi cha m’ma 10 koloko m’mawa pa August 29. Inell akukumbukira kuti: “Ndinaona madzi akulowa m’chipinda chimodzi chogona kufupi ndi kumbuyo kwa nyumbayo. Kenaka anayamba kulowa paliponse. Tinakwera ku kachipinda kapamwamba kakang’ono kosungira katundu kuti tipulumuke. Koma madziwo sanasiye kukwera. Tinafunika kuchoka m’kachipindako kuti madziwo asatitsekereze. Koma kodi tikadapita kuti?

“Mwana wanga wamwamuna anachita kung’amba sefa ya pawindo kuti tithe kutuluka m’kachipindako. Atatero tinasambira n’kufika pamwamba pa madziwo panja. Kenaka tinatha kuyandama pogwira m’mphepete mwa denga. Anthu atatu anapita kumanja kwa nyumbayo, ndipo mwana wanga wamkazi anapita kumanzere. Ndinaona mtengo waukulu chapafupi. Ineyo, mwana wanga wamwamuna, ndi apongozi anga aakazi tinasambira n’kupita pa mtengowo n’kuugwira zolimba. Kenaka ndinamva mwana wanga wamkazi akukuwa kuti, “Amayi! Amayi!” Mpongozi wanga wamwamuna, amene anali womaliza kutuluka m’kachipinda kaja, anasambira n’kupita kukamupulumutsa. Awiriwo anakwanitsa kufika pa bwato limene linaimikidwa pakanjira kokhotera kunyumba kwathuko ndipo linali kuyandama pafupi ndi nyumbayo. Anandipempha kuti ndikwere m’bwatolo. Sindinafune kupita chifukwa choopa madzi amene anali kuthamanga kwambiri motizungulira. Ndinaona kuti ndinaliko bwino mumtengomo, ndipo sindinafune kuusiya.

“Kuchokera mumtengomo, ndinatha kuona madziwo akuyenda mumsewu ndiponso kuzungulira nyumba yathu yonse. Ndinayamba kuganizira zomwe zinatichitikirazi ndipo ndinaona kuti ndinachita zopusa posamvera machenjezo oti tichoke.

“Patapita nthawi, madziwo anayamba kuphwera, ndipo kenaka tonse tinakwera bwato lija. Kunabwera galimoto yozimitsa moto ndipo inatitenga n’kutipititsa kuchipatala. Tinali oyamikira kwambiri kuti tinali ndi moyo!”

Zimene Mboni Zinakonza Kuti Zipulumutse Anthu

Katrina anawononga zinthu m’mizinda yomwe ili ku gombe la Gulf Coast, kumene nyumba zambiri zinawonongeka kuchokera ku Louisiana kulowera chakum’mawa kufika ku Alabama. Koma ku dera limeneli la ku United States, mphepo za mkuntho si zachilendo. Choncho Mboni za Yehova zinakonzeratu njira zopulumutsira anthu zomwe zakhalapo kwa zaka zingapo. Chaka chilichonse, makamaka mu June, nyengo ya mphepo za mkuntho isanayambe, mipingo 21 ya Mboni za Yehova m’madera ozungulira mzinda wa New Orleans imakambirananso zomwe angachite ngati atafunika kuchoka mwadzidzidzi. Choncho, Mboni zambiri kumeneku zinkadziwa zomwe ziyenera kuchita ngati patagwa zinazake zadzidzidzi. Kodi njira zimene anakonzazi zinagwira ntchito bwanji kutabwera mphepo ya mkuntho ya Katrina?

Akuluakulu a mzindawo atalengeza zoti anthu ayenera kuchoka, akulu mu mpingo uliwonse analankhulana ndi anthu a m’mipingo mwawo n’kuwalimbikitsa kuti achoke mu mzindawo. Ambiri anatha kukonza mmene angachokere ndi achibale awo ndi anzawo. Anakonza thiransipoti yapadera yoti itenge anthu okalamba ndi odwala. John, mmodzi wa anthu a m’komiti ya Mboni yothandiza pakagwa tsoka, anati, “Ndikukhulupirira kuti potsatira njira imeneyi, tinapulumutsa miyoyo yambiri.” Choncho Mboni za Yehova zambiri zinatha kuchoka mumzindawo mphepo ya mkunthoyo isanayambe. Kuti athandize anthu amene anali kufunikira chithandizo m’madera amene anakhudzidwawo, a ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku United States anakonza makomiti opereka chithandizo.

Kufunafuna Mboni mu Sitediyamu ya Astrodome

Anthu pafupifupi 16,000 othawa kwawo, makamaka ochokera ku chigawo cha Louisiana, anali kulandira chakudya, madzi, ndiponso kugona mu sitediyamu ya Astrodome mu mzinda wa Houston, m’chigawo cha Texas. Anthu a m’komiti yopereka chithandizo ku Houston anamva zoti Mboni zina zinali m’chikhamu cha anthucho. Koma kodi akanazipeza bwanji?

M’mawa Lachisanu, pa September 2, gulu la akulu a Mboni linafika ku Astrodome kuti lifunefune abale awo omwe anachoka m’nyumba zawowo. Anadabwa kwambiri kuona amuna, akazi, achinyamata, ana, ndi makanda ambirimbiri amene anali paliponse m’sitediyamu yaikuluyo. Pabwalo losewerera mpira panali zikuku za ana mbwee! komanso panali anthu othawa kwawo amene anali kudikirira modekha kuti apeze njira yothetsera mavuto awo. Panali mizera italiitali ya anthu ofuna chithandizo cha mankhwala, ndipo antchito achipatala anali kuthamanga kuti atengere odwala ku maambulansi.

Samuel, mmodzi mwa akulu amene ankafunafuna Mboni zinzawo, anati: “Ndinamva ngati ndili pakati pa msasa wa anthu othawa kwawo.” Kodi akanatha bwanji kupeza Mboni zowerengeka m’chigulu cha anthuchi? Akuluwo anayamba n’kuyenda m’mizere ya anthuwo atanyamula zimapepala zikuluzikulu zouza Mbonizo kuti zinene pomwe zili. Atafufuza kwa maola atatu osaphula kanthu, anazindikira kuti akufunika kupeza njira ina yofufuzira. Anapempha a bungwe la Red Cross kuti alengeze pa zokuzira mawu zawo kuti: “Onse amene ali Mboni za Yehova zobatizidwa, apite pa malo otsika a kum’mawa kwa sitediyamuyi pansanjika yapansi.”

Kenaka, Mboni zinayamba kubwera pang’onopang’ono zikumwetulira. Samuel anafotokoza kuti: “Anali ndi misozi m’maso mwawo ndipo anali ndi chimwemwe chodzaza tsaya potiona. Anatikupatira mwamphamvu n’kutigwira manja. Sankafuna kutisiya poopa kuti angasowe m’chikhamu cha anthucho.” Lachisanu ndi Loweruka, anapeza Mboni 24 ndipo anazitengera ku malo operekera chithandizo a Mboni.

Ambiri a iwo analibe katundu aliyense kupatulapo zovala zakuda zomwe anavalazo basi. Mboni ina inanyamula kabokosi kakang’ono. Munali mapepala ena ofunika, ndipo katundu yense amene anatha kupulumutsa ku mphepo ya mkunthoyo anali ameneyu.

Ku sitediyamu ya Astrodome, anthu ambiri anawazindikira akuluwo kuti ndi atumiki a Mboni za Yehova ndipo anabwera kudzalankhula nawo. Anawapempha Mabaibulo ndi mabuku ofotokoza za m’Baibulo. Anapempha Mabaibulo oposa 220. Mbonizo zinapatsanso anthu magazini ya Galamukani! ya August 8, 2005, yomwe inali ndi nkhani zapanthawi yake zoyankha funso lakuti, “Kodi Masoka Akuwonjezeka?”

Ena Abwerera Kwawo

Munthu mmodzi amene anapulumuka pa mphepo ya mkunthoyo ndi mtolankhani ndiponso bwana wamkulu wa pa siteshoni ina ya TV ku New Orleans yemwe wagwira ntchito imeneyi kwa zaka zambiri. Choncho, waonapo zinthu zambirimbiri zitawonongeka m’mbuyomu. Iye anabwerera ku nyumba kwake ku Jefferson Parish, m’chigawo cha Louisiana, kuti akatenge zinthu zina zofunikira. Iye anati: “Sindinakhulupirire zomwe ndinaona. Zinthu zinawonongeka koopsa, osatsala kalikonse. Pa TV tinaona madzi amene anasefukira chifukwa cha kugumuka kwa migula ndiponso amene anasefukira kuchokera m’ngalande. Koma mphepo yamphamvuyo inawononganso zinthu zambiri. Mdadada wa nyumba umene munali nyumba yanga unawonongekeratu. Panopa kuli nkhungu, zinthu zowola, ndi fungo loipa. Fungo lake n’lonunkha koopsa. N’zoipa kwambiri, zoipa zedi. Tikungoyamika kuti tili moyo.”

Alan, amene tinamutchula koyambirira kuja, patapita nthawi anabwerera kunyumba kwawo ku Metairie, yomwe ndi tawuni ina yakum’mwera kwa mzinda wa New Orleans. Mphepo ya mkunthoyo inawononga zinthu koopsa. Iye anati: “Zomwe ndinaona zinali zosakhulupirika, zoopsa kwambiri. Zinaoneka ngati kuti bomba laphulitsidwa mumzindawu kuchokera kumwamba. Kumva zimenezi pa nkhani zapawailesi kapena kuzionerera pa TV n’kosiyana kwambiri ndi kuyenda pansi kapena kuyendetsa galimoto m’dera lanu ndi kuona ndi maso anu mmene zinthu zambirimbiri zawonongekera. N’zovuta kwambiri kukhulupirira kuti zimenezi zachitikadi.

“Mwachitsanzo, fungo limene linali kutuluka pamenepo linali loipa kwambiri. Panali kununkha ngati mnofu woola, ngati fungo la munthu wakufa. Malo ambiri amabizinesi anawonongeka kapena kumizidwa ndi madzi osefukira. Apolisi ndi asilikali anali paliponse. Kunkaoneka ngati kunkhondo.”

Thandizo Limene Ena Anapereka

Akuluakulu a mzindawo, a chigawocho, ndi a boma anakhazikitsa mabungwe othandiza anthu. Bungwe limene linkathandiza anthu kwambiri linali la FEMA (Federal Emergency Management Agency). Mabungwe enanso anayesetsa kuthandiza anthu ambirimbiri amene ankafunikira thandizo. M’dera lomwe linakanthidwa ndi mphepo ya mkuntholo munabwera chakudya, zovala, ndi madzi ambirimbiri pamagalimoto akuluakulu. Pasanapite nthawi yaitali bungwe la FEMA linayamba kupereka macheke kwa anthu ndi chithandizo china cha ndalama kuti athe kupeza poyambira kwa masiku ndi milungu ingapo yoyambirira. Koma kodi panthawi imeneyi Mboni za Yehova zinali bwanji?

Kuona Zowonongeka ndi Kuzikonza

Mphepo ya mkunthoyo itangoyamba, Mbonizo zinapanga magulu a anthu oti apite akaone momwe nyumba zogona ndi Nyumba za Ufumu zawonongekera m’deralo. Kodi akanakwanitsa bwanji kugwira chintchito chachikulu ngati chimenecho? Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ku Brooklyn, mu mzinda wa New York, linapereka chilolezo choti makomiti othandiza anthu akhazikitsidwe moyang’aniridwa ndi Komiti ya Nthambi ya ku United States. Komanso, Makomiti Omanga Achigawo ochokera ku mbali zosiyanasiyana za dziko la United States anaitanidwa kuti ayambe ntchito yokonzanso nyumba zowonongeka. * Kodi achita zotani?

Pofika pa February 17, 2006, gulu lopereka chithandizo la ku Long Beach, ku Mississippi, linanena kuti m’dera lawo, pa nyumba 632 za Mboni zimene zinawonongeka, 531 anali atamaliza kuzikonzanso, kutanthauza kuti patsala nyumba 101 zimene zikufunika kuti azikonze. Mbonizo zinathandizanso anthu okhala pafupi omwe si Mboni. Nyumba za Ufumu 17 zinawonongeka kwambiri madenga, ndipo pofika pakati pa mwezi wa February, madenga atsopano anali ataikidwa pa Nyumba za Ufumu 16. Nanga bwanji za komiti ya ku Baton Rouge, m’chigawo cha Louisiana?

Gulu limeneli limasamalira dera la Louisiana, lomwe linasakazidwa kwambiri ndi mphepo ya mkuntho ya Katrina. Pa nyumba 2,700 za Mboni zomwe zikufunika kukonzedwa kumeneko, anali atamaliza kukonza nyumba 1,119 pofika pakati pa February, choncho gulu limeneli linali likadali ndi chintchito chachikulu choti ligwire. Ukunso, anthu okhala pafupi ndi achibale a Mboni amene amafunikira thandizo kwambiri anathandizidwanso. Nyumba za Ufumu 50 zinawonongeka kwambiri. Pofika mu February, 25 mwa zimenezi zinali zitakonzedwa. Ku Texas, gulu la ku Houston linafunika kukonza nyumba 871 zomwe zinawonongedwa ndi mphepo ya mkuntho yotchedwa Rita mu September. Pofika pa February 20, 830 zinali zitakonzedwa.

Zimene Katrina Anatiphunzitsa

Anthu ambiri amene anavutika ndi mphepo ya mkuntho ya Katrina aphunzira phunziro lofunika kwambiri loti kumvera machenjezo kumapulumutsa moyo. Zoonadi, anthu ambiri angavomerezane ndi Joe, yemwe tinamutchula kale uja, yemwe anati: “Akadzanenanso kuti ‘Chokani,’ ndidzakhala woyamba kuchoka!”

Mboni za Yehova zikupitirizabe kuthandiza anthu amene anavutika ndi mphepo ya mkunthoyi m’dera lakugombeli. (Agalatiya 6:10) Komabe, utumiki wawo siwongopatsa anthu chithandizo chakuthupi ayi. M’malo mwake, ntchito yaikulu ya Mboni za Yehova, yomwe ikuchitika m’mayiko 235 padziko lonse lapansi, ndiyo kuchenjeza anthu kuti athawe zinthu zoopsa kwambiri kuposa mphepo ya mkuntho. Baibulo linaneneratu kuti Mulungu posachedwapa adzathetsa dongosolo la zinthu losaopa Mulunguli, n’kuyeretsa dziko lathuli n’kulibwezeretsa mwakale kuti likhale ngati mmene iye anafunira. Ngati mukufuna kudziwa zomwe Baibulo limaphunzitsa zokhudza nthawi ya chiweruzo imeneyi, lankhulani ndi Mboni za Yehova m’dera lanu kapena lembani kalata ku adiresi yoyenerera yomwe ili pa tsamba 5 la magazini ino.—Marko 13:10; 2 Timoteo 3:1-5; Chivumbulutso 14:6, 7; 16:14-16.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 32 Makomiti Omanga Achigawo amapangidwa ndi magulu a Mboni za Yehova a anthu ongodzipereka amene agwira ntchito yomanga ndi kukonzanso Nyumba za Ufumu kwa nthawi yaitali. Pali magulu pafupifupi 100 oterewa ku United States komanso pali ena ambiri padziko lonse lapansi.

[Chithunzi pamasamba 14, 15]

Chithunzi chojambulidwa kuchokera m’mwamba choonetsa m’kati mwa mphepo ya mkuntho ya Katrina

[Mawu a Chithunzi]

NOAA

[Chithunzi patsamba 15]

Mzinda wa New Orleans utasefukira madzi

[Mawu a Chithunzi]

AP Photo/​David J. Phillip

[Chithunzi patsamba 15]

Mphepo ya Katrina inawononga nyumba ndi kupha anthu ambiri

[Mawu a Chithunzi]

AP Photo/​Ben Sklar

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Anthu othawa kwawo okwana pafupifupi 16,000 anathawira m’sitediyamu ya Astrodome ku Houston, m’chigawo cha Texas

[Zithunzi patsamba 17]

Akulu achikristu anafunafuna Mboni pakati pa anthu othawa kwawowo

[Chithunzi patsamba 18]

Mboni zinathokoza kwambiri chifukwa chozikonzera nyumba

[Chithunzi patsamba 18]

Anthu ongodzipereka akukonza denga lowonongeka kwambiri

[Chithunzi patsamba 18]

Anthu ongodzipereka anagawa chakudya

[Chithunzi patsamba 19]

Alan